Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kuvutitsidwa ndi Amuna Kapena Akazi Kodi Ndingadzitetezere Motani?
ANITA ndi mtsikana wansangala wazaka 16 ndipo amakonda kumwetulira. Komabe, akumanga nkhope yake pofotokoza zochitika kusukulu kwake posachedwa. “Mnyamata wina wotchuka anandichinga m’likole nayamba kundigwiragwira,” akukumbukira motero. “Anachita zimenezi kwa atsikana ena popanda vuto—anatengeka naye mtima, koma ine sindinatero! Ndinampempha mwaulemu kuti asiye kundigwiragwira koma sanamve. Anaganiza kuti ndinkaseka.”
Vuto la Anita lili lofala kwambiri. Mwachionekere kuvutitsidwa ndi amuna kunali kofala m’nthaŵi za Baibulo. (Yerekezerani ndi Rute 2:8, 9, 15.) Ndipo nkofalikira kowopsa lerolino. “Amuna ena kuntchito analankhula zopusa ponena za thupi langa,” akutero mtsikana wina. Koma nthaŵi zambiri kuvutitsako sikumangothera m’mawu. “Ena ayesa kundikhudza ngakhale kundikumbatira,” akuwonjezera motero. Mtsikana wina wotchedwa René anauza Galamukani! kuti: “Kuntchitoko anandivuta kwambiri moti ndinasiya ntchito.”
Lipoti la kufufuza kwina kwa posachedwa linasonyeza kuti 81 peresenti ya ana a sukulu a magiredi 8 mpaka 11 anati anavutitsidwapo kamodzi. “Mwa amenewo,” ikutero U.S.News & World Report, “65 peresenti ya atsikana ndi 42 peresenti ya anyamata anati anawagwiragwira, kuwakumbatira kapena kuwatsina modzutsa chilakolako choipa.” Inde, anyamata ndi atsikana zimawachitikira zimenezo. Kholo la mnyamata wina likukumbukukira kuti: “Ndadabwa ndi kulimba mtima kwa atsikana akusukulu kumene mwana wanga wamwamuna amaloŵa. Kuyambira pamene anali wazaka ngati 12, talandira mafoni osaleka, mapempho okayenda naye, mawu odzutsa chilakolako choipa—ndi zina zambiri.”
Nkwapafupi kupeputsa khalidwe losautsa limeneli. Mtsikana wina anati: “Nthaŵi zina amakuchita moseka.” Koma Akristu samaziyesa kuseka ayi! Amadziŵa kuti ovutitsa kaŵirikaŵiri amayesa kukukopa kuti uloŵe m’chisembwere, chinthu chimene Yehova Mulungu amatsutsa. (1 Akorinto 6:9, 10) Ndiponso, Mawu a Mulungu amalamula kuti akazi aang’ono achitidwe “m’kuyera mtima konse.” (1 Timoteo 5:2) Amaletsanso ‘kulankhula zopusa.’ (Aefeso 5:3, 4) Chotero Akristu achinyamata sayenera kulekerera ovutitsawo! Funso nlakuti, Kodi mungadzitetezere motani kuti musavutitsidwe? Tiyeni tikambitsirane za njira zake zopeŵera.
Njira Zopeŵera Kuvutitsidwa
Khalani ndi mbiri ya khalidwe Lachikristu. “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu,” Yesu analangiza motero. (Mateyu 5:16) Njira ina yochitira zimenezi ndiyo kuuza anzanu akusukulu ndi akuntchito zimene mumakhulupirira. Pamene mudziŵika monga munthu wa chikhulupiriro cholimba ndi wa miyezo yapamwamba ya makhalidwe, mwachionekere sadzakuvutitsani kwambiri.
Samalani kavalidwe ndi kaonekedwe kanu. M’nthaŵi za Baibulo zovala zina zinkadziŵikitsa mkazi kukhala wachiwerewere. (Yerekezerani ndi Miyambo 7:10.) Momwemonso lerolino, masitayelo onyanyula angakuchititseni kudziŵika kwa anzanu, koma akhoza kupereka uthenga wolakwika. Mungapezeke kuti mukukopa anyamata kapena atsikana mosayenera. Pangakhale vuto lofanana ngati mtsikana adzikometsera mwa njira imene ingamchititse kukhala ngati wachikulirepo. Malangizo a Baibulo amati ‘mudziveke nokha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso.’—1 Timoteo 2:9.
Sankhani mabwenzi anu mosamala. (Miyambo 13:20) Ndi iko komwe, anthu adzakuonani malinga ndi mmene amaonera mabwenzi anu. Ndipo ngati anzanu amawononga nthaŵi yaitali akumalankhula za atsikana kapena anyamata, anthu angakuganizireni molakwa.—Yerekezerani ndi Genesis 34:1, 2.
Peŵani kutyasira. Nzoona kuti kukhala waubwenzi sikulakwa, komabe kuyang’ana mwa chidwi ndi kukhudza kungasokeretse mtsikana kapena mnyamata mosavuta. Simufunikira kukhudza wina kuti mupitirize kukambitsirana. Tsatirani Lamulo la Chikhalidwe ndipo chitirani atsikana kapena anyamata mwa njira imene mufuna kuti azikuchitirani—m’kuyera mtima ndi ulemu. (Mateyu 7:12) Peŵani kukopa chidwi cha anyamata kapena atsikana mukumaganiza kuti mukungoseŵera. Kuchita zimenezo kungakhale kosakoma mtima ndi kosokeretsa ndiponso kowopsa. “Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake?” Baibulo limafunsa pa Miyambo 6:27.
Ngati Muvutitsidwa
Ndithudi, ngakhale ngati mwasintha kavalidwe, kaonekedwe, ndi khalidwe lanu, ena alibe ufulu wa kukukhudzani kapena kukugwiragwirani mosayenera. Ndipo zimenezi zachitikira ngakhale achinyamata ena amaonekedwe ndi khalidwe labwino. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati zimenezo zikuchitikirani? Nawa malingaliro ena.
Kanani kwa mtu wagalu. Aliyense amadziŵa kuti anthu ena amakana kuti safuna kugonana pamene akufuna. Chotero ovutitsawo angaganize kuti kukana wamba ndiko kuvomereza—kapena kuti zinthu zingatheke ndithu—kufikira mutawatsimikizira kuti sizingatheke. Uphungu wa Yesu wakuti iyayi wanu akhale iyayi umathandiza kwambiri pankhaniyi. (Mateyu 5:37) Musasekerere kapena kuchita ngati mukuseŵera. Ndipo musalole majesicha anu, liwu, kapena nkhope yanu kusemphana ndi zokamba zanu.
Chitani ukali. Kaŵirikaŵiri ovutitsawo amadalira pa kukayikira kukana kwa amene akumvutitsa. Komabe, m’nthaŵi za Baibulo akazi Achiisrayeli anapatsidwa mphamvu, inde thayo, la kukana kugonedwa. (Deuteronomo 22:23, 24) Momwemonso lerolino, Mkristu sayenera kuganiza kuti kumgwiragwira mosayenera kapena kumkumbatira sikuli nkhani yaikulu. Nkosafunika, ndiko nkhanza ya kukuchotserani ulemu monga munthu ndipo monga Mkristu. Simuyenera kulola zimenezo! Baibulo limalangiza kuti “dana nacho choipa”!—Aroma 12:9.
Njira ina yothandiza kuletsa khalidwelo ndiyo kuzazira ndi kuchititsa manyazi wokuvutaniyo; mwinamwake angasiye. Kumbukirani zimene zinachitikira Anita, wotchulidwa poyamba. Kumuuza mwaulemu mnyamatayo kuti asiye kumgwiragwira sikunathandize. Anita akuti: “Ndinamchititsa manyazi pamaso pa anzake mwa kumkalipira mofuula KUSANDIGWIRA motero!” Nchiyani chimene chinachitika? “Anzake onse anamseka. Iye ananyowa kwambiri kwa kanthaŵi, koma patapita masiku angapo, anapepesa kaamba ka khalidwe lake ndipo pambuyo pake ananditetezera pamene wina anayesa kundivutitsa.”
Ngati mawu sathandiza, mungangofunikira kuchokapo—ngakhale kuthaŵa—kusiyana ndi munthuyo. Ndipo ngati kuthaŵa sikutheka, muli ndi ufulu wa kugwiritsira ntchito njira iliyonse kuti mupeŵe nkhanzayo. Mtsikana wina Wachikristu ananena mosapita m’mbali kuti: “Pamene mnyamata wina anayesa kundigwira, ndinammenya ndi nkhonya mwamphamvu, ndi kuthaŵa!” Ndithudi, zimenezi sizikutanthauza kuti wovutitsayo sadzayesanso. Chotero mwachionekere mudzafunikira thandizo.
Uzani munthu wina. “Nzimene ndinachita pomalizira pake,” Adrienne wazaka 16 akuvomereza motero. “Ndinapempha nzeru kwa makolo anga kuti ndidziŵe chochita pamene mnyamata wina amene ndinayesa bwenzi labwino sanafune kusiya kundivutitsa. Pamene ndinamkanira, nayenso analimbikira, ngati kuti tinali pa seŵero.” Makolo a Adrienne anampatsa nzeru zabwino zimene zinamthandiza kulimbana bwino kwambiri ndi vutolo.
Nanunso makolo anu angakuthandizeni kuchita ndi kusautsika mtima kulikonse konga kudodoma, mantha, ndi manyazi, kumene mungakhale nako chifukwa cha kuvutitsidwa. Angakulimbikitseni mwa kukuuzani kuti kusautsidwako si mlandu wanu. Ndiponso angagwiritsire ntchito njira zina zimene zingathandize kukutetezerani mtsogolo.
Mwachitsanzo, anganene kuti kuli bwino kudziŵitsa mphunzitsi wanu kapena akuluakulu a sukulu za vutolo. Sukulu zambiri ku United States sizimanyalanyaza madandaulo ayi ndipo zili ndi njira zolongosoka zosamalira kuvutitsana kwa anyamata ndi atsikana pakati pa ana a sukulu.
Zoona, si akulu onse a sukulu amene amamvetsera. “Kusukulu kwathu,” akutero Earlisha wazaka 14, “aphunzitsi nthaŵi zina amatukwana ndi kuchita zinthu zoipa kuposa achichepere. Sudziŵa kumene ungapite kaamba ka thandizo.” Pamenepo, mposadabwitsa kuti pamene iye anakanena kuti mnyamata akumvutitsa, iwo anamnena kuti anali woliralira. Komabe, Earlisha sanalekere pamenepo. Anagwirizana ndi atsikana ena asanu ndi mmodzi amene mnyamata amodzimodziyo anatsina ndi kuwagwiragwira. “Kuti ahedimasitala atsimikize kuti panalidi vuto, panafunikira asanu ndi mmodzi a ife,” akutero. Pomalizira pake, mtsikanayo anathetsa khalidwe loipalo.
Pitani kwa Mulungu kaamba ka thandizo. Ngati kukhala pasukulu kumakuchititsani kumva ngati akutsekerani m’dzenje la mikango, kumbukirani kuti Yehova Mulungu anatetezera mneneri Danieli m’dzenje lenileni la mikango. (Danieli 6:16-22) Yehova akhozanso kukuthandizani. Akudziŵa mavuto amene mukukumana nawo kusukulu. Ndipo zinthu zikafika povuta, mungaitanire pa iye kuti akuthandizeni—mofuula ngati kuli kofunika! Musawope kapena kuchita manyazi chifukwa cha kudziŵika monga mtumiki wa Mulungu woona. Baibulo limalonjeza atumiki okhulupirika a Yehova kuti: “Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m’manja mwa oipa.”—Salmo 97:10.
Zimenezi sizikutanthauza kuti adzakulanditsani mozizwitsa. Muyenera kuchita zimene mungathe kudzitetezera nokha. Tsatirani miyezo ya Baibulo. Khalani odekha m’mawu ndi m’kaonekedwe kanu. Samalani pochita ndi anyamata kapena atsikana. Mwa kutero, mungadzitetezere kwambiri kuti musavutitsidwe.
Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Chithunzi patsamba 30]
Musakhale wokana wamba pokana machitidwe osayenera; iyayi wanu akhale iyayi!