Lachisanu, September 5
Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pang’ono kugwa ndipo amadzutsa onse amene awerama chifukwa cha mavuto.—Sal. 145:14.
Ngakhale titayesetsa kukhala odziletsa kapena kukhala ndi mtima wofunitsitsa, tingakumanebe ndi zolepheretsa. Mwachitsanzo, “zinthu zosayembekezereka” zingatiwonongere nthawi yomwe timafunika kukwaniritsa cholinga chathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane ndi vuto lomwe lingachititse kuti tifooke komanso tisakhale ndi mphamvu. (Miy. 24:10) Popeza ndife ochimwa, nthawi zina tingachite zinthu zimene sizingatithandize kukwaniritsa cholinga chathu. (Aroma 7:23) Kapenanso mwina tingamadzimve kuti tatopa. (Mat. 26:43) Ndiye n’chiyani chingatithandize tikakumana ndi zolepheretsa? Tizikumbukira kuti tikakumana ndi zolepheretsa sizitanthauza kuti ndife olephera. Baibulo limanena kuti tingakumane ndi mavuto mobwerezabwereza. Komabe limafotokoza momveka bwino kuti tingathe kukwaniritsa cholinga chathu.. Mukamayesetsa kuti mukwaniritse zolinga zanu ngakhale pali zolepheretsa, mumamusonyeza Yehova kuti mukufuna kumamusangalatsa. Iye amasangalala akaona kuti mukupitirizabe kuyesetsa kukwaniritsa cholinga chanu. w23.05 30 ¶14-15
Loweruka, September 6
Muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.—1 Pet. 5:3.
Upainiya umathandiza wachinyamata kuti azitha kugwira bwino ntchito ndi anthu osiyanasiyana. Umathandizanso munthu kuti azipanga bajeti yabwino n’kumaitsatira. (Afil. 4:11-13) Upainiya wothandiza ndi poyambira pabwino kuti munthu achite utumiki wa nthawi zonse ndipo ungamuthandize kuti akonzekere kudzachita upainiya wokhazikika. Upainiya umapatsa munthu mwayi wochita mautumiki wosiyanasiyana a nthawi zonse, monga kugwira nawo ntchito zomangamanga kapena kutumikira pa Beteli. Amuna a Chikhristu ayenera kukhala ndi cholinga choti ayenerere kutumikira abale ndi alongo awo mumpingo ngati akulu. Baibulo limanena kuti amuna amene akuyesetsa kuti akhale ndi udindo umenewu “akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Choyamba, m’bale amafunika akhale kaye mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njira zambiri. Akulu ndi atumiki othandiza amatumikira abale ndi alongo awo modzichepetsa ndiponso amagwira nawo ntchito yolalikira mwakhama. w23.12 28 ¶14-16
Lamlungu, September 7
Akadali mnyamata, Yosiya anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake.—2 Mbiri 34:3.
Mfumu Yosiya anayamba kufunafuna Yehova ali wachinyamata. Ankafuna kuphunzira za Yehova n’kumachita chifuniro chake. Komabe zinthu sizinali zophweka kwa mfumu yachinyamatayi. Iye ankafunika kusankha kukhala kumbali ya kulambira koona pa nthawi imene anthu ambiri ankalambira milungu yabodza. Ndipo iye anachitadi zimenezo. Asanakwanitse zaka 20, Yosiya anayamba kuthetsa kulambira kwabodza. (2 Mbiri 34:1, 2) Ngakhale kuti ndinu wamng’ono mungathe kusankha kuti muzitsanzira Yosiya pofunafuna Yehova komanso kuphunzira makhalidwe ake. Kuchita zimenezi kudzakulimbikitsani kuti mudzipereke kwa iye. Kodi kudzipereka kumeneko kudzakhudza bwanji moyo wanu? Luke yemwe anabatizidwa ali ndi zaka 14 ananena kuti, “Kuyambira tsopano, ndiziika kutumikira Yehova pamalo oyamba ndipo ndiziyesetsa kuti ndizimusangalatsa.” (Maliko 12:30) Ngati inunso mutachita zimenezi Yehova adzakudalitsani. w23.09 11 ¶12-13