Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mzimu
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • wakumwamba. Panali patsiku lachitatu pambuyo pa zimenezi pamene Yesu anaukitsidwa kwa akufa. Ndiyeno, monga momwe Machitidwe 1:3, 9 amasonyezera, panali masiku ena 40 iye asanakwere kumwamba. Chotero, kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la zimene Yesu adanena panthaŵi ya imfa yake? Iye anali kunena kuti anadziŵa kuti, pamene akafa, ziyembekezo za moyo wake wamtsogolo zinadalira kotheratu kwa Mulungu. Kaamba ka ndemanga zowonjezereka ponena za ‘mzimu umene umabwerera kwa Mulungu,’ wonani tsamba 297, 298, pamutu wakuti “Moyo (Soul).”)

      Ngati Wina Anena Kuti—

      ‘Kodi muli nawo mzimu woyera (kapena Mzukwa Woyera)?’

      Mungayankhe kuti: ‘Inde, ndicho chifukwa chake ndadza pakhomo panu lerolino. (Mac. 2:17, 18)’

      Kapena munganene kuti: ‘Ndiwo umene umanditheketsa kukhala ndi phande muuminisitala Wachikristu. Koma ndimapeza kuti anthu saali ndi lingaliro lofanana ponena za zimene zimapereka umboni wakuti munthu alidi ndi mzimu wa Mulungu. Kodi inu mumayang’ananji?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (Kukambitsirana kwa mfundo zina patsamba 320, 321.)

  • Mzimu wa Dziko
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Mzimu wa Dziko

      Tanthauzo: Mphamvu yosonkhezera imene imayambukira anthu amene saali atumiki a Yehova Mulungu, kuchititsa anthu amenewo kunena ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mchitidwe wapadera. Ngakhale kuli kwakuti anthu amachita mogwirizana ndi zikhumbo zawo, osonyeza mzimu wa dziko amapereka umboni wa mikhalidwe ina yaikulu, njira zochitira zinthu, ndi zolinga m’moyo zimene ziri zoŵanda m’dongosolo liripoli la zinthu limene Satana ali wolamulira ndi mulungu wake.

      Kodi nchifukwa ninji kuipitsidwa ndi mzimu wa dziko kuli nkhani yodetsa nkhaŵa kwambiri?

      1 Yoh. 5:19: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (Satana watulutsa mzimu umene umalamulira malingaliro ndi zochita za anthu amene saali atumiki ovomerezedwa a Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena