Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mungatani Mutakumana Ndi Vuto Lalikulu?
    Galamukani!—2014 | July
    • 1. Zinthu zotsalira pa nthawi ya tsoka lachilengedwe; 2. Bedi la kuchipatala; 3. Magalimoto agundana

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUTAKUMANA NDI VUTO LALIKULU?

      Kodi Mungatani Mutakumana Ndi Vuto Lalikulu?

      ANTHUFE tikhoza kukumana ndi vuto lalikulu pa nthawi imene sitikuyembekezera. Ndipo zimenezi zikhoza kuchitikira aliyense, ngakhale munthu wolemera.

      BAIBULO LIMANENA KUTI:

      “Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo, anzeru sapeza chakudya, omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma, ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”—Mlaliki 9:11.

      Popeza aliyense akhoza kukumana ndi vuto lalikulu, funso ndi lakuti: Kodi inuyo zimenezi zitakuchitikirani mungatani? Mwachitsanzo, kodi mungatani:

      • Katundu wanu yense atawonongeka pa ngozi zamwadzidzidzi monga kusefukira kwa madzi?

      • Atakupezani ndi matenda aakulu?

      • Munthu wa m’banja lanu atamwalira?

      A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magaziniyi, amakhulupirira kuti Baibulo lingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita zoterezi zikachitika. Baibulo lingakuthandizeninso kudziwa zimene mungachite kuti mukhale ndi chiyembekezo. (Aroma 15:4) Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza umboni wa zimenezi.

  • Katundu Wanu Yense Atawonongeka
    Galamukani!—2014 | July
    • Zotsalira pambuyo pa chivomezi ndi tsunami

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUTAKUMANA NDI VUTO LALIKULU?

      Katundu Wanu Yense Atawonongeka

      Pa March 11, 2011, ku Japan kunachitika chivomezi champhamvu kwambiri. Chivomezichi chinapha anthu oposa 15,000 komanso chinawononga katundu wa ndalama zoposa madola 200 biliyoni a ku America. Bambo wina wazaka 32 dzina lake Kei, atamva kuti chivomezichi chichititsanso kuti kubwere tsunami, anathawira kumalo ena okwera. Kei anati: “Tsiku lotsatira ndinabwerera kunyumba kuti ndikatenge zina ndi zina. Koma nditafika, sindinapeze chilichonse pamalopo. Nyumba komanso katundu wanga yense anali atakokolokera m’nyanja.”

      Kei

      Kei ananenanso kuti: “Zinanditengera nthawi kuti ndivomereze zoti zinthu zanga zonse zapita. Zinthu monga galimoto, makompyuta, matebulo, mipando, zida zanga zoimbira nyimbo ndiponso zogwirira ntchito, zonse zinali zitapita ndi madzi. Palibe ngakhale chinthu chimodzi chimene chinatsala.”

      ZIMENE MUNGACHITE

      Muziganizira kwambiri zinthu zimene mwatsala nazo, osati zimene zawonongeka. Baibulo limati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Kei ananena kuti: “Poyamba ndinalemba zinthu zonse zimene ndinkafuna nditakhala nazo. Koma ndinaona kuti zimenezi zinkangochititsa kuti ndizikumbukira katundu wanga amene anawonongeka uja. Choncho ndinaganiza zolemba zinthu zofunika kwambiri zokha ndipo ndikapeza chinthu chimodzi, ndinkachichotsa pamene ndinalembapo. Zimenezi zinandithandiza kuti ndiyambirenso kukhala bwinobwino.”

      M’malo momangodzimvera chisoni, yesetsani kumathandiza anthu ena. Kei anati: “Ndinalandira zinthu zosiyanasiyana kuchokera ku mabungwe komanso anzanga. Koma kenako ndinayamba kuona kuti kumangolandira zinthu kuchokera kwa anthu kukundichotsera ulemu. Zitatere ndinakumbukira mawu a m’Baibulo a palemba la Machitidwe  20:35 akuti: ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.’ Popeza ndinalibe zinthu zoti ndingapatse anthu ena amene anakhudzidwa ndi tsokali, ndinkangowauza mawu olimbikitsa. Zimenezi zinandithandiza kwambiri.”

      Muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni pa mavuto anuwo. Kei ankakhulupirira zimene Baibulo limanena zoti Mulungu ‘amamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse.’ (Salimo 102:17) Inunso lemba limeneli lingakulimbikitseni.

      Dziwani izi: Baibulo limanena kuti m’tsogolomu palibe munthu aliyense amene adzadandaule chifukwa choti zinthu zake zawonongeka ndi masoka achilengedwe.a—Yesaya 65:21-23.

      a Kuti mudziwe za cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili, werengani mutu 3 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.pr418.com/ny.

  • Atakupezani Ndi Matenda Aakulu
    Galamukani!—2014 | July
    • Bedi la kuchipatala

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUTAKUMANA NDI VUTO LALIKULU?

      Atakupezani Ndi Matenda Aakulu

      Mabel, yemwe amakhala ku Argentina, anali mzimayi wolimbikira ntchito ndipo ankathandiza anthu kuchita mafizo. Koma mu 2007, mutu wake unayamba kumamupweteka kwambiri tsiku lililonse, komanso ankamva kutopa kwambiri. Iye anati: “Ndinapita kuzipatala zosiyanasiyana ndipo ndinamwa mankhwala ambirimbiri koma sizinathandize.” Kenako atapita kuchipatala china, anakamuunika m’mutu ndipo anamupeza kuti ali ndi chotupa mu ubongo. Mabel ananena kuti: “Adokotala atandiuza, sindinakhulupirire. Sindinkayembekezera kuti ndingapezeke ndi matenda oopsa chonchi.”

      Mabel

      Iye ananenanso kuti: “Atandichita opaleshoni, m’pamene ndinazindikira kuti vutoli linali lalikulu kwambiri. Nditatsitsimuka, sindinkatha kutakataka moti ndinangogona chagada. Ndisanayambe kudwala, ndinali munthu wakhama pa ntchito komanso ndinkapanga zinthu pandekha. Koma matendawa anachititsa kuti zinthu zisinthe kwambiri pa moyo wanga moti sindinkathanso kuchita chilichonse. Nthawi yonse imene ndinakhala m’chipatala zinthu sizinkandiyendera. Ndinkangomva phokoso la zipangizo za m’chipatala, kulira kwa maambulansi komanso kubuula kwa anthu odwala. Kulikonse kumene ndinkayang’ana, ndinkangoona zinthu zomvetsa chisoni.”

      Mabel anawonjezera kuti: “Panopa, ndingati ndikupezako bwino. Ndimatha kuyenda ndekha komanso nthawi zina ndimatha kukayendako panja. Komabe ndimavutika kuona, moti ndimaona zinthu ziwiriziwiri komanso nthawi zambiri ndimakhala wofooka.”

      ZIMENE MUNGACHITE

      Musamangoganizira kwambiri za mavuto anuwo. Lemba la Miyambo 17:22 limati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” Mabel anati: “Nditayamba kuchira, ndinkafunika kuchita mafizo amene ndinkachititsa odwala omwe ndinkawasamalira poyamba paja. Ndikamachita mafizowa, ndinkamva kuwawa kwambiri, moti nthawi zina ndinkaganiza kuti ndi bwino ndingosiya. Komabe, ndinkayesetsa kuchotsa maganizo amenewa chifukwa ndinkadziwa kuti mafizowa angandithandize kuti ndipezeko bwino.”

      Muziganizira kwambiri za zinthu zosangalatsa zomwe zidzachitike m’tsogolo. Mabel ananenanso kuti: “Baibulo linandithandiza kudziwa chifukwa chake anthufe timavutika. Ndinkadziwanso kuti tsiku lililonse likadutsa, ndiye kuti tikuyandikira nthawi imene mavuto onse adzathe.”a

      Muzikumbukira kuti Mulungu amakuderani nkhawa. (1 Petulo 5:7) Mabel anafotokoza mmene kudziwa zimenezi kunamuthandizira. Iye anati: “Pamene ankanditenga kuti akandipange opaleshoni, ndinamvetsa bwino tanthauzo la lemba la Yesaya 41:10. Palemba limeneli Mulungu amati: ‘Usachite mantha, pakuti ndili nawe.’ Ndinkamvako bwino ndikaganizira kuti Yehova akuona zimene zikundichitikira ndipo akundidera nkhawa.”

      Dziwani izi: Baibulo limaphunzitsa kuti posachedwapa anthu sazidzadwalanso.—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

      a Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

  • Munthu wa M’banja Lanu Akamwalira
    Galamukani!—2014 | July
    • Ngozi yoopsa ya galimoto

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUTAKUMANA NDI VUTO LALIKULU?

      Munthu wa M’banja Lanu Akamwalira

      Ronaldo wa ku Brazil, anapulumuka pa ngozi ya galimoto imene inapha anthu 5 a m’banja lake. Omwalirawo anali mayi ake, bambo ake, azichimwene ake awiri komanso azakhali ake. Ronaldo anati: “Mmene ndinkamva kuti anthuwa anamwalira, n’kuti nditakhala m’chipatala miyezi iwiri.”

      Ronaldo

      Iye ananenanso kuti: “Atandiuza, sindinakhulupirire kuti apitadi. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Koma zoona onse angamwalire nthawi imodzi?’ Nditazindikira kuti apitadi, ndinamva chisoni kwambiri ndipo ndinali ndisanamvepo chisoni chonchi. Kenako ndinayamba kuona kuti sindingakwanitse kukhala ndi moyo popanda anthuwa moti kwa miyezi ingapo, ndinkalira tsiku lililonse. Nthawi zambiri ndinkadziimba mlandu kuti ndinaloleranji munthu wina kuyendetsa galimoto. Ndinkaona kuti ndikanakhala kuti ndinkayendetsa ndi ineyo, mwina anthuwa sakanafa.”

      Iye anawonjezeranso kuti: “Panopa patha zaka 16 kuchokera pamene zimenezi zinachitika ndipo ndayamba kuzolowera kukhala ndekha. Koma ndimaganizirabe za imfa yomvetsa chisoniyi moti ndimaona kuti sindidzaiwala.”

      ZIMENE MUNGACHITE

      Ngati mukumva chisoni kwambiri moti mukufuna kulira, ndi bwino kulira. Baibulo limati pali “nthawi yolira.” (Mlaliki 3:1, 4) Ronaldo ananena kuti: “Ndikaona kuti ndikufuna kulira, ndinkalira. Sindinkamva bwino ndikadzigwira kuti ndisalire, koma ndikalira ndinkamvako bwino.” Komabe anthufe timasonyeza chisoni m’njira zosiyanasiyana. Choncho kusalira sikuti nthawi zonse kumasonyeza kuti munthu akudzigwira kuti asalire. Ndipo munthu amene sakufuna kulira, sayenera kuchita kudzikakamiza kuti agwetse misozi.

      Muziyesetsa kukhala pa gulu komanso kucheza ndi anthu. (Miyambo 18:1) Ronaldo ananenanso kuti: “Nthawi zina ndinkafuna nditangokhala ndekha, komabe ndinkayesetsa kuti ndizicheza ndi anthu. Anthu akabwera kudzacheza nane ndinkawalandira ndi manja awiri. Komanso ndinkakonda kuuza mkazi wanga ndi anzanga mmene ndikumvera.”

      Musamakhumudwe kwambiri munthu wina akakulankhulani mawu okhumudwitsa. Mawu okhumudwitsa amenewa akhoza kukhala akuti, “Komabe zinakhala bwino kuti, . . . ” Ronaldo anati: “Zinthu zina zimene anthu ankanena pofuna kundilimbikitsa, zinkangondikhumudwitsa.” Choncho m’malo momangoganizira mawu okhumudwitsawo, mungachite bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Usamaganizire kwambiri mawu onse amene anthu amalankhula.”—Mlaliki 7:21.

      Phunzirani Baibulo kuti mudziwe zimene zimachitikadi munthu akamwalira. Ronaldo anati: “Lemba la Mlaliki 9:5, limasonyeza kuti anthu amene anamwalira sakuzunzika. Kudziwa zimenezi kunandithandiza kuti ndisamadandaule poganiza kuti mwina makolo komanso abale anga akuzunzika. Baibulo limaphunzitsanso kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. Choncho ndikaganizira za abale anga amene anamwalira, ndimangoona ngati anapita ku ulendo winawake ndipo adzabweranso.”—Machitidwe 24:15.

      Dziwani izi: Baibulo limanena kuti posachedwapa Mulungu “adzameza imfa kwamuyaya.”a—Yesaya 25:8.

      Nkhanizi zikufotokoza zimene mungachite mutakumana ndi vuto lalikulu. Kuti mudziwe zimene Baibulo limanena zokhudza chifukwa chake anthufe timavutika, werengani nkhani za mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana Ndi Mavuto?” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2014.

      a Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 7 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena