Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lachiwiri, September 2

Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.—1 Akor. 2:10.

N’kutheka kuti abale ndi alongo ambiri amakonda kuyankha pamisonkhano moti nthawi zambiri mukakweza dzanja sakulozani. Choncho mungaganize kuti bola kungosiya kuyankha. Koma simuyenera kusiya kuyesetsa kuti muyankhe pamisonkhano. Mungachite bwino kumakonzekera ndemanga zingapo pamsonkhano uliwonse. Choncho ngati simunalozedwe kuti muyankhe kumayambiriro kwa phunziro, mungakhalebe ndi mwayi woyankha mkati mwa misonkhanoyo. Mukamakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, muziganizira mmene ndime iliyonse ikugwirizanirana ndi mutu wa nkhaniyo. Mukamachita zimenezo mungakhale ndi mfundo zoti muyankhe m’phunziro lonselo. Mungakonzekere kuti mukayankhe pa ndime zimene zikufotokoza mfundo zozama za choonadi, zomwe ndi zovuta kuzifotokoza. Chifukwa chiyani? Chifukwa mwina pangakhale anthu ochepa oimika manja kuti ayankhe pa mbali imeneyi. Koma bwanji ngati pamisonkhano ingapo mwaonabe kuti simunapatsidwe mwayi woyankha? Misonkhano isanayambe mungauze amene akuchititsa phunzirolo funso limene mukufuna kuyankha. w23.04 21-22 ¶9-10

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachitatu, September 3

Yosefe anadzuka n’kuchita mogwirizana ndi zimene mngelo wa Yehova anamuuza. Anatenga mkazi wake n’kupita naye kunyumba.​—Mat. 1:24.

Yosefe ankakhala wokonzeka kutsatira malangizo a Yehova ndipo izi zinachititsa kuti akhale mwamuna wabwino. Pa nthawi zosachepera zitatu, analandira malangizo ochokera kwa Mulungu okhudza banja lake. Pa nthawi zonsezi ankamvera ndi mtima wonse, ngakhale pamene zinali zovuta kutero. (Mat. 1:20, 24; 2:13-15, 19-21) Chifukwa chotsatira malangizo a Mulungu, Yosefe anateteza, kuthandiza komanso kusamalira Mariya. Taganizirani mmene zochita za Yosefe zinathandizira Mariya kuti azimukonda komanso azimulemekeza kwambiri. Amuna, mungatsanzire Yosefe pofufuza ndi kutsatira malangizo a m’Baibulo okhudza mmene mungasamalire banja lanu. Mukamatsatira malangizowa, ngakhale kuti mungafunike kusintha zinthu zina, mumasonyeza kuti mumakonda mkazi wanu komanso mumalimbitsa banja lanu. Mlongo wina wa ku Vanuatu, yemwe wakhala pabanja kwa zaka zoposa 20, anati: “Mwamuna wanga akamafufuza komanso kutsatira malangizo a Yehova, ndimamulemekeza kwambiri. Ndimadzimva kukhala wotetezeka komanso sindikayikira zimene wasankha.” w23.05 21 ¶5

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachinayi, September 4

Kumeneko kudzakhala msewu waukulu. Inde msewu umene udzatchedwe Msewu Wopatulika.​—Yes. 35:8.

Ayuda obwerera kwawo kuchokera ku Babulo akanakhala “anthu oyera” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe zimenezi sizinkatanthauza kuti iwo sankafunika kusintha zinthu zina kuti azisangalatsa Yehova. Ambiri mwa Ayuda omwe anabadwira ku Babulo ankatsatira kaganizidwe ndi mfundo za anthu akumeneko. Patapita zaka zambiri kuchokera pamene Ayuda oyambirira anabwerera ku Isiraeli, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa atapeza kuti ana ena omwe anabadwira ku Isiraeli, sankadziwa chilankhulo cha Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Kodi ana amenewa akanaphunzira bwanji kukonda komanso kulambira Yehova ngati sankadziwa Chiheberi, chilankhulo chomwe chinagwiritsidwa ntchito polemba Mawu a Mulungu? (Ezara 10:3, 44) Choncho panali zinthu zambiri zomwe Ayuda ankafunika kusintha. Koma zikanakhala zosavuta kusintha ngati akanakhala ku Isiraeli kumene kulambira koona kunkabwezeretsedwa pang’onopang’ono.—Neh. 8:8, 9. w23.05 15 ¶6-7

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena