Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingathetse Bwanji Vuto Langa Loopa Kunenepa?
“Chimene chimandivuta kwambiri m’moyo wanga ndicho kusankha kuti ndizipaka majalini pa buledi wanga kapena ayi. Kodi ndingakhale bwanji ndi chidwi pochita zinthu ngati ndikuda nkhaŵa choncho ndi majalini? Basi, ndagamula kuti sindidzadyanso majalini—chifukwa ali ndi mafuta ambiri. Matenda a “anorexia” apambananso. Ine ndagonja.”—Jaimee.
MATENDA a kudya amavutitsa achinyamata mamiliyoni ambiri.a Ambiri a iwo sanachite kufuna kuti ayambe kudya pang’ono (anorexia) kapena kudya chakudya chochuluka kenako n’kumasanza (bulimia). Koma ambiri anayamba zimenezi chifukwa chongofuna kuonda pang’ono basi. Komabe, asakuganizako n’komwe anangozindikira kuti ayamba mkhalidwe wachilendo womadya pang’ono kapena womadya mopitirira kenako n’kumakasanza. “Ndinayamba khalidwe losala kudya limeneli chifukwa choti ndimafuna kuonda koma m’malo mwake khalidweli likundilamulira,” akutero Jaimee.
Ngati muli ndi vuto la kudya chifukwa choopa kunenepa, kodi mungachite chiyani? Choyamba dziŵani kuti pali achinyamata ambiri amene akhala akulimbana ndi matenda akudya ndipo apambana! Koma motani?
Kudziyang’ana Bwino
Njira yofunika kwambiri imene mungatsate kuti mugonjetse vuto la kudya ndiyo kudziyang’ana bwino. “Anthu ambiri amene ali ndi vuto la kudya amadziona ngati onenepa, samaona matupi awo mmene alilidi ndipo amadzida kwambiri, makamaka thupi lawo.” Likutero buku lotchedwa Changing Bodies, Changing Lives (Kusintha Thupi, Kusintha Moyo). Ndithudi, achinyamata ena amaganiza kwambiri za maonekedwe a thupi lawo kotero kuti akangosintha pang’ono amaona ngati vuto lalikulu kwambiri.
Vicki wa zaka 17 akuti: “sindingalole kuti ndikhalebe wonenepa chonchi. Chiuno changa n’chachikulu kwambiri moti sindingathe kupisira malaya aliwonse.” Ngakhale kuti anali atawonda kale ndi makilogalamu 10, Vicki sanakhutiritsidwebe. Ankakana kudya ndipo nthaŵi zina amapisa chala ku m’mero n’kusanza zimene wadya.
Inde sikulakwa nthaŵi zina kuganizira za maonekedwe anu. N’chifukwa chake, Baibulo limatchulapo za maonekedwe a amuna ndi akazi angapo kuti anali abwino; ena a iwo ndi Sara, Rakele, Yosefe, Davide, ndi Abigayeli.b Mpaka Baibulo limatcha Abisagi, namwali amene amasunga Davide kuti “wokongola ndithu.”— 1 Mafumu 1:4.
Kukongola Kwenikweni
Komabe, Baibulo silinena kuti kuoneka bwino m’maso kapena kukhala ndi thupi loumbika bwino n’kumene kuli kofunika koposa. Koma m’malo mwake limati ‘kukhala munthu wobisika wamtima’ ndiko. (1 Petro 3:4) Munthu wam’kati ndi amene amapangitsa munthu kukhala wabwino kapena woipa pamaso pa Mulungu ngakhalenso pa anthu.— Miyambo 11:20, 22.
Taganizirani za Abisalomu, mwana wa Mfumu Davide. Baibulo limati: “Ndipo m’Israyeli monse munalibe wina anthu anam’tama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chirema.” (2 Samueli 14:25) Komatu, mnyamata ameneyu anali wachinyengo. Kudzikuza ndi kulakalaka kukhala wapamwamba kunam’chititsa kuyesa kugwetsa mfumu yoikidwa ndi Yehova. Choncho, Baibulo silinena kuti Abisalomu anali wabwino, m’malo mwake limanena kuti iye anali munthu wosachita manyazi n’kugalukira ndipo anali ndi udani wotha kupha nawo munthu.
Kuoneka bwino kwenikweni kapena kukongola, kwa munthu, sikuti kumadalira mmene akuonekera m’maso. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Nzeru ipambana, tatenga nzeru; M’kutenga kwako konseko utenge luntha. Idzaika chisada cha chisomo pamutu pako; Idzakupatsa korona wokongola.”—Miyambo 4:7, 9.
Komabe, tiyenera kuvomereza kuti anthu amene ali ndi mavuto a kudya sikuti nthaŵi zonse amatero chifukwa chakuti sakusangalatsidwa ndi maonekedwe awo. Buku lina la maumboni linati: “Anthu amene amakhala ndi mavuto a kudya kenaka n’kugwidwa ndi matenda a kudya monga anorexia nervosa, bulimia ndi overeating, nthaŵi zambiri amadziderera—samadziona ngati kanthu ndipo amaganiza kuti ena amawaonanso chimodzimodzi.”
Pali zinthu zingapo zimene zingachititse kuti munthu azidziona kukhala wopanda pake. Mwachitsanzo, pamene mwatha msinkhu mungasokonezeke maganizo—makamaka ngati anzanu sanathebe msinkhu. Ndiyenso, pali ana ena amene amaleredwa m’mabanja mmene amangotukwanidwa, mwina kumenyedwa ngakhalenso kuchitidwa chipongwe monga kugwiriridwa. Ngakhale kuti mavutowa amayamba mosiyanasiyana, kuti muwathetse muyenera kuzindikira chimene chikukuchititsani kuti muzidziderera. Ndiye kuti muyenera kudzimva kuti ndinu munthu wofunika. Palibe munthu wopanda pabwino. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 12:14-18.) N’zoona kuti mwina inuyo simungaone ubwino wanu, koma mnzanu wachikulire angathe kukulongosolerani.
Koma nanga mungatani ngati muyeneradi kuchepetsako thupi lanu kuti mukhale ndi thanzi labwino? Baibulo limatilangiza kuti tizikhala “odzisunga.” (1 Timoteo 3:11) Choncho, tiyenera kupeŵa kudya pang’ono mopambanitsa kapena kutengeka ndi njira zodziondetsera msanga. Kuti muchepetseko thupi, mwina njira yabwino ndiyo kudya bwinobwino koma n’kumachita maseŵera olimbitsa thupi pamlingo wabwino. Magazini ya FDA Consumer inati, “Pali njira yabwino ndi yoipa yochitira chinthu chilichonse, n’chimodzimodzinso ndi kuchepetsa thupi. Njira yoipa yochitira zimenezi ndiyo kusadya chakudya cha nthaŵi inayake, n’kumangodya buledi ndi kumwera madzi basi, kumwa mankhwala owondetsa, kapena kudzikakamiza kusanza.”
Mmene Kuuza Munthu Wina Kungakuthandizireni
Nancy Kolodny amene akugwira ntchito yothandiza anthu akuyerekezera kukhala ndi vuto la kudya ndi “kuloŵa wekha m’nyumba yaikulu yokhala ndi njira zambirimbiri koma ulibe munthu wokutsogolera, sukudziŵa kuti potulukira ndi pati, ndipo kuti upaona nthaŵi yanji ngati uti upaone n’komwe. . . . Pamene ukukhalitsamo m’nyumbamo m’pamenenso ukuthedwa maganizo kwambiri ndi kusoŵa chochita kuti utulukemo.” Ngati muli ndi zizindikiro za matenda a anorexia kapena bulimia, ndiye kuti mukufunika kuthandizidwa. Panokha simungathe kutulukamo “m’nyumba” yotereyi. Choncho uzani makolo anu kapena munthu wina wamkulu amene mumam’khulupirira. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Bwenzi lenileni limakonda nthaŵi zonse, ndipo limakhala mbale panthaŵi ya tsoka.”—Miyambo 17:17, NW.
Mboni za Yehova zambiri zapeza mabwenzi enieni oterowo pakati pa akulu mumpingo wachikristu. Komabe, akulu ameneŵa si madokotala ayi, ndipo ngati angakuthandizeni si ndiye kuti simukufunikiranso mankhwala. Ngakhale zili choncho, oyang’anira achikristu sangatsekere dala makutu awo “polira waumphaŵi,” ndipo uphungu ndi mapemphero awo ‘zingapulumutse wodwalayo.’—Miyambo 21:13; Yakobo 5:13-15.
Ngati kuyankhula ndi munthu maso ndi maso kumakuvutani, lembani maganizo anu m’kalata, ndipo mupemphe kuti akuyankheni. Chofunika ndicho kuulula vutolo. Nancy Kolodny akuti: “Mukavomereza kuti simungathenso kulimbana nawo nokha, ndiye kuti mwadzipereka kuti kuyambira tsiku limenelo munthu wina azikuthandizani.” Akuwonjeza kuti: “Mwina njira zimenezi zingakuvuteni kuchita ndi kuzimvetsa, koma ndi zothandiza, zili ngati njira zimene mungatsate kuti mutuluke m’nyumba yaikulu ija.”
Akristu achinyamata angagwiritsenso ntchito njira ina yothandiza koposa—pemphero. Kupemphera kwa Mulungu si njira yongotonthozera maganizo pang’ono kwa kanthaŵi. N’kuyankhulitsana kwenikweni ndiponso kofunika, ndi Mlengi amene amakudziŵani bwino koposa mmene mumadzidziŵira! (1 Yohane 3:19, 20) Choncho, ngakhale kuti inoyo si nthaŵi yoti Yehova achotse matenda onse, Mulungu wathu wachikondiyu angatsogolere mapazi anu kotero kuti simungagwedezeke. (Salmo 55:22) Posimba za zinthu zomwe zinamuchitikirapo, wamasalmo Davide analemba kuti: “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, Nandilanditsa m’mantha anga onse. Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nam’pulumutsa m’masautso ake onse.”—Salmo 34:4, 6.
Choncho, yesetsani kumuuza Yehova Mulungu maganizo a pansi penipeni pa mtima wanu. Mtumwi Petro analemba kuti: “Ndi kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.” (1 Petro 5:7) Kuti muthe kuyamikira chifundo cha Yehova, bwanji nanga osaŵerenga mwachifatse Masalmo 34, 77, 86, 103, ndi 139? Kusinkhasinkha mutaŵerenga masalmo ameneŵa kudzalimbitsa chikhulupiriro chanu chakuti Yehova ndi wokhulupirika ndipo akufuna kuti mupambane. Mwakuŵerenga Mawu ake, mudzayamba kumva mmene Davide ankamvera. Iyeyu analemba kuti: “Pamene ndikuda nkhaŵa ndi pamene ndikudandaula, inu mumanditonthoza ndi kundisangalatsa.”— Salmo 94:19, Today’s English Version.
Lezani Mtima—Kuchira Kwake N’kwapang’onopang’ono
Anthu ambiri amene amalandira chithandizo akadwala matenda a kudya sachira lero ndi lero. Taganizirani zimene zinamuchitikira Jaimee, amene ananena mawu amene ali kumayambiriro kwa nkhani ino. Atalandira chithandizo, ankalepherabe kudya chakudya bwinobwino ngakhale phala. Iye akunena kuti: “Kuti ndidye ndiyenera kumadzinong’oneza n’kumadziuza kuti chakudya chimenechi n’chabwino, chakudya n’chofunika kuti ndikhale ndi moyo. Ndikadya phala lodzaza sipuni imodzi yokha ndimaona ngati kuti ndadya chiphala chambirimbiri.
Ngakhale kuti nthaŵi ina Jaimee anatsala pang’ono kufa anaganiza kuti ndibwino kuti athetse vuto lake la kudya. Iye anati; “Sindilola kufa. Ndilimbana nalo vuto limeneli ndipo ndipambana. Ndithetsa anorexia. Kukhala kovuta, komabe nditero.” Inunso Mungapambane!
[Mawu a M’munsi]
b Onani Genesis 12:11; 29:17; 39:6; 1 Samueli 17:42; 25:3.
[Chithunzi patsamba 15]
Kudya zakudya za magulu onse ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi zingakuthandizeni kuti musanenepe mopitirira