Lolemba, September 1
Kuwala kwam’mawa kudzatifikira kuchokera kumwamba.—Luka 1:78.
Mulungu wapatsa Yesu mphamvu zothetsa mavuto onse a anthu. Pochita zozizwitsa, Yesu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zothetsera mavuto omwe sitingathe kuwathetsa patokha. Mwachitsanzo, iye ali ndi mphamvu yotipulumutsa ku zimene zinayambitsa mavuto a anthu, zomwe ndi uchimo umene tinatengera komanso zotsatirapo zake monga matenda ndi imfa. (Mat. 9:1-6; Aroma 5:12, 18, 19) Zozizwitsa zomwe anachita, zimasonyeza kuti iye angathe kuchiritsa “matenda amtundu uliwonse” ngakhalenso kuukitsa akufa. (Mat. 4:23; Yoh. 11:43, 44) Alinso ndi mphamvu yotha kuletsa mphepo zamkuntho komanso kugonjetsa mizimu yoipa. (Maliko 4:37-39; Luka 8:2) N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova wapatsa Mwana wake mphamvu zochitira zimenezi. Sitikayikira kuti malonjezo omwe tikuyembekezera mu Ufumu wa Mulungu adzakwaniritsidwa. Zozizwitsa zimene Yesu anachita ali munthu padzikoli, zimatiphunzitsa kuti monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzachita zambiri m’tsogolomu. w23.04 3 ¶5-7
Lachiwiri, September 2
Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.—1 Akor. 2:10.
N’kutheka kuti abale ndi alongo ambiri amakonda kuyankha pamisonkhano moti nthawi zambiri mukakweza dzanja sakulozani. Choncho mungaganize kuti bola kungosiya kuyankha. Koma simuyenera kusiya kuyesetsa kuti muyankhe pamisonkhano. Mungachite bwino kumakonzekera ndemanga zingapo pamsonkhano uliwonse. Choncho ngati simunalozedwe kuti muyankhe kumayambiriro kwa phunziro, mungakhalebe ndi mwayi woyankha mkati mwa misonkhanoyo. Mukamakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, muziganizira mmene ndime iliyonse ikugwirizanirana ndi mutu wa nkhaniyo. Mukamachita zimenezo mungakhale ndi mfundo zoti muyankhe m’phunziro lonselo. Mungakonzekere kuti mukayankhe pa ndime zimene zikufotokoza mfundo zozama za choonadi, zomwe ndi zovuta kuzifotokoza. Chifukwa chiyani? Chifukwa mwina pangakhale anthu ochepa oimika manja kuti ayankhe pa mbali imeneyi. Koma bwanji ngati pamisonkhano ingapo mwaonabe kuti simunapatsidwe mwayi woyankha? Misonkhano isanayambe mungauze amene akuchititsa phunzirolo funso limene mukufuna kuyankha. w23.04 21-22 ¶9-10
Lachitatu, September 3
Yosefe anadzuka n’kuchita mogwirizana ndi zimene mngelo wa Yehova anamuuza. Anatenga mkazi wake n’kupita naye kunyumba.—Mat. 1:24.
Yosefe ankakhala wokonzeka kutsatira malangizo a Yehova ndipo izi zinachititsa kuti akhale mwamuna wabwino. Pa nthawi zosachepera zitatu, analandira malangizo ochokera kwa Mulungu okhudza banja lake. Pa nthawi zonsezi ankamvera ndi mtima wonse, ngakhale pamene zinali zovuta kutero. (Mat. 1:20, 24; 2:13-15, 19-21) Chifukwa chotsatira malangizo a Mulungu, Yosefe anateteza, kuthandiza komanso kusamalira Mariya. Taganizirani mmene zochita za Yosefe zinathandizira Mariya kuti azimukonda komanso azimulemekeza kwambiri. Amuna, mungatsanzire Yosefe pofufuza ndi kutsatira malangizo a m’Baibulo okhudza mmene mungasamalire banja lanu. Mukamatsatira malangizowa, ngakhale kuti mungafunike kusintha zinthu zina, mumasonyeza kuti mumakonda mkazi wanu komanso mumalimbitsa banja lanu. Mlongo wina wa ku Vanuatu, yemwe wakhala pabanja kwa zaka zoposa 20, anati: “Mwamuna wanga akamafufuza komanso kutsatira malangizo a Yehova, ndimamulemekeza kwambiri. Ndimadzimva kukhala wotetezeka komanso sindikayikira zimene wasankha.” w23.05 21 ¶5