-
BaibuloKukambitsirana za m’Malemba
-
-
. . . Chotero tiri okondwera kuti Baibulo latembenuzidwira m’Chicheŵa.’ (2) ‘Tchati ichi (“Mpambo wa Mabukhu a Baibulo,” mu NW) chimasonyeza kuti Genesis, bukhu loyamba la Baibulo, linamalizidwa mu 1513 B.C.E. Kodi munadziŵa, kuti pambuyo pa kulembedwa kwa Genesis, panapita zaka 2 900 Baibulo lonse lathunthu lisanatembenuziridwe m’Chingelezi? Ndipo zoposa zaka 200 zinapita matembenuzidwe a King James Version asanamalizidwe (1611 C.E.).’ (3) ‘Kuyambira zaka za zana la 17, Chingelezi chakhala ndi masinthidwe ambiri. Tawona zimenezo m’nthaŵi ya moyo wathu, kodi sichoncho? . . . Chotero tikuyamikira matembenuzidwe amakono amene amasonyeza mosamalitsa chowonadi choyambirira chimodzimodzicho m’chinenero chimene timalankhula makono.’
‘Muli ndi Baibulo lanu’
Wonani mutu waukulu wakuti “New World Translation.”
-
-
BomaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Boma
Tanthauzo: Kakonzedwe ka anthu kopangira ndi kugwiritsira ntchito malamulo. Kaŵirikaŵiri maboma amadziŵikitsidwa mogwirizana ndi magwero ndi ukulu wa ulamuliro wawo. Yehova Mulungu ndiye Wolamulira Wachilengedwe chonse, amene amapereka ulamuliro pa ena mogwirizana ndi chifuniro chake ndi chifuno. Komabe, Satana Mdyerekezi, wopandukira ulamuliro wa Yehova wamkulu, ali ‘wolamulira wa dziko’—mololedwa ndi Mulungu kwa kanthaŵi. Baibulo limasonyeza dongosolo ladziko lonse la ulamuliro wandale zadziko kukhala chirombo ndipo limanena kuti “chinjoka [Satana Mdyerekezi] chinampatsa [chirombo] mphamvu yake, ndi mpando wake wachifumu, ndi ulamuliro waukulu.”—Yoh. 14:30; Chiv. 13:2; 1 Yoh. 5:19.
Kodi nkotheka kwa anthu kukhazikitsa boma limene lidzabweretsadi chimwemwe chosatha?
Kodi cholembedwa cha mbiri ya anthu chimasonyezanji?
Mlal. 8:9: “Wina apweteka mzake pomlamulira.” (Zimenezi ziridi zowona ngakhale kuli kwakuti maboma ena ndi olamulira anayamba ndi chitsanzo chabwino.)
“Chitaganya chirichonse chimene chinaliko potsirizira pake chinatha. Mbiri iri ndi nkhani ya zoyesayesa zimene zinalephera, kapena zolinga zimene sizinakwaniritsidwe. . . . Chotero, monga wolemba mbiri, munthu ayenera kukhala ali ndi lingaliro la kusapeŵeka kwa tsoka.”—Henry Kissinger, wasayansi yandale zadziko ndi profesala pankhani zaboma, monga momwe kwagwidwira mawu mu The New York Times, October 13, 1974, p. 30B.
Kodi nchiyani chimene chimapinga zoyesayesa za anthu m’nkhani za boma?
Yer. 10:23: “Yehova, ndidziŵa kuti njira yamunthu siiri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Mulungu sanapereke chilolezo ku chilengedwe chake chaumunthu kuti chidziyambire njira yake yosadalira pa Mulungu.)
Gen. 8:21: “Ndingaliro ya mtima wamunthu iri yoipa kuyambira paunyamata wake.” (Siolamulira okha koma ndi olamulidwa omwe onsewo amabadwira mu uchimo, ndi zikhoterero zadyera.)
2 Tim. 3:1-4: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osayanjanitsika, . . . otukumuka mtima.” (Mavuto oyang’anizana ndi anthu lerolino sangathetsedwe kotheratu ndi mtundu umodzi wokha; amafunikira kugwirizana kotheratu kwa mitundu yonse. Koma zikhumbo zadyera zimalepheretsa zimenezo ndipo zimalepheretsanso moipa kwambiri chichirikizo chowona chirichonse pakati pa magulu osiyanasiyana mkati mwa mitundu.)
Baibulo limavumbulanso kuti mphamvu zoposa anthu zikugwira ntchito m’zochitika za anthu. “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) “Tiri ndi nkhondo, osati yomenyana ndi mwazi ndi thupi, koma yomenyana . . . ndi olamulira adziko amdima uno, yomenyana ndi makamu a mizimu yoipa mmalo akumwamba.” (Aef. 6:12, NW) “Mawu ouziridwa ndi ziwanda . . . amapita kwa mafumu adziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu, kuwasonkhanitsira pamodzi kunkhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chiv. 16:14, NW.
Kodi anthu angapeze motani mpumulo wosatha ku chisalungamo cha boma ndi chitsenderezo?
Kodi kuika amuna ena m’malo antchito kudzathetsa vutolo?
Kodi siziwona kuti kaŵirikaŵiri kumene masankho ali aufulu
-