Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gl tsamba 26-27
  • Girisi ndi Roma Akhudza Moyo wa Ayuda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Girisi ndi Roma Akhudza Moyo wa Ayuda
  • ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ufumu wa Roma
  • Anthu a Mulungu Abwerera Kudziko Lawo
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Mayiko Otchulidwa M’baibulo
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Maufumu Athira Nkhondo Dziko Lolonjezedwa
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Chikristu Chifalikira Kumayiko Ena
    ‘Onani Dziko Lokoma’
Onani Zambiri
‘Onani Dziko Lokoma’
gl tsamba 26-27

Girisi ndi Roma Akhudza Moyo wa Ayuda

Ufumu wa Girisi

UFUMU wa Girisi unayambira kumapiri a Makedoniya n’kumakula. Kumeneko Alesandro, ali kumayambiriro a zaka zake za m’ma 20, anayamba kuganiza zopita kum’maŵa. M’chaka cha 334 B.C.E., anatsogolera asilikali ake kudutsa Helesipotale (Dardanelles), amene amalekanitsa Ulaya ndi Asiya. Agirikiwo ali pambuyo pa Alesandro, anayamba kugonjetsa mitundu ina mofulumira mofanana ndi “nyalugwe” wamphamvu. (Dan. 7:6) Alesandro anagonjetsa Aperisi pafupi ndi Troy, m’madambo a Mtsinje wa Gelenikasi, ndipo anawagonjetsanso kotheratu ku Isase.

Kenako Agiriki anaukira Suriya ndi Foinike, ndipo analanda Turo atazinga mudziwo miyezi isanu ndi iŵiri. (Ezek. 26:4, 12) Alesandro anasiya Yerusalemu ndi kukagonjetsa Gaza. (Zek. 9:5) Atafika ku Igupto, anakhazikitsa mzinda wa Alesandriya, umene unakhala malo a zamalonda ndi zamaphunziro. Atadutsanso ku Dziko Lolonjezedwa, iye anakagonjetsanso Aperisi kotheratu, ku Gogamela, pafupi ndi mabwinja a Nineve.

Atatero, Alesandro anatembenukira kum’mwera kukalanda Babulo, Susani (Susa), ndi Pesepoli—malikulu a Ufumu wa Perisiya. Kenako anadutsa dera la Perisiya mofulumira mpaka anakafika ku Mtsinje wa Indase, kudera limene panopa ndi Pakistan. Pa zaka zisanu ndi zitatu zokha, Alesandro anagonjetsa mbali yaikulu ya dziko linkadziŵika panthaŵi imeneyo. Koma m’chaka cha 323 B.C.E., ali ndi zaka 32, anamwalira ndi malungo ku Babulo.—Dan. 8:8.

Moyo wa Agiriki unakhudza kwambiri moyo wa Ayuda m’Dziko Lolonjezedwa. Agiriki ena amene kale anali asilikali a Alesandro anakhazikika kuderalo. Mmene zaka za zana loyamba zinali kufika, kuderalo kunali chigawo chokhala ndi mizinda yolankhula Chigiriki (Dekapole). (Mat. 4:25; Marko 7:31) Malemba Achihebri anali kupezeka m’Chigiriki. Chinenero chotchedwa Koine (Chigiriki cha anthu ŵamba) chinali kulankhulidwa kulikonse ndipo chinagwiritsidwa ntchito kufalitsira ziphunzitso zachikristu.

Ufumu wa Roma

Nanga kodi kumadzulo kunali kuchitika zotani? Roma—amene poyamba anali midzi yosiyanasiyana ku Mtsinje wa Tiber—anayamba kukula. M’kupita kwa nthaŵi, chifukwa cha luso lake pa zankhondo komanso chifukwa chokhala ndi boma pamalo amodzi, Roma anasesa madera onse olamulidwa ndi akazembe anayi a Alesandro. Mmene chaka cha 30 B.C.E. chimafika, zinali zoonekeratu kuti Ufumu wa Roma unali ndi mphamvu kwambiri. Kumeneku kunali kuyamba kuonekera kwa ‘chilombo choopsa’ chimene Danieli anaona m’masomphenya.—Dan. 7:7.

Ufumu wa Roma

Dera la Ufumu wa Roma linayambira ku Britain mpaka Kumpoto kwa Africa, komanso kuchokera ku Nyanja ya Atlantic mpaka ku Nyanja ya Perisiya. Popeza kuti ufumuwo unazungulira dera lonse la Mediterranean, Aroma anatcha nyanjayo Mare Nostrum (Nyanja Yathu).

Roma anakhudzanso moyo wa Ayuda, amene dziko lawo linali chigawo cha Ufumu wa Roma. (Mat. 8:5-13; Mac. 10:1, 2) Yesu anabatizidwa ndi kumwalira panthaŵi imene Mfumu Tiberiyo anali kulamulira. Olamulira ena achiroma anazunza Akristu mwankhanza koma sanagonjetse kulambira koona. Patapita zaka 1,300, ufumuwo unagonja poukiridwa ndi mitundu ya ku Germania kumpoto kwake komanso mitundu yoyendayenda kum’maŵa kwake.

[Mapu patsamba 26]

(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)

Ufumu wa Girisi

Alesandro atamwalira, akazembe ake anayi analamulira ufumu waukulu wonsewu

▪ Kasanda

▫ Lasamekasi

○ Tolemi Woyamba

• Selukasi Woyamba

A2 ▪ GIRISI

A2 ▪ Atene

A2 ▪ AKAYA

A3 ○ Kurene

A3 ○ LIBIYA

B2 ▫ Bezantiyamu

B3 ○ KUPRO

B4 ○ No-Amoni (Thebes)

C3 Palimelia (Tadimori)

C3 ○ Gerasa

C3 ○ Filadelfeya

C3 ○ Yerusalemu

C5 ○ Sevene

G2 • Alesandriya Margiana

Njira ya Alesandro

A2 ▪ MAKEDONIYA

A2 ▪ Pella

A2 ▫ THIRESI

B2 ▫ Troy

B2 ▫ Sarde

B2 ▫ Efeso

B2 ▫ Gordium

C2 ▫ Ankara

C3 • Tariso

C3 • Isase

C3 • Antiokeya (wa Suriya)

C3 ○ Turo

C4 ○ Gaza

B4 ○ IGUPTO

B4 ○ Mofi

B4 ○ Alesandriya

A4 ○ Mudzi wa Madzi wa Siwa

B4 ○ Mofi

C4 ○ Gaza

C3 ○ Tulo

C3 ○ Damasiko

C3 • Allepo

D3 • Nisibis

D3 • Gogamela

D3 • Babulo

E3 • Susani

E4 • PERISIYA

E4 • Pesepoli

E4 • Pasagade

E3 • MEDIYA

E3 • Akimeta

E3 • Rhagae

E3 • Hecatompylos

F3 • PARTI

G3 • ARIA

G3 • Alesandriya Areion

G3 • Alesandriya Prophthasia

F4 • DRANGIANA

G4 • ARACHOSIA

G4 • Alesandriya Arachosiorum

H3 • Kabul

G3 • Drapsaca

H3 • Alesandriya Oxiana

G3 • Drapsaca

G3 • BACTRIA

G3 • Bactra

G2 • Derbent

G2 • SOGDIANA

G2 • Maracanda

G2 • Bukhara

G2 • Maracanda

H2 • Alesandriya Eschate

G2 • Maracanda

G2 • Derbent

G3 • Bactra

G3 • BACTRIA

G3 • Drapsaca

H3 • Kabul

H3 • Takasila

H5 • INDIYA

H4 • Alesandriya

G4 • GEDROSIA

F4 • Pura

E4 • PERESIYA

F4 • Alesandriya

F4 • CARMANIA

E4 • Pasagade

E4 • Pesepoli

E3 • Susani

D3 • Babulo

[Malo ena]

A3 KRETE

D4 ARABIYA

[Nyanja]

B3 Nyanja ya Mediterranean

C5 Nyanja Yofiira

E4 Nyanja ya Perisiya

G5 Nyanja ya Arabiya

[Mitsinje]

B4 Nile

D3 Firate

D3 Tigirisi

G4 Indase

[Mapu patsamba 27]

(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)

Ufumu wa Roma

A1 BRITAIN

A3 SPANYA

B1 GERMANIA

B2 GAU

B2 ITALIYA

B2 Roma

B3 Kafeji

C2 ILURIKO

C3 GIRISI

C3 Akitumu

C3 Kurene

D2 Bezantiyamu (Kositantinopo)

D3 ASIYA MINA

D3 Efeso

D3 Allepo

D3 Antiokeya (wa Suriya)

D3 Damasiko

D3 Gerasa (Jarash)

D3 Yerusalemu

D3 Alesandriya

D4 IGUPTO

[Nyanja]

A2 Nyanja ya Atlantic

C3 Nyanja ya Mediterranean

D2 Nyanja Yakuda

D4 Nyanja Yofiira

[Chithunzi patsamba 26]

Atamanganso Raba, Tolemi Wachiŵiri anatcha mzindawo Filadelfeya. Mabwinja a bwalo lalikulu la Aroma adakaliko

[Chithunzi patsamba 27]

Mzinda wa Gerasa (Jarash) ku Dekapole

[Chithunzi patsamba 27]

Misewu ya Aroma, ngati msewu uwu umene uli pafupi ndi Allepo, inadutsa ku Ulaya, Kumpoto kwa Africa, ndi ku Middle East. Akristu anadutsa misewu imeneyi pofalitsa choonadi cha m’Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena