Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ukwati Wolemekezeka kwa Mulungu ndi kwa Anthu
    Nsanja ya Olonda—2006 | October 15
    • Ukwati Wolemekezeka kwa Mulungu ndi kwa Anthu

      “Panali ukwati m’Kana . . . ndipo Yesu . . . ndi akuphunzira ake anaitanidwa ku ukwatiwo.”​—YOHANE 2:1, 2.

      1. Kodi nkhani yonena za Yesu ali ku Kana imatiuza za chiyani?

      YESU, amayi ake, ndiponso ena mwa ophunzira ake ankadziwa kuti ukwati wolemekezeka wa anthu a Mulungu umakhala wosangalatsa. Ndipo Kristu anachititsa ukwati wina kukhala wapadera ndi wosangalatsa kwambiri mwa kuchita chozizwitsa chake choyambirira kulembedwa m’Baibulo. (Yohane 2:1-11) N’kutheka kuti mwasangalalapo kupita ku ukwati wa Akristu ofuna kutumikira Yehova monga banja losangalala. Kapena mwina mukuyembekezera kuchita ukwati woterowo kapena mufuna kuthandiza mnzanu kuti ukwati wake udzakhale wosangalatsa. Kodi n’chiyani chingathandize kuti zinthu zidzayende bwino?

      2. Kodi Baibulo lili ndi nkhani zotani zokhudza ukwati?

      2 Akristu aona kuti malangizo a m’Mawu ouziridwa a Mulungu n’ngothandiza kwambiri mwamuna ndi mkazi akamakonzekera ukwati. (2 Timoteo 3:16, 17) N’zoona kuti Baibulo lilibe mfundo zatsatanetsatane za mmene ukwati wachikristu uyenera kuchitikira. M’pomveka kuti silitero chifukwa miyambo ndi malamulo a boma amasiyanasiyana malinga ndi malo komanso nthawi. Mwachitsanzo, kalekale, ku Israyeli kunalibe mwambo wapadera wa ukwati. Tsiku la ukwati, mkwati ankatenga mkwatibwi n’kupita naye kunyumba kwake kapena kunyumba kwa atate ake. (Genesis 24:67; Yesaya 61:10; Mateyu 1:24) Ukwati unkachitika anthu akaonerera mwambowu. Sipankakhala mwambo wina wapadera monga momwe zimakhalira pa ukwati wa masiku ano.

      3. Kodi Yesu anathandizapo pa mwambo wotani ku Kana?

      3 Aisrayeli ankaona kuti munthu akachita zimenezi ndiye kuti wakwatira. Nthawi zina akatero ankachitanso phwando. Lemba la Yohane 2:1 limati: ‘Panali ukwati m’Kana.’ Koma mawu a chinenero choyambirira omwe anamasuliridwa kuti ukwati palembali, angakhale bwino kuwamasulira kuti “phwando la ukwati” kapena kuti “madyerero a ukwati.”a (Mateyu 22:2-10; Luka 14:8) Nkhaniyi imanena momveka bwino kuti Yesu analipo ndipo anathandizapo pa phwando la ukwati wachiyuda. Pamenepa, mfundo yaikulu n’njakuti, zomwe zinkachitika pa ukwati nthawi imeneyo n’zosiyana ndi zinthu zimene zimachitika masiku ano.

      4. Kodi Akristu ena amasankha kuchita ukwati wotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

      4 Masiku ano, m’mayiko ambiri muli malamulo amene Akristu ofuna kulowa m’banja amafunika kutsatira. Akatero, angathe kumangitsa ukwati wawo m’njira iliyonse yovomerezeka ndi boma. Angachite zimenezi mwina pa mwambo waung’ono ndiponso wosavuta kuutsatira wochititsidwa ndi woweruza milandu, meya, kapena mtumiki wachipembedzo wovomerezedwa ndi Boma. Ena amasankha kukwatira mwa njira imeneyi, mwina ataitana achibale kapena anzawo achikristu angapo kuti adzachitire umboni kapena kungofuna kuti adzasangalalire limodzi pa mwambo wofunika umenewu. (Yeremiya 33:11; Yohane 3:29) Komanso, Akristu ena angasankhe kuti asakhale ndi phwando lalikulu la ukwati lomwe lingafune zinthu ndiponso ndalama zambiri pokonzekera. M’malo mwake, angakonze zoitana anzawo apamtima ochepa kuti akhale nawo pa chakudya. Chilichonse chomwe tingasankhe kuchita pankhaniyi, tiyenera kuzindikira kuti Akristu ena okhwima maganizo angakhale ndi maganizo osiyana ndi athu.​—Aroma 14:3, 4.

      5. N’chifukwa chiyani Akristu ambiri akamakwatirana amafuna kukhala ndi nkhani ya ukwati, ndipo kodi nkhaniyi imakhala yotani?

      5 Akristu ambiri amasankha kuti pa ukwati wawo padzakambidwe nkhani ya m’Baibulo.b Amazindikira kuti Yehova ndiye anayambitsa ukwati ndipo m’Mawu ake anaikamo malangizo anzeru othandiza kuti banja liyende bwino komanso kuti likhale lachimwemwe. (Genesis 2:22-24; Marko 10:6-9; Aefeso 5:22-33) Ndiponso ambiri amafuna kuti anzawo komanso achibale awo achikristu asangalalire nawo limodzi pa mwambowo. Komano, kodi tiyenera kuona motani kusiyana komwe kulipo pa malamulo a boma, dongosolo, ngakhalenso miyambo ya ukwati yofala m’madera osiyanasiyana? Nkhani ino ifotokoza zimene zimachitika m’madera osiyanasiyana. Zina zingasiyane kwambiri ndi zimene inu mumadziwa kapena zomwe zimachitika m’dera lanu. Komabe, mupeza mfundo kapena zochitika zina zomwe ndi zofunika kwa atumiki onse a Mulungu.

      Ukwati Wotsatira Malamulo Umakhala Wolemekezeka

      6, 7. N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza zimene malamulo a boma amafuna pankhani ya ukwati, ndipo tingachite motani zimenezo?

      6 Ngakhale kuti Yehova ndiye anayambitsa ukwati, maboma a anthu ali ndi malamulo amene amafuna kuti anthu omwe akukwatirana awatsatire. M’poyenera kutsatira zimenezo. Yesu anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:17) Mtumwi Paulo nayenso analangiza kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.”​—Aroma 13:1; Tito 3:1.

      7 M’mayiko ambiri, Kaisara kapena kuti boma, ali ndi malamulo pankhani ya munthu woyenerera kukwatira kapena kukwatiwa. Motero, Akristu awiri amene ali omasuka mwa Malemba akasankha kuti akwatirane, amayesetsa kutsatira malamulo a dziko lawo. Mwina pangafunike kutenga mtchatho, kumangitsa ukwati pamaso pa munthu woimira boma pa za ukwati, ndipo mwinanso kukalembetsa m’kaundula, dongosolo lonse la ukwati likatha. Kaisara Augusto atalamula kuti pachitike ‘kalembera,’ Mariya ndi Yosefe anamvera lamulolo, n’kupita ku Betelehemu “kukalembedwa.”​—Luka 2:1-5.

      8. Kodi ukwati uli ndi mphamvu zotani, ndipo Mboni za Yehova zimachita chiyani posonyeza kuti zimamvetsa mfundo imeneyi?

      8 Akristu akakwatirana motsatira malamulo ndiponso movomerezeka, Mulungu amaona kuti mgwirizano wa anthu awiriwo wayamba kugwira ntchito. N’chifukwa chake Mboni za Yehova sizibwereza mwambo wa ukwati mwa kuchita miyambo yambirimbiri ya lamulo, ndiponso sizibwereza malumbiro a ukwati, monga pachikondwerero choti mwamuna ndi mkazi akwanitsa zaka 25 kapena 50 ali m’banja. (Mateyu 5:37) (Matchalitchi ena amanyalanyaza ukwati wolembetsa ku boma, n’kumati si ukwati weniweni pokhapokha wansembe kapena mbusa akachita mwambo wake kapena akalengeza kuti anthuwo akwatirana.) M’mayiko ambiri, boma limapatsa mtumiki wa Mboni za Yehova mphamvu zomangitsira ukwati. Ngati n’zotheka kutero, iye angafune kumangitsa ukwati panthawi ya nkhani ya ukwatiwo pa Nyumba ya Ufumu. Awa ndi malo a kulambira koona m’dera lililonse, ndipo ndi oyenera kukambiramo nkhani ya mwambo woterewu, umene unayambitsidwa ndi Yehova Mulungu.

      9. (a) Ngati ukwati wamangitsidwira ku boma, kodi mwamuna ndi mkazi wachikristu angasankhe kuchita chiyani? (b) Kodi akulu angakhudzidwe motani ndi ntchito yokonzekera ukwati?

      9 M’mayiko ena muli malamulo akuti mwamuna ndi mkazi azikamangitsa ukwati wawo ku maofesi a boma, monga ku maofesi a akuluakulu oyang’anira mzinda, kapena malamulo oti ukwati wawo azikaumangitsa pamaso pa munthu woimira boma. Nthawi zambiri Akristu amasankha kuti pambuyo pa mwambo wa lamulo umenewu akhale ndi nkhani ya ukwati pa Nyumba ya Ufumu tsiku lomwelo kapena tsiku lotsatira. (Safuna kuti kuchokera patsiku la mwambowo, padutse masiku ambiri asanakhale ndi nkhani ya m’Baibuloyo, chifukwa chakuti kwa Mulungu, anthu, ndiponso ku mpingo wachikristu, iwo amakhala atakwatirana mwa lamulo.) Ngati mwamuna ndi mkazi amene adzamangitsire ukwati wawo ku boma akufuna kudzakhala ndi nkhani pa Nyumba ya Ufumu, ayenera kupempheratu chilolezo kwa akulu a m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo. Kuwonjezera pa kutsimikizira kuti mwamuna ndi mkaziyo ali ndi mbiri yabwino, akulu amenewa amaonetsetsanso kuti nthawi ya ukwatiwo sikusokoneza misonkhano ya nthawi zonse ndiponso zinthu zina zimene zakonzedwa kudzachitikira pa nyumbayo. (1 Akorinto 14:33, 40) Amaonanso bwino pempho la akwatiwo la mmene adzakonzere Nyumba ya Ufumuyo, ndipo amaonanso ngati kungakhale kofunikira kulengeza za ukwatiwo.

      10. Ngati pangafunikire kukamangitsa ukwati ku boma, kodi nkhani ya ukwati ingakhudzidwe motani ndi zimenezi?

      10 Mkulu wokamba nkhaniyo amayesetsa kuikamba mwaubwenzi, mwaulemu ndiponso moti iwalimbikitse anthu mwauzimu. Ngati mwamuna ndi mkaziyo ayamba ndi kumangitsa ukwati wawo pamaso pa nthumwi ya boma, mkulu wokamba nkhaniyo ayenera kufotokoza momveka bwino kuti anthuwo anakwatirana mogwirizana ndi malamulo a Kaisara. Ngati pamwambo wa ku bomawo panalibe malumbiro a ukwati, mwamuna ndi mkaziyo angafune kuchita zimenezo m’kati mwa nkhaniyo.c Ngati analumbira kale pa mwambowo, koma mwamuna ndi mkazi ongokwatirana kumenewo akufuna kulumbira pamaso pa Yehova ndiponso mpingo, ayenera kugwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti analumbira kale, zomwe zingasonyeze kuti anthuwo ‘anamangidwa [kale] pamodzi.’​—Mateyu 19:6; 22:21.

      11. Kodi anthu amakwatirana motani m’madera ena, ndipo zimenezo zimakhudza motani nkhani ya ukwati?

      11 M’madera ena mulibe malamulo ofuna kuti mwamuna ndi mkazi akwatirane mwa mwambo winawake, ngakhalenso ofuna kumangitsira ukwati pamaso pa nthumwi ya boma. Ukwati umachitika iwo akapereka ku boma chikalata chosainidwa cholembetsera ukwati. Akatero, amalowetsa m’kaundula mtchatho wa ukwatiwo. Zikatero, anthu awiriwo amaonedwa kuti ndi mwamuna ndi mkazi wake, ndipo tsiku lomwe laikidwa pa mtchatho wawo ndilo limakhala tsiku la ukwati wawo. Monga momwe taonera kale, anthu amene akwatirana mwa njira imeneyi angafune kuti pambuyo polembetsa ukwati akhale ndi nkhani ya m’Baibulo pa Nyumba ya Ufumu. Mbale wokhwima mwauzimu amene wasankhidwa kukamba nkhaniyi amadziwitsa anthu onse obwera ku mwambowo kuti anthu awiriwo akwatirana kale chifukwa chakuti adula kale mtchatho. Malumbiro alionse ayenera kuchitika mogwirizana ndi zimene zafotokozedwa m’ndime 10 ndiponso m’mawu a m’munsi a ndimeyi. Anthu ofika pa Nyumba ya Ufumu adzasangalalira limodzi ndi akwatiwo ndiponso kupindula ndi malangizo a m’Mawu a Mulungu.​—Nyimbo ya Solomo 3:11.

      Ukwati Wotsatira Mwambo Komanso Womangitsa ku Boma

      12. Kodi ukwati wotsatira mwambo ndi ukwati wotani, ndipo m’pofunika kuchita chiyani pambuyo pa ukwati woterowo?

      12 M’mayiko ena, mwamuna ndi mkazi amatha kuchita ukwati wotsatira mwambo (kapena kuti chikhalidwe). Izi sizikutanthauza kungokhalira pamodzi kwa mwamuna ndi mkazi, kapena ukwati wina umene umangotengedwa ngati ukwati kumalo ena koma womwe si wovomerezeka mwa malamulo.d Koma ukwati wotsatira mwambo womwe tikunena pano ndi ukwati umene anthu alowa mogwirizana ndi miyambo yovomerezeka ndi mtundu kapena anthu ambiri m’dera lawolo. Mwa zina, mwina pangakhale kupereka ndi kulandira malowolo onse, ndipo akatero mwamuna ndi mkaziyo amakhala okwatirana mwalamulo komanso mogwirizana ndi Malemba. Boma limaona ukwati wa mwambo woterowo kuti ndi wovomerezeka, walamulo ndiponso woti sungathe wambawamba. Zimatheka kukalembetsa ku boma ukwati womwe wachitika motsatira mwambo, ndipo anthuwo akatero, mwamuna ndi mkaziyo amatha kupatsidwa mtchatho. Kulembetsa ukwatiwo kungateteze mwamuna ndi mkaziyo mwalamulo kapena kungathe kuteteza mkazi ngati mwamuna wamwalira ndiponso kungadzateteze ana m’tsogolo. Mpingo ungalimbikitse aliyense amene wakwatira motsatira mwambo kuti akalembetse mwamsanga ukwati wakewo. N’zochititsanso chidwi kuona kuti m’nthawi ya Chilamulo cha Mose, anthu ankalembetsa ukwati ndiponso kubadwa kwa mwana.​—Mateyu 1:1-16.

      13. Pambuyo pa ukwati wotsatira mwambo, kodi m’pofunika kuchitanji ndi nkhani ya ukwati?

      13 Anthu amene akwatirana mwalamulo pa ukwati wotsatira mwambo, amayamba kukhala mwamuna ndi mkazi wake akamangitsa ukwatiwo. Monga momwe taonera kale, Akristu amene akumangitsa ukwati wawo mwalamulo angafune kukhala ndi nkhani ya ukwati, komanso kupanga malumbiro a ukwati, pa Nyumba ya Ufumu. Ngati zatero, wokamba nkhaniyo ayenera kunena kuti anthuwo anakwatirana kale mogwirizana ndi malamulo a Kaisara. Nkhani imeneyi iyenera kukambidwa kamodzi basi. Ukwati wotsatira mwambo (chikhalidwe) komanso wovomerezeka ndi malamulo umenewu ndi umodzi, n’chifukwa chakenso pamakhala nkhani imodzi ya m’Malemba. Kuyesetsa kuti mwambo womangitsa ukwati ndi nkhani yake zisatalikirane kwambiri, mwina zichitike tsiku limodzi, kumathandiza kuti anthu m’deralo azilemekeza ukwati wachikristu.

      14. Kodi Mkristu angachite chiyani ngati n’zotheka kuchita ukwati wotsatira mwambo ndiponso womangitsa ku boma?

      14 M’mayiko ena kumene ukwati wotsatira mwambo umakhala wovomerezeka mwalamulo, mulinso dongosolo loti ukwati uzimangitsidwa ku boma. Ukwati womangitsa ku boma nthawi zonse umachitikira pamaso pa nthumwi ya boma, ndipo mwina pangachitike zinthu zonse ziwiri, kupanga malumbiro a ukwati ndiponso kusaina mu kaundula. Akristu ena amakonda ukwati womangitsira ku boma kusiyana ndi ukwati wotsatira mwambo. Palibe malamulo amene amafuna kuti munthu achite ukwati wa mitundu yonse iwiri; mtundu uliwonse wa ukwatiwu ndi wovomerezeka mwalamulo. Mfundo zimene tanena m’ndime 9 ndi 10 zokhudza nkhani ya ukwati ndiponso malumbiro, zimagwiranso ntchito pa ukwati wamtunduwu. Chachikulu n’chakuti mwamuna ndi mkaziyo akwatirana m’njira yolemekezeka kwa Mulungu ndiponso kwa anthu.​—Luka 20:25; 1 Petro 2:13, 14.

      Pitirizani Kukhala ndi Ukwati Wolemekezeka

      15, 16. Kodi ulemu uyenera kusonyezedwa motani mu ukwati?

      15 M’banja la mfumu ya ku Perisiya mutabuka mavuto, mlangizi wamkulu wa mfumuyo, dzina lake Memukana, anapereka malangizo abwino kwambiri akuti, ‘akazi onse azichitira amuna awo ulemu.’ (Estere 1:20) M’mabanja achikristu, malangizo amenewa sayenera kuchokera kwa mfumu iliyonse yaumunthu monga lamulo ayi. Akazi ayenera kulemekeza amuna awo. N’chimodzimodzinso ndi amuna achikristu, nawonso amalemekeza ndi kuyamikira akazi awo. (Miyambo 31:11, 30; 1 Petro 3:7) M’mabanja mwathu sitiyenera kuyembekezera kuti padutse zaka zambirimbiri tisanayambe kulemekezana. Tiyenera kuyamba kulemekezana tikangokwatirana, patsiku la ukwati lomwelo.

      16 Sikuti ndi mwamuna ndi mkazi wake yekhayo amene ayenera kusonyeza ulemu patsiku la ukwati. Ngati mkulu wachikristu adzakambe nkhani ya ukwati, nayonso nkhaniyo iyenera kukambidwa mwaulemu. Pokamba nkhani, azilankhula ndi mwamuna ndiponso mkaziyo. Popeza nkhaniyi imathandizira kupereka ulemu kwa anthu omwe akukwatiranawo, wokambayo sayenera kuikamo nthabwala kapena nthano. Sayenera kufotokozamo kwambiri maganizo ake omwe angachititse manyazi anthu omwe akukwatiranawo kapena anthu omvera. M’malo mwake, ayenera kuyesetsa kulankhula mwaubwenzi ndiponso molimbikitsa, ndipo asonyeze amene anayambitsa ukwati ndiponso malangizo Ake abwino kwambiri. Inde, nkhani yolemekezeka yomwe mkulu angakambe pa ukwati ingathandizire kuti ukwatiwo ukhale wolemekeza Yehova Mulungu.

      17. N’chifukwa chiyani Akristu amatsatira malamulo pa ukwati wawo?

      17 Mwachidziwikire, m’nkhaniyi mwaphunziramo mfundo zambiri za malamulo a ukwati. N’kutheka kuti mfundo zina sizingagwire ntchito mwachindunji m’dera lanu. Komabe, tonsefe tikufunika kuzindikira kufunika koti dongosolo la ukwati wa Mboni za Yehova lizisonyeza kuti timalemekeza malamulo a m’dziko mwathu, kapena kuti zofuna za Kaisara. (Luka 20:25) Paulo anatilimbikitsa kuti: “Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; . . . ulemu kwa eni ake a ulemu.” (Aroma 13:7) Inde, n’kofunika kuti Akristu, kungochokera patsiku la ukwati, azilemekeza zimene Mulungu akufuna kuti tizichita.

      18. Kodi m’pofunika kuganizira mbali iti ya ukwati imene anthu angasankhe kukhala nayo, ndipo nkhani zokhudza mbali imeneyi tingazipeze kuti?

      18 Pambuyo pa ukwati wachikristu pamakhala phwando, kapena kuti madyerero ake. Musaiwale kuti Yesu anapitapo ku phwando loterolo. Ngati pakonzedwa phwando loterolo, kodi uphungu wa m’Baibulo ungatithandize motani kuonetsetsa kuti phwandolo nalonso likhale lolemekeza Mulungu ndiponso losonyeza chitsanzo chabwino cha anthu okwatirana kumenewo ndi pa mpingo wachikristu? Nkhani yotsatirayi ifotokoza zimenezi.e

  • Kodi Zochita Zanu Zimatsimikizira Kuti Muli ndi Chikhulupiriro?
    Nsanja ya Olonda—2006 | October 15
    • Kodi Zochita Zanu Zimatsimikizira Kuti Muli ndi Chikhulupiriro?

      “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.”​—YAKOBO 2:17.

      1. N’chifukwa chiyani Akristu oyambirira ankafunika kuonetsetsa kuti chikhulupiriro ndi ntchito zawo ndi zabwino?

      ZOCHITA za Akristu oyambirira, zinatsimikizira kuti iwo anali ndi chikhulupiriro. Wophunzira Yakobo analimbikitsa Akristu onse kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha.” Ndipo anawonjezera kuti: “Monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.” (Yakobo 1:22; 2:26) Patatha zaka pafupifupi 35 chilembereni mawu amenewa, Akristu ambiri anali kupitiriza kutsimikizira kuti ali ndi chikhulupiriro mwa kuchita ntchito zabwino. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ena sankatero. Yesu anayamikira mpingo wa ku Smurna; koma anauza Akristu ambiri a mu mpingo wa ku Sarde kuti: “Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.”​—Chivumbulutso 2:8-11; 3:1.

      2. Kodi Akristu ayenera kumadzifunsa mafunso otani pankhani ya chikhulupiriro chawo?

      2 Motero, Yesu analimbikitsa Akristu a ku Sarde, ndiponso onse owerenga mawu ake, kuti apitirize kukonda choonadi chachikristu monga momwe ankachitira poyamba ndiponso kuti akhale maso mwauzimu. (Chivumbulutso 3:2, 3) Aliyense wa ife angadzifunse kuti: ‘Bwanji za zochita zanga? Kodi zochita zanga zonse, ngakhale pazinthu zimene sizikhudzana mwachindunji ndi ntchito yolalikira kapena misonkhano ya mpingo, zimasonyezeratu kuti ndikuyesetsa kutsimikizira kuti ndili ndi chikhulupiriro?’ (Luka 16:10) Pankhaniyi, pali zambiri zimene zimachitika m’moyo mwathu zomwe tingathe kuziganizira, koma tiyeni tikambirane chinthu chimodzi chokha, chomwe ndi mapwando, kuphatikizapo mapwando amene nthawi zambiri amachitika pambuyo pa ukwati wachikristu.

      Mapwando Ang’onoang’ono

      3. Kodi Baibulo limati chiyani pankhani yopezeka pa phwando?

      3 Ambirife timasangalala kuitanidwa ku phwando la Akristu anzathu. Yehova ndi ‘Mulungu wachisangalalo,’ yemwe amafuna kuti atumiki ake azisangalala. (1 Timoteo 1:11, NW) Iye anachititsa Solomo kulemba mfundo yoona iyi m’Baibulo, yakuti: “Ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m’vuto lake masiku onse a moyo wake.” (Mlaliki 3:1, 4, 13; 8:15) Kusangalala kumeneku kungachitike pa chakudya cha pabanja kapena pa phwando laling’ono la olambira oona.​—Yobu 1:4, 5, 18; Luka 10:38-42; 14:12-14.

      4. Kodi munthu amene akukonza phwando ayenera kuganizira za chiyani?

      4 Ngati mukukonza phwando loterolo, muyenera kuganizira mofatsa zimene mukukonzazo, ngakhale pa chakudya kapena kucheza komwe mukukonza zodzaitana okhulupirira anzanu ochepa chabe. (Aroma 12:13) Muyenera kudzaonetsetsa kuti ‘zonse zikuchitika koyenera,’ motsogoleredwa ndi “nzeru yochokera kumwamba.” (1 Akorinto 14:40; Yakobo 3:17) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. Khalani osakhumudwitsa.” (1 Akorinto 10:31, 32) Kodi n’zinthu zina ziti zimene mufunikira kuziganizira mosamala? Kuganizira zinthu zimenezo nthawi idakalipo, kungakuthandizeni kuonetsetsa kuti zochita zanu ndiponso za anthu oitanidwa kuphwandolo zidzasonyeze kuti mumachita zinthu zogwirizana ndi chikhulupiriro chanu.​—Aroma 12:2.

      Kodi Phwandolo Lidzakhala Lotani?

      5. N’chifukwa chiyani munthu akamakonza phwando ayenera kuganizira mosamala ngati akufuna kuti padzakhale mowa ndiponso nyimbo?

      5 Anthu ambiri akamakonza phwando amafunika kuganizira bwino kuti paphwandopo padzakhale mowa kapena ayi. Kuti phwando likhale losangalatsa, sikuti pamachita kufunikira mowa ayi. Kumbukirani kuti Yesu anapatsa chakudya gulu lina lalikulu limene linabwera kwa iye. Anachulukitsa mkate ndi nsomba. Nkhaniyi sinena kuti anapanga vinyo mozizwitsa, ngakhale tikudziwa kuti iye akanatha kuchita zimenezo. (Mateyu 14:14-21) Mukasankha kuti paphwando padzakhale mowa, onetsetsani kuti pasadzakhale mowa wambiri, komanso padzakhale zakumwa zina zimene anthu angakonde kumwa m’malo mwa mowawo. (1 Timoteo 3:2, 3, 8; 5:23; 1 Petro 4:3) Musapangitse munthu kukakamizika kumwa chakumwa chimene chingathe kumuluma “ngati njoka.” (Miyambo 23:29-32) Nanga bwanji za nyimbo? Ngati paphwando lanulo padzakhale nyimbo, mosakayikira mungasankhe nyimbo zake mosamala, poganizira kaimbidwe ka zida ndiponso mawu ake. (Akolose 3:8; Yakobo 1:21) Akristu ambiri aona kuti kuimba nyimbo za Ufumu za Kingdom Melodies kapenanso kuimbira limodzi pakamwa nyimbo zimenezi, kumachititsa kuti phwando likhale losangalatsa kwambiri. (Aefeso 5:19, 20) Ndipo, m’pofunikanso kuonetsetsa kuti sizinakwere kwambiri kuti zisasokoneze kucheza kapena zisasokoneze anthu oyandikana nawo nyumba.​—Mateyu 7:12.

      6. Kodi munthu amene wakonza phwando angasonyeze motani kuti ndi munthu wachikhulupiriro pankhani yocheza kapena pazochita zina?

      6 Paphwando, Akristu angathe kukambirana nkhani zosiyanasiyana, kuwerengerana nkhani mokweza, kapena kufotokozerana zinthu zochititsa chidwi zimene zawachitikira m’moyo. Anthu akayamba kukambirana nkhani zosayenera Akristu, munthu wokonza phwandolo angathe kuchita zinthu mosamala kuti anthuwo azikambirana nkhani zabwino. Ayeneranso kukhala maso kuti munthu wina asamangolankhula yekha, osapatsa anzake mpata. Akaona kuti zimenezi zayamba kuchitika, iye angathe kufotokoza maganizo ake mwanzeru, ndi kupereka mpata kwa enanso kuti alankhulepo. Angachite zimenezi, mwina mwa kupempha ana kuti nawonso alankhulepo kapena kuyambitsa nkhani imene anthu osiyanasiyana angalankhulepo. Ana ndi akulu omwe angasangalale ndi kucheza kotereku. Ngati, inuyo monga wokonza phwando, muchita zinthu mwanzeru ndi mosamala, ‘kufatsa kwanu kudzazindikiridwa’ ndi anthu omwe abwera paphwandopo. (Afilipi 4:5) Adzazindikira kuti ndinu munthu wachikhulupiriro, ndipo chikhulupirirocho chimakhudza mbali zonse za moyo wanu.

      Ukwati ndi Phwando Lake

      7. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuganizira mosamala za kukonzekera ukwati ndi phwando lake?

      7 Ukwati wachikristu ndi chimodzi mwa zinthu zapadera zosangalatsa kwambiri. Atumiki a Mulungu akale, kuphatikizapo Yesu ndi ophunzira ake, ankasangalala kukhala nawo pa chisangalalo choterocho, ndiponso pa phwando lake. (Genesis 29:21, 22; Yohane 2:1, 2) Koma masiku ano, pakhala pakuchitika zinthu zimene zasonyeza kuti pokonzekera phwando la ukwati, pamafunika kusamala kwambiri ngati munthu akufuna kuti phwando lotero lidzakhale labwino ndiponso logwirizana ndi mfundo zachikristu. Komabe, mapwando amenewa si achilendo ndipo amapatsa Akristu mwayi wosonyeza chikhulupiriro chawo.

      8, 9. Kodi zochitika pa maukwati ambiri zimatsimikizira motani zimene timawerenga pa 1 Yohane 2:16, 17?

      8 Anthu ambiri amene sadziwa ndiponso alibe ntchito ndi mfundo za Mulungu amaona kuti phwando la ukwati ndi nthawi yochita zinthu mopyola malire kapena yomwe anthu angaloledwe kuchita zinthu motero. M’magazini ina ya ku Ulaya, mkazi wina yemwe anali atangolowa kumene m’banja anafotokoza izi pankhani ya ukwati wake womwe anati unali waulemerero kwambiri. Anati: ‘Tinayenda pa ngolo ya akavalo anayi yomwe m’mbuyo mwake munali ngolo zina 12 za kavalo mmodzimmodzi ndiponso ngolo ina yaikulu, momwe munali bandi ikuimba nyimbo. Kenako tinadya chakudya chapamwamba kwambiri ndipo panali nyimbo zabwino kwambiri; zonse zinali zapamwamba kwambiri. Zimenezo n’zimene ndinkafuna, ndipo panalibenso munthu wondiposa.’

      9 Ngakhale kuti kachitidwe ka zinthu kangasiyane malinga ndi malo, maganizo amenewa akungotsimikizira zimene mtumwi Yohane analemba, kuti: “Chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.” Kodi mungayembekezere Akristu okhwima maganizo kufuna kukhala ndi ukwati waulemerero kwambiri ndiponso phwando lopambanitsa? Ayi. M’malo mwake, pokonzekera ukwati wawo afunika kuganizira malangizo akuti “iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.”​—1 Yohane 2:16, 17.

      10. (a) Kuti ukwati ukhale wabwino, n’chifukwa chiyani kukonzekera n’kofunika? (b) Kodi kusankha anthu oti aitanidwe kuyenera kuchitika motani?

      10 Mwamuna ndi mkazi wachikristu afunika kuchita zinthu molingalira bwino, ndipo Baibulo lingathe kuwathandiza pamfundoyi. Ngakhale kuti tsiku la ukwati n’lapadera, iwo amadziwa kuti langokhala chiyambi cha moyo wabanja wa Akristu awiri omwe akuyembekezera moyo wosatha. Sayenera kukakamizika kuchita phwando lalikulu la ukwati. Akasankha kuchita phwando, ayenera kuganizira mtengo wake ndiponso mtundu wa phwandolo. (Luka 14:28) M’banja lawo lachikristu, mwamuna adzakhala mutu mogwirizana ndi Malemba. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:22, 23) Motero, mkwati ndiye amene ali ndi udindo waukulu pa phwando la ukwati. N’zoona kuti poganizira munthu amene adzakhale mkazi wakeyo, iye angakambirane naye nkhani monga ya anthu amene akufuna kuwaitana kapena anthu amene angakwanitse kuwaitana ku phwando la ukwatilo. Mwina sangakwanitse kapena sizingakhale bwino kuitana anzawo ndi achibale onse; motero ayenera kusankha zochita zina modzichepetsa. Mwamuna ndi mkaziyo ayenera kuzindikira kuti ngati satha kuitana ena mwa Akristu anzawo, iwo adzamvetsa zimenezo ndipo sadzakhumudwa.​—Mlaliki 7:9.

      “Mkulu wa Phwando”

      11. Kodi “mkulu wa phwando” angagwire ntchito yotani pa ukwati?

      11 Ngati mwamuna ndi mkazi asankha kukhala ndi phwando lokondwerera ukwati wawo, kodi angatani pofuna kuonetsetsa kuti mwambowo udzakhale wopatsa ulemu? Kwa zaka zambiri tsopano, Mboni za Yehova zaona kufunika kokhala ndi munthu amene anatchulidwa m’nkhani ya phwando lomwe Yesu anachita nawo ku Kana. Paphwandolo panali “mkulu wa phwando,” amene mosakayikira ankalambirira limodzi mokhulupirika ndi eni ukwatiwo. (Yohane 2:8-10) Mofanana ndi zimenezi, mkwati wanzeru angapereke ntchito yofunika imeneyi kwa mbale wachikristu wokhwima maganizo. Atadziwa zofuna ndi zokonda za mkwati, mkulu wa phwandoyo angaonetsetse kuti zonsezo zikutsatiridwa, pokonzekera ndi pochita phwandolo.

      12. Kodi mkwati ayenera kuganizira chiyani pankhani yokhala ndi mowa pa ukwati?

      12 Mogwirizana ndi zomwe taona m’ndime 5, amuna ndi akazi ena amasankha kuti asakhale ndi mowa paphwando la ukwati wawo poopa kuti anthu angathe kusokoneza mwambowo ngati atamwa kwambiri. (Aroma 13:13; 1 Akorinto 5:11) Koma ngati akonza zodzakhala ndi mowa, mkwati ayenera kuonetsetsa kuti anthu asadzapatsidwe mowa wambiri, komanso kuti paphwandopo pasadzakhale mowa wambiri. Ku ukwati wa ku Kana komwe Yesu anapita, kunali vinyo ndipo iye anapanga vinyo wina wabwino kwambiri. N’zochititsa chidwi kumva zimene mkulu wa phwandolo ananena, kuti: “Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu [“ataledzera,” NW], pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.” (Yohane 2:10) Zoona zake n’zakuti Yesu sanalimbikitse anthu kuledzera, chifukwa ankadana nako. (Luka 12:45, 46) Podabwa ndi vinyo wabwino uja, mkuluyo anasonyeza kuti anaonapo nthawi zina pamene anthu obwera ku ukwati analedzera. (Machitidwe 2:15; 1 Atesalonika 5:7) Motero, mkwati ndiponso Mkristu wodalirika amene wasankhidwa kukhala mkulu wa phwando, ayenera kuonetsetsa kuti onse ofika pa phwandolo akutsatira malangizo omveka bwino awa, akuti: “Musaledzere naye vinyo, mmene muli chitayiko.”​—Aefeso 5:18; Miyambo 20:1; Hoseya 4:11.

      13. Kodi mwamuna ndi mkazi ayenera kuganizira chiyani ngati akukonza zoti adzakhale ndi nyimbo paphwando la ukwati, ndipo n’chifukwa chiyani?

      13 Mofanana ndi phwando lina lililonse, ngati padzakhale nyimbo, m’pofunika kusamala kuti voliyumu yake isadzalepheretse anthu kumvana. Mbale wina yemwe ndi mkulu mumpingo wachikristu anati: “Kukamada, kucheza kukayamba kukoma kwambiri kapena kuvina kukayamba, nthawi zina voliyumu ya nyimbo imakwera. Nyimbo zimene poyamba zinali kumveka chapansipansi, zimatha kukhala zaphokoso, mpaka anthu osatha kumvana. Phwando la ukwati limapereka mpata wabwino kwambiri wocheza. Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati nyimbo zingasokoneze mwayi umenewu!” Apanso, mkwati limodzi ndi mkulu wa phwando amafunika kuchita zinthu mwanzeru. Sayenera kusiyira abandi, kaya ndi olipidwa kapena ayi, kuti ndiwo asankhe mtundu wa nyimbo ndiponso voliyumu yake. Paulo analemba kuti: “Chilichonse mukachichita m’mawu kapena muntchito, chitani zonse m’dzina la Ambuye Yesu.” (Akolose 3:17) Anthu akabwerera kwawo pambuyo pa phwando (kapena madyerero) a ukwati ndi kukumbukira nyimbo za paphwandopo, kodi adzaona kuti mwamuna ndi mkaziyo achita chilichonse m’dzina la Yesu? Umu ndi mmene ziyenera kukhalira.

      14. Kodi n’zinthu ziti zokhudzana ndi ukwati zimene zimakhala zosaiwalika?

      14 Zoonadi, ukwati wokonzedwa bwino umakhala wosaiwalika. Adam ndi Edyta, omwe akhala m’banja zaka 30, anafotokozapo za ukwati wina kuti: “Zinkachita kuonekeratu kuti ndi mwambo wachikristu. Panali nyimbo zotamanda Yehova komanso zosangalatsa zina zabwino. Nyimbo ndi kuvina sizinali zofunika kwenikweni. Unali ukwati wabwino ndi wosangalatsa, ndipo chilichonse chinali chogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.” Kunena zoona, pali zambiri zimene mkwati ndi mkwatibwi angachite pa ukwati wawo posonyeza kuti ndi anthu achikhulupiriro.

      Mphatso za pa Ukwati

      15. Kodi ndi uphungu wa m’Baibulo wotani womwe ungagwiritsidwe ntchito pankhani ya mphatso za pa ukwati?

      15 M’mayiko ambiri mabwenzi ndiponso achibale amakonda kupereka mphatso kwa anthu amene akukwatirana. Ngati mukufuna kuchita zimenezi, kodi muyenera kukumbukira chiyani? Musaiwale mfundo ya mtumwi Yohane yonena za “matamandidwe a moyo.” Iye anagwirizanitsa kudzionetsera koteroko ndi ‘dziko lapansi limene likupita,’ osati ndi Akristu amene zochita zawo zimasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro. (1 Yohane 2:16, 17) Malinga ndi mfundo youziridwa yomwe Yohane anatchula, kodi anthu omwe angokwatirana kumene ayenera kulengeza mayina a anthu amene apereka mphatso ndiponso mphatso zawo? Akristu a ku Makedoniya ndi ku Akaya anapereka chithandizo kwa abale awo ku Yerusalemu, koma palibe pamene pamasonyeza kuti mayina awo analengezedwa. (Aroma 15:26) Akristu ambiri amene apereka mphatso pa ukwati angakonde kuti anthu asadziwe mayina awo, m’malo mofuna kudzionetsera. Pamfundoyi, onani uphungu wa Yesu womwe uli pa Mateyu 6:1-4.

      16. Kodi anthu omwe angokwatirana kumene angatani kuti asakhumudwitse anthu ena pankhani ya mphatso za pa ukwati?

      16 Kudziwitsa anthu mayina a amene apereka mphatso kungalimbikitse mpikisano wofuna kupereka mphatso yabwino ndi yokwera mtengo kwambiri. Motero, Akristu anzeru omwe angokwatirana kumene salengeza mayina a anthu amene apereka mphatso. Kulengeza mayinawo kungachititse manyazi anthu ena amene mwina sanathe kupereka mphatso. (Agalatiya 5:26; 6:10) N’zoona kuti palibe cholakwika kuti mkwati ndi mkwatibwi adziwe amene wapereka mphatso inayake. Iwo angathe kudziwa zimenezo kudzera pa khadi labwino lomwe munthu waperekera limodzi ndi mphatsoyo, koma osati n’cholinga choti awerengere anthu ayi. Pogula, popereka, ndi polandira mphatso za ukwati, tonse timakhala ndi mwayi wotsimikizira ngakhale pankhani yaing’ono ngati imeneyi, kuti ndife achikhulupiriro chomwe chimakhudza zochita zathu.a

      17. Kodi Akristu ayenera kukhala ndi cholinga chotani pankhani ya chikhulupiriro ndi ntchito zawo?

      17 Kutsimikizira kuti tili ndi chikhulupiriro kumafuna zambiri kuwonjezera pa kukhala akhalidwe labwino, kupita ku misonkhano yachikristu, ndiponso kugwira nawo ntchito yolalikira. Tiyeni tonse tikhale ndi chikhulupiriro champhamvu chomwe chimakhudza zonse zimene timachita. Inde, tingasonyeze chikhulupiriro chathu, mwa ntchito ‘zochitidwa mokwanira,’ kuphatikizapo mbali zosiyanasiyana zokhudza moyo wathu zomwe takambirana m’nkhani ino.​—Chivumbulutso 3:2, NW.

      18. Kodi mawu a pa Yohane 13:17 angagwire ntchito motani pankhani ya ukwati ndi phwando lachikristu?

      18 Yesu atasonyeza ophunzira ake okhulupirika chitsanzo chabwino mwa kugwira ntchito yonyozeka yosambitsa mapazi awo, anati: “Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.” (Yohane 13:4-17) Mwina kumadera omwe tikukhala masiku ano, kulibe mwambo wosambitsa mapazi a alendo panyumba pathu. Komabe monga momwe taonera m’nkhaniyi, nthawi zina timasonyeza chikhulupiriro chathu mwa kukhala achikondi, oganizira ena, kuphatikizapo pankhani zokhudza ukwati wachikristu kapena phwando lina lililonse. Tingachite zimenezi kaya tikukwatira, taitanidwa ku ukwati kapena phwando la ukwati wa Akristu omwe amasonyeza chikhulupiriro chawo mwa ntchito zawo.

      [Mawu a M’munsi]

      a Nkhani yotsatirayi yakuti, “Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri” yafotokoza mbali zina za ukwati ndiponso phwando lake.

      Kodi Mungayankhe Bwanji?

      Kodi mungatsimikizire motani chikhulupiriro chanu

      • pokonzekera phwando laling’ono?

      • pokonzekera ukwati kapena phwando la ukwati?

      • popereka kapena polandira mphatso za pa ukwati?

      [Chithunzi patsamba 24]

      Ngakhale poitana anthu ochepa chabe, lolani “nzeru yochokera kumwamba” kuti ikutsogolereni

  • Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2006 | October 15
    • Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri

      “TSIKU la ukwati wanga linali limodzi mwa masiku apadera ndi osangalatsa kwambiri pamoyo wanga,” anatero Gordon, amene wakhala pabanja zaka pafupifupi 60. N’chiyani chimachititsa tsiku la ukwati kukhala losangalatsa kwambiri kwa Akristu oona? Chifukwa chakuti ndi tsiku limene amapanga lumbiro lapadera kwa okondedwa awo, komanso kwa Yehova Mulungu. (Mateyu 22:37; Aefeso 5:22-29) Zoonadi, anthu amene akukonzekera ukwati amafuna kudzasangalala patsiku la ukwati wawo, koma amafunanso kulemekeza amene anayambitsa ukwati.​—Genesis 2:18-24; Mateyu 19:5, 6.

      Kodi mkwati angatani kuti mwambo wa ukwati wake ukhale wosangalatsa ndi wolemekezeka kwambiri? Kodi mkwatibwi angasonyeze motani ulemu kwa mwamuna wake ndiponso Yehova? Nanga anthu ena amene abwera pa ukwatiwo, angathandizire motani kuti tsikuli likhale losangalatsa kwambiri? Kuona mfundo zina ndi zina za m’Baibulo, kutithandiza kuyankha mafunso amenewa, ndipo kutsatira mfundo zimenezo kungachepetse mavuto amene angasokoneze mwambo wapaderawu.

      Ndani Ali ndi Udindo Waukulu Pokonzekera Ukwati?

      M’mayiko ambiri, atumiki a Mboni za Yehova angathe kuvomerezedwa kuti azimangitsa ukwati mwalamulo. Ngakhale m’madera amene anthu amafunika kumangitsa ukwati pamaso pa nthumwi ya boma, okwatiranawo angakonde kukhala ndi nkhani ya m’Baibulo. M’nkhani yoteroyo, mkwati amapemphedwa kukwaniritsa udindo umene Mulungu wam’patsa wokhala mutu wa banja. (1 Akorinto 11:3) Motero, mkwati ali ndi udindo waukulu pa zinthu zomwe zingachitike pa ukwatiwo. Ndipotu iye amakhalabe ndi udindo ngakhale pokonzekera dongosolo la mwambo wa ukwati ndiponso phwando lomwe lingachitike pambuyo pake. N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti mkwati akonze dongosolo limeneli?

      Chifukwa chimodzi n’chakuti achibale ake kapena achibale a mkazi angayese kumuumiriza kutsatira maganizo awo pokonzekera ukwatiwo. Rodolfo, yemwe wakhala akumangitsa ukwati wa anthu ena nthawi zambiri, anati: “Nthawi zina mkwati amakakamizika kuchita zina chifukwa cha achibale, makamaka ngati achibalewo athandiza ndalama zogwiritsa ntchito pa phwando la ukwati. Angathe kuumirira kuti pa mwambo wa ukwatiwo ndiponso pa phwando lake adzachite zimene iwo akufuna. Izi zingapeputse udindo wa m’Malemba womwe mkwatiyo ali nawo, wokhala ndi udindo waukulu pokonzekera ukwatiwo.”

      Max, amene wakhala akumangitsa ukwati kwa zaka zoposa 35, anati: “Ndaona kuti pali chizolowezi choti mkwatibwi ndiye amakhala patsogolo kusankha zoti zidzachitike pa mwambo wa ukwati ndiponso pa phwando lake, ndipo mkwati sapatsidwa mpata waukulu wopereka maganizo ake.” David, amenenso wamangitsa ukwati nthawi zambiri, ananena kuti: “Nthawi zina mkwati amakhala woti sanazolowere kutsogolera ndipo nthawi zambiri sakhudzidwa kwambiri ndi zokonzekera ukwati.” Kodi mkwati angatani kuti akwaniritse bwinobwino udindo wake?

      Kukambirana Kumawonjezera Chimwemwe

      Kuti mkwati akwaniritse bwinobwino udindo wake pokonzekera ukwati, ayenera kumakambirana bwino ndi anthu. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Zolingalira zizimidwa popanda upo.” (Miyambo 15:22) Koma, mavuto ambiri angathe kupewedwa ngati choyamba mkwati akambirana zimene akufuna kudzachita pa ukwati wawo ndi mkwatibwi, achibale, ndiponso anthu ena amene angam’patse malangizo abwino a m’Baibulo.

      Zoonadi, m’pofunika kwambiri kuti anthu otomerana azikambirana choyamba zimene akukonza ndiponso zimene akuona kuti ndi zotheka kudzachita pa ukwati wawo. Chifukwa chiyani? Taonani zina mwa zinthu zimene Ivan ndi mkazi wake Delwyn ananena. Iwo akhala mosangalala m’banja mwawo zaka zambiri ngakhale kuti anachokera kosiyana. Pokumbukira zimene anakonza kuti zidzachitike pa ukwati wawo, Ivan anati: “Ndinkadziwiratu zomwe ndinkafuna pa ukwati ndiponso pa phwando lake. Ndinkafuna kuti padzafike anzanga onse, tidzakhale ndi keke ya ukwati, ndiponso mkwatibwi wanga adzavale diresi loyera laukwati. Koma Delwyn ankafuna kuti padzakhale anthu ochepa. Ankafuna ukwati wosalira zambiri komanso wopanda keke. Ndipo ankaganiza zodzavala diresi wamba, osati laukwati.”

      Kodi Ivan ndi Delwyn anatani kuti agwirizane chimodzi? Anakambirana mokoma mtima ndiponso mosabisa mawu kukhosi. (Miyambo 12:18) Ivan anawonjezera kuti: “Tinawerenga nkhani za m’Baibulo zonena za ukwati, monga nkhani zolembedwa mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1984.a Nkhanizi zinatithandiza kuona mwambowu monga momwe Mulungu amauonera. Poganizira kuti tinali osiyana chikhalidwe, tinaona kufunika kosintha zina mwa zokonda zathu. Tonse tinasintha maganizo omwe tinali nawo.”

      Aret ndi Penny anachitanso chimodzimodzi. Ponena za tsiku la ukwati wawo, Aret anati: “Ine ndi Penny tinakambirana zomwe tinkafuna pa ukwati wathu, zomwe zinali zosiyana, ndipo tinafika pogwirizana chimodzi. Tinapemphera kwa Yehova kuti adalitse tsikuli. Ndinafunsiranso malangizo kwa makolo athu ndiponso mabanja ena okhwima maganizo mumpingo. Malangizo omwe anatipatsa anatithandiza kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti ukwati wathu ukhale wosangalatsa kwambiri.”

      Kuvala ndi Kudzikongoletsa Mopatsa Ulemu

      M’pomveka kuti mkwati ndi mkwatibwi amafuna kuvala bwino pa ukwati wawo. (Salmo 45:8-15) Iwo angagwiritse ntchito nthawi, mphamvu, ndiponso ndalama kuti apeze zovala zoyenera. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingawathandize kusankha zovala zopatsa ulemu ndiponso zabwino?

      Taganizirani zimene mkwatibwi amavala pa mwambowu. Ngakhale kuti anthufe timakonda zinthu zosiyanasiyana komanso zogwirizana ndi mayiko omwe tikukhala, malangizo a m’Baibulo amagwira ntchito kulikonse. Akazi amafunika ‘kudziveka chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso.’ Akazi achikristu amafunika kutsatira mfundoyi nthawi zonse, ndipo zikuphatikizanso patsiku la ukwati. Mfundo n’njakuti ukwati wosangalatsa sulira zovala zamtengo wapatali. (1 Timoteo 2:9; 1 Petro 3:3, 4) Kutsatira malangizo amenewa kumakhala ndi zotsatirapo zosangalatsa kwambiri.

      David, yemwe tam’tchula kale uja anati: “Amuna ndi akazi ambiri amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, ndipo n’ngofunika kuwayamikira. Koma nthawi zina mkwatibwi ndiponso womugwirizira amavala zovala zosapatsa ulemu, za khosi lalikulu mpaka kuonetsa mawere kapena zovala zoonetsa m’kati.” Mbale wina yemwe ndi mkulu ndiponso ndi Mkristu wokhwima maganizo, akamakumana ndi mkwati ndiponso mkwatibwi ukwati usanachitike, amawathandiza kuti asasokonezeke maganizo mwauzimu. Kodi amachita zimenezi motani? Mwa kuwafunsa ngati zovala zomwe akufuna kudzavala ndi zopatsa ulemu moti angathe kuzivala pa misonkhano yachikristu. N’zoona kuti kasokedwe ka zovala za ukwati kangakhale kosiyana ndi ka zovala zimene munthu amavala nthawi zonse ku misonkhano, ndipo zovala za paukwati zingakhale zogwirizana ndi mwambo wa m’dera lomwe timakhala, koma ziyenera kukhala zopatsa ulemu, ndiponso zogwirizana ndi miyezo yachikristu. Ngakhale kuti anthu m’dzikoli angaone ngati mfundo za m’Baibulo pankhani ya makhalidwe ndi zopondereza, Akristu oona n’ngokonzeka kulimbana ndi zimene dzikoli lingachite pofuna kuwakanikizira m’chikombole chake.​—Aroma 12:2; 1 Petro 4:4.

      Penny anati: “M’malo moona zovala kapena phwando kuti ndiye zinthu zofunika kwambiri, ine ndi Aret tinkaganizira kwambiri za mbali yauzimu ya mwambowu. Inali mbali yofunika kwambiri pa zinthu zomwe zinachitika patsikuli. Zinthu zapadera zimene ndimakumbukira, si zinthu zimene ndinavala kapena kudya, koma munthu amene ndinakhala naye tsikulo ndiponso chisangalalo chomwe ndinali nacho pokwatiwa ndi munthu amene ndimamukonda.” Mwamuna ndi mkazi wachikristu angachite bwino kuganizira zinthu ngati zimenezi pamene akukonzekera ukwati wawo.

      Nyumba ya Ufumu ndi Malo Olemekezeka

      Amuna ndi akazi ambiri achikristu amafuna kuti ukwati wawo ukachitikire m’Nyumba ya Ufumu ngati ilipo. Kodi n’chifukwa chiyani amakonda zimenezi? Banja lina linafotokoza maganizo ake motere: “Tinazindikira kuti ukwati ndi makonzedwe opatulika a Yehova. Kumangitsira ukwati m’Nyumba ya Ufumu, yomwe ndi malo athu olambiriramo, kunatithandiza kumvetsa poyamba pomwe kuti Yehova amafunika kukhala mbali ya ukwati wathu. Ubwino wina wochitira mwambowu m’Nyumba ya Ufumu, osati malo ena alionse unali wakuti zinasonyeza achibale athu omwe si Mboni amene anabwera pamwambowo kuti ifeyo timaona kulambira Yehova kukhala kofunika kwambiri.”

      Ngati akulu a pa Nyumba ya Ufumuyo avomera kuti m’nyumbayo muchitikire ukwati, mwamuna ndi mkaziyo ayenera kuwadziwitsa kudakali nthawi, zinthu zimene akuganiza kuti adzachite. Njira imodzi imene mkwati ndi mkwatibwi angasonyezere ulemu kwa anthu oitanidwa ku ukwatiwo ndi yoonetsetsa kuti afika panthawi yomwe inakonzedwa kuyambira mwambowo. Ndipo afunika kuonetsetsa kuti zonse zichitike mopatsa ulemu.b (1 Akorinto 14:40) Motero ayenera kupewa kuchita zinthu modzionetsera komwe kwafala m’maukwati ambiri a anthu amene si Mboni.​—1 Yohane 2:15, 16.

      Nawonso anthu odzakhala nawo pa ukwatiwo angasonyeze kuti amaona ukwati monga momwe Yehova amauonera. Mwachitsanzo, sangayembekezere kuti ukwatiwo upose maukwati ena achikristu, ngati kuti pali mpikisano wofuna kupeza ukwati wopambana kwambiri. Akristu okhwima maganizo amazindikiranso kuti kudzamvera nkhani ya m’Baibulo pa Nyumba ya Ufumu n’kofunika ndi kopindulitsa kwambiri kuposa kufika pa phwando limene lingakhalepo pambuyo pake. Ngati nthawi kapena zochitika zina zingapangitse kuti Mkristu apezeke pa mwambo umodzi wokha, mosakayikira angasankhe kukapezeka pa Nyumba ya Ufumu. Mkristu wina yemwe ndi mkulu, dzina lake William, anati: “Ngati anthu oitanidwa alephera kufika pa Nyumba ya Ufumu popanda zifukwa zomveka koma n’kukapezeka paphwando, zimasonyeza kuti samvetsa kupatulika kwa mwambowu. Ngakhale titapanda kuitanidwa ku phwando, tingathandize mkwati ndi mkwatibwi ndiponso kupereka umboni wabwino kwambiri kwa achibale omwe si Mboni amene abwera pa ukwatiwo, mwa kupezeka pankhani ya ukwatiwo pa Nyumba ya Ufumu.”

      Chisangalalo Chomwe Sichithera Patsiku la Ukwati

      Akatswiri amalonda achititsa kuti madyerero a ukwati akhale njira yopangira ndalama. Malinga ndi zomwe lipoti lina linanena posachedwapa, maukwati ambiri ku United States “amadya ndalama zokwana madola 22,000, kapena kuti theka la ndalama zonse zimene mabanja ambiri a ku America amapeza pachaka.” Chifukwa chotengeka ndi zonena za akatswiri amalonda, anthu ambiri ongokwatirana kumene kapena achibale awo amakhala ndi ngongole zikuluzikulu ndiponso zotenga zaka kuti abweze, kaamba ka tsiku limodzi limeneli. Kodi kumeneku n’kuliyamba mwanzeru banja? Anthu amene sadziwa kapena sasamala mfundo za m’Baibulo angasankhe kuchita zimenezi, koma Akristu oona satero ayi.

      Mwa kukhala ndi phwando laling’ono la ukwati ndiponso lomwe munthu angakwanitse, komanso mwa kuganizira kwambiri mbali yauzimu ya mwambowu, mabanja ambiri achikristu akwanitsa kugwiritsa ntchito nthawi yawo ndiponso ndalama zawo mogwirizana ndi kudzipereka kwawo kwa Mulungu. (Mateyu 6:33) Taonani chitsanzo cha Lloyd ndi Alexandra, amene apitiriza kuchita utumiki wa nthawi zonse, kwa zaka 17 chichitireni ukwati wawo. Lloyd anati: “Ena mwina anaona kuti ukwati wathu sunali wapamwamba, koma ine ndi Alexandra tinasangalala kwambiri. Tinkafuna kuti tsiku la ukwati wathu lisadzatilowetse m’mavuto aakulu a zachuma, koma lidzakhale tsiku lokondwera ndi zimene Yehova anakonza zopatsa chimwemwe chachikulu anthu awiri.”

      Alexandra anawonjezera motere: “Tisanakwatirane, ndinali kuchita upainiya, ndipo sindinkafuna kutaya mwayi umenewu chabe chifukwa chofuna kukhala ndi ukwati wopambanitsa. Tsiku la ukwati linali tsiku lapadera kwambiri. Komabe, linali chiyambi chabe cha moyo wokhalira limodzi. Tinatsatira malangizo oti tisaikire mtima kwambiri pa mwambo wa ukwati ndipo tinafufuza malangizo a Yehova okhudza moyo wathu wa banja. Yehova anatidalitsa chifukwa cha zimenezi.”c

      Inde, tsiku la ukwati wanu ndi tsiku lapadera. Maganizo ndi zochitika patsiku limenelo zingayale maziko a moyo wanu wa banja. Motero, dalirani malangizo a Yehova. (Miyambo 3:5, 6) Ganizirani kwambiri za mbali yauzimu ya tsikuli. Thandizanani pa udindo umene Mulungu anakupatsani. Mwa kuchita zimenezi, mungayale maziko olimba a ukwati wanu, ndipo chifukwa cha madalitso a Yehova, mudzapeza chisangalalo chomwe sichidzathera pa tsiku la ukwati lokha.​—Miyambo 18:22.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena