7 “Dama,” Kugonana Kosaloleka kwa Mtundu Uliwonse
Mt 5:32—Chigiriki, πορνεία (por·neiʹa); Chilatini, for·ni·caʹti·o
Mawu achigiriki akuti por·neiʹa (poneya) amatanthauza zambiri. Buku lolembedwa ndi Bauer patsamba 693, pofotokoza mawu akuti por·neiʹa limati mawuwa amatanthauza “uhule, kusadzisunga, dama, kugonana kosaloleka kwa mtundu uliwonse.”
Pothirira ndemanga mawu a Yesu a pa Mt 5:32 ndi 19:9, mtanthauzira mawu wotchedwa TDNT, Vol. VI, tsa. 592, amati “πορνεία [por·neiʹa] amatanthauza munthu amene ali pa banja akagonana ndi munthu amene si mwamuna wake kapena mkazi wake.” Choncho, Malemba amagwiritsa ntchito mawu akuti por·neiʹa ponena za anthu amene ali pa banja. Mtanthauzira mawu ameneyu, patsamba 594, ponena za Aef. 5:3, 5, amati Paulo “anazindikira kuti si onse amene ali ndi mphatso ya kudziletsa, 1Ak 7:7. Kuti apewe tchimo la dama, munthu [amene sali pa banja] amene sangathe [kudziletsa] atsatire njira yoikidwa ndi Mulungu yomanga ukwati wovomerezeka, 1Ak 7:2.” Choncho, Malemba amagwiritsanso ntchito mawu akuti por·neiʹa ponena za anthu amene sali pa banja amene amagonana, zomwe ndi zinthu zosaloleka, kapena amene amachita zinthu zosayenera zokhudzana ndi zakugonana.—Onani 1Ak 6:9.
B. F. Westcott, mmodzi wa akonzi a Malemba Achigiriki otchedwa Westcott and Hort, m’buku linalake pa mfundo yake yokhudza Aef 5:3 ananenapo za matanthauzo osiyanasiyana a por·neiʹa m’Malemba. Iye anati: “Mawu amenewa amatanthauza kugonana kosaloleka kwa mtundu uliwonse, (I) chigololo: Hos. ii. 2, 4 (LXX.); Mat. v. 32; xix. 9; (2) ukwati wosaloleka, I Akor. v. I; (3) dama, limene ambiri amalidziwa monga mmene alitchulira pa [Aef 5:3].” (Saint Paul’s Epistle to the Ephesians, London ndi New York, 1906, tsa. 76), Ponena kuti “limene ambiri amalidziwa,” zikuonekeratu kuti akutanthauza dama limene ambiri masiku ano amalidziwa kuti limachitidwa ndi anthu amene sali pa banja.
Kuwonjezera pa tanthauzo lenileni limeneli, m’malo ena m’Malemba Achigiriki por·neiʹa ali ndi tanthauzo lophiphiritsa. Ponena za tanthauzo limeneli, mtanthauzira mawu wotchedwa ZorellGr, danga 1106, pofotokoza za mawu akuti por·neiʹa amati: “kupanduka pa chikhulupiriro choona, kwapang’ono kapena kupandukiratu, kusiya Mulungu woona yekha Yahweh n’kupita kwa milungu yachilendo [4Mf 9:22; Yer 3:2, 9; Ho 6:10; ndi malemba ena, pakuti mgwirizano wa Mulungu ndi anthu ake unali ngati ukwati wauzimu]: Chv 14:8; 17:2, 4; 18:3; 19:2.” (4Mf m’Baibulo la LXX n’chimodzimodzi ndi 2Mf m’malemba olembedwa ndi Amasorete.)
M’Malemba Achigiriki, por·neiʹa akupezeka m’malo 25 otsatirawa: Mt 5:32; 15:19; 19:9; Mko 7:21; Yoh 8:41; Mac 15:20, 29; 21:25; 1Ak 5:1, 1; 6:13, 18; 7:2; 2Ak 12:21; Aga 5:19; Aef 5:3; Akl 3:5; 1At 4:3 ndi Chv 2:21; 9:21; 14:8; 17:2, 4; 18:3; 19:2.
Mneni wa mawu amenewa, wakuti por·neuʹo, amene Baibulo la Dziko Latsopano lamumasulira kuti ‘kuchita dama’ akupezeka m’malo 8 otsatirawa: 1Ak 6:18; 10:8, 8; Chv 2:14, 20; 17:2; 18:3, 9.
Mneni wina wakuti ek·por·neuʹo, amene Baibulo la Dziko Latsopano lamumasulira kuti “pochita dama loipitsitsa,” akupezeka kamodzi kokha pa Yuda 7.
Dzina lopangidwa kuchokera ku mawu amenewa, lakuti porʹne, limene Baibulo la Dziko Latsopano lalimasulira kuti “hule,” likupezeka m’malo 12 awa: Mt 21:31, 32; Lu 15:30; 1Ak 6:15, 16; Ahe 11:31; Yak 2:25 ndi Chv 17:1, 5, 15, 16; 19:2.
Dzina linanso lopangidwa kuchokera ku mawu amenewa lakuti porʹnos, limene Baibulo la Dziko Latsopano lalimasulira kuti “wadama,” likupezeka m’malo 10 otsatirawa: 1Ak 5:9-11; 6:9; Aef 5:5; 1Ti 1:10; Ahe 12:16; 13:4 ndi Chv 21:8; 22:15. Mtanthauzira mawu wotchedwa LSJ, tsa. 1450 amati mawuwa amatanthauza “mnyamata wogonedwa ndi amuna, mwamuna wogona anzake kumatako, munthu wadama, komanso munthu wopembedza mafano.”