Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
Chilengezo
Chinenero chatsopano chomwe chilipo: Romany (Meçkar)
  • Lero

Lachinayi, September 4

Kumeneko kudzakhala msewu waukulu. Inde msewu umene udzatchedwe Msewu Wopatulika.​—Yes. 35:8.

Ayuda obwerera kwawo kuchokera ku Babulo akanakhala “anthu oyera” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe zimenezi sizinkatanthauza kuti iwo sankafunika kusintha zinthu zina kuti azisangalatsa Yehova. Ambiri mwa Ayuda omwe anabadwira ku Babulo ankatsatira kaganizidwe ndi mfundo za anthu akumeneko. Patapita zaka zambiri kuchokera pamene Ayuda oyambirira anabwerera ku Isiraeli, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa atapeza kuti ana ena omwe anabadwira ku Isiraeli, sankadziwa chilankhulo cha Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Kodi ana amenewa akanaphunzira bwanji kukonda komanso kulambira Yehova ngati sankadziwa Chiheberi, chilankhulo chomwe chinagwiritsidwa ntchito polemba Mawu a Mulungu? (Ezara 10:3, 44) Choncho panali zinthu zambiri zomwe Ayuda ankafunika kusintha. Koma zikanakhala zosavuta kusintha ngati akanakhala ku Isiraeli kumene kulambira koona kunkabwezeretsedwa pang’onopang’ono.—Neh. 8:8, 9. w23.05 15 ¶6-7

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachisanu, September 5

Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pang’ono kugwa ndipo amadzutsa onse amene awerama chifukwa cha mavuto.​—Sal. 145:14.

Ngakhale titayesetsa kukhala odziletsa kapena kukhala ndi mtima wofunitsitsa, tingakumanebe ndi zolepheretsa. Mwachitsanzo, “zinthu zosayembekezereka” zingatiwonongere nthawi yomwe timafunika kukwaniritsa cholinga chathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane ndi vuto lomwe lingachititse kuti tifooke komanso tisakhale ndi mphamvu. (Miy. 24:10) Popeza ndife ochimwa, nthawi zina tingachite zinthu zimene sizingatithandize kukwaniritsa cholinga chathu. (Aroma 7:23) Kapenanso mwina tingamadzimve kuti tatopa. (Mat. 26:43) Ndiye n’chiyani chingatithandize tikakumana ndi zolepheretsa? Tizikumbukira kuti tikakumana ndi zolepheretsa sizitanthauza kuti ndife olephera. Baibulo limanena kuti tingakumane ndi mavuto mobwerezabwereza. Komabe limafotokoza momveka bwino kuti tingathe kukwaniritsa cholinga chathu.. Mukamayesetsa kuti mukwaniritse zolinga zanu ngakhale pali zolepheretsa, mumamusonyeza Yehova kuti mukufuna kumamusangalatsa. Iye amasangalala akaona kuti mukupitirizabe kuyesetsa kukwaniritsa cholinga chanu. w23.05 30 ¶14-15

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Loweruka, September 6

Muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.—1 Pet. 5:3.

Upainiya umathandiza wachinyamata kuti azitha kugwira bwino ntchito ndi anthu osiyanasiyana. Umathandizanso munthu kuti azipanga bajeti yabwino n’kumaitsatira. (Afil. 4:11-13) Upainiya wothandiza ndi poyambira pabwino kuti munthu achite utumiki wa nthawi zonse ndipo ungamuthandize kuti akonzekere kudzachita upainiya wokhazikika. Upainiya umapatsa munthu mwayi wochita mautumiki wosiyanasiyana a nthawi zonse, monga kugwira nawo ntchito zomangamanga kapena kutumikira pa Beteli. Amuna a Chikhristu ayenera kukhala ndi cholinga choti ayenerere kutumikira abale ndi alongo awo mumpingo ngati akulu. Baibulo limanena kuti amuna amene akuyesetsa kuti akhale ndi udindo umenewu “akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Choyamba, m’bale amafunika akhale kaye mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njira zambiri. Akulu ndi atumiki othandiza amatumikira abale ndi alongo awo modzichepetsa ndiponso amagwira nawo ntchito yolalikira mwakhama. w23.12 28 ¶14-16

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena