-
Nkhani Imene Ikudetsa Nkhawa Kwambiri MakoloGalamukani!—2007 | October
-
-
Nkhani Imene Ikudetsa Nkhawa Kwambiri Makolo
BANJA la a Phiri ndi akazi awo a Zione n’losangalala, ndipo lili ndi mwana wamwamuna wa zaka zitatu yemwe ndi wochenjera ndiponso wathanzi labwino.a Banjali limasamalira bwino kwambiri mwana wawoyu, komabe kusamalira bwino mwana si kophweka masiku ano. Munthu amene ali ndi mwana amadziwiratu kuti wasenza udindo waukulu ndiponso amakhala ndi nkhawa. Izi zili choncho chifukwa pali zinthu zambiri zimene ana ayenera kuphunzitsidwa. Bambo Phiri ndi akazi awo a Zione amada nkhawa kwambiri ndi udindo wawo wina, womwe ndi kuteteza mwana wawo kuti asachitidwe zachipongwe zosiyanasiyana zokhudza kugonana. N’chifukwa chiyani amada nkhawa choncho?
A Zione anati: “Bambo anga anali chidakwa chouma mtima. Ineyo pamodzi ndi azing’ono anga ankatimenya kwambiri ndiponso ankatigwiririra.”b Anthu ambiri amavomereza kuti nkhanza zoterezi zimasokoneza kwambiri maganizo a ana kwa moyo wawo wonse. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti a Zione akufunitsitsa kuteteza mwana wawo. Nawonso a Phiri akugwirizana ndi akazi awo pankhani imeneyi.
Makolo ambiri akuda nkhawa chifuwa cha kufala kwa khalidwe logona ana. N’kutheka kuti nanunso mukuda nkhawa, komano mwina simunaonepo zimene anaona a Phiri ndi a Zione. Komabe mwamvapo nkhani zambiri zovuta kumvetsa zokhudza khalidwe limeneli. Nkhani zimenezi sizinasiye malo padziko lonse ndipo zikudetsa nkhawa kwambiri makolo.
Motero n’zosadabwitsa kuti katswiri wina wofufuza nkhani imeneyi ananena kuti ili ndi “limodzi la makhalidwe ofoola nkhongono kwambiri amene ayamba kufala kwambiri masiku ano.” Izitu n’zomvetsa chisoni kwambiri, koma n’zosadabwitsa ngakhale pang’ono kwa anthu amene amawerenga Baibulo. Mawu a Mulungu amati tikukhala mu nthawi yovuta yotchedwa “masiku otsiriza,” imene anthu ake ndi “owopsa,” “odzikonda” ndiponso “opanda chikondi chachibadwa.”—2 Timothy 3:1-5.
Khalidweli ndi lochititsa nthumanzi kwambiri, moti makolo ena amachita kuima mutu akaganizira zoti anthu aipa kwambiri n’kufika pomachita kusakasaka ana kuti agone nawo. Koma kodi vutoli n’lalikulu kwambiri moti makolo sangathane nalo? Kapena kodi pali zinthu zimene makolo angachite kuti ateteze ana awo? M’nkhani zotsatirazi tikambirana mafunso amenewa.
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha maina munkhani zino.
b Akuluakulu ena amagona ana pofuna kukhutiritsa zilakolako zawo. Iwo kawirikawiri amachita zimene Baibulo limazitcha dama, kapena kuti por·neiʹa, zomwe zimaphatikizapo kuchita zinthu monga kuwaseweretsa maliseche, kuwagona, ndiponso kuwagona m’kamwa kapena kumatako. Zina mwa nkhanza zomwe akuluakulu amachita kwa ana ndi kuwasisita mabere, kuwanyengerera kuti achite nawo zopusa, kuwaonetsa zinthunzi zolaula, kuwaonera, ndiponso kuwaonetsa maliseche. Baibulo limaletsa zimenezi ndipo limazitcha ‘khalidwe lotayirira, lonyansa kapena ladyera.’—Agalatiya 5:19-21; Aefeso 4:19.
-
-
Mmene Mungatetezere Ana AnuGalamukani!—2007 | October
-
-
Mmene Mungatetezere Ana Anu
AMBIRIFE sitifuna kuganizira kwambiri za vuto la kugona ana. Makolo ambiri, safuna n’komwe kumva nkhaniyi. Koma vuto la kugona ana likudetsa nkhawa kwambiri masiku ano ndipo lafala kwabasi. Ana amene akumanapo ndi vutoli amasokonezeka kwambiri. Ndiye kodi n’zomveka kuti makolonu muzizemba nkhaniyi? Kodi simukuona kuti m’pofunika kudziwa bwino nkhani imeneyi kuti muteteze ana anu? Ndiyetu musaope kudziwa zoopsa zokhudzana ndi nkhaniyi chifukwa zimenezi zingakuthandizeni kuteteza ana anu.
Musalole kuti kufala kwa vuto la kugona ana kukufooleni. Dziwani kuti ana anu sangathe kudziteteza pawokha, motero musadziderere chifukwa inuyo ndi amene muli ndi mphamvu kuposa anawo ndipo pangafunike zaka zambiri kuti ana anu adzakhale ndi mphamvu zotero. Mukudziwa zinthu zambiri chifukwa mwakumana ndi zinthu zosiyanasiyana ndiponso muli ndi nzeru zambiri kuposa ana anu. Koma nkhani yagona pa kugwiritsira ntchito zinthu zimenezi poteteza ana anuwo. Tikambirana njira zitatu zimene makolo onse angatsatire pofuna kuteteza ana awo. Njira zake ndi izi: (1) Inuyo mukhale chitetezo choyamba kwa ana anu. (2) Phunzitsani ana anu za nkhani imeneyi mogwirizana ndi misinkhu yawo. (3) Phunzitsani ana anu njira zina zodzitetezera.
Kodi Inuyo Ndinu Chitetezo Choyamba kwa Ana Anu?
Amene ali ndi udindo woyamba woteteza ana ndi makolo osati anawo ayi. Motero, makolo ndiwo ayenera kuyamba kuphunzitsidwa, kenaka ana. Ngati muli ndi ana, pali zinthu zingapo zimene muyenera kudziwa zokhudza vuto la kugona ana. Muyenera kudziwa kuti ndi anthu otani amene amagona ana ndiponso kuti amagwiritsira ntchito njira zotani kuti awachite anawo zachipongwezi? Makolo ambiri akamaganizira za anthu ogona ana, amaganiza za anthu amene amabisalira ana n’cholinga chowaba ndi kuwagwiririra. Inde, anthu oterewa alipo ndithu. Nkhani zoterezi n’zotchuka m’manyuzi, pa TV, ndiponso pa wailesi. Koma zoterezi sizichitikachitika. Anthu ambiri amene amagona ana amakhala oti mwanayo akuwadziwa ndipo amawakhulupirira.
Ambirife sitingakayikire anzathu, aphunzitsi, azachipatala, kapena achibale powaganizira kuti iwowa angamalakelake kugona ndi ana athu. Ndipotu n’zoona kuti anthu ambiri alibe maganizo oipa ogona ana. Motero sibwino kukayikira wina aliyense. Komabe, mungathe kuteteza ana anu ngati mutadziwa njira zimene anthu ambiri ogona ana amagwiritsa ntchito.—Onani bokosi lomwe lili pa tsamba 6.
Kudziwa njira zimenezi kungakuthandizeni makolonu kuti mukhale chitetezo choyamba kwa mwana wanu. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati pali munthu winawake amene amakonda kwambiri ana kuposa akuluakulu ndipo amakonda kuti azikhala awiriwiri limodzi ndi mwana wanu wina? Mwina munthuyo amapita ndi mwana wanuyo koyenda, amam’patsa mphatso zosiyanasiyana, kapenanso amakonda kukuuzani kuti akhoza kukuthandizani kum’samalira mwana wanuyo. Kodi zikatero muzingoti basi ameneyo ndi wogona ana? Ayi, musamafulumire kuganiza zimenezo. N’kutheka kuti munthuyo ndi wamtima wabwino basi. Komabe, mwina zimenezi zingakuthandizeni kukhala maso. Baibulo limati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.
Musaiwale kuti anthu achinyengo amakhala ngati anthu abwino kwambiri. Choncho samalani kwambiri ndi munthu aliyense amene akudzipereka kuti azichita zinthu zinazake ndi mwana wanu pawokha. Ndi bwino kumuuza munthuyo kuti mungathe kutulukira nthawi iliyonse kuti muonane ndi mwana wanuyo. Bambo Andreya ndi a Linda, omwe ndi makolo achinyamata ali ndi ana aamuna atatu, ndipo amasamala kwambiri kuti asamasiye ana awowo ali wokhawokha ndi munthu wamkulu. Mmodzi wa ana awowo ankaphunzitsidwa zoimbaimba panyumba pawo pompo ndi mphunzitsi winawake wam’muna. A Linda anamuuza munthuyo kuti: “Pepani, ndizilowalowa m’chipinda muno mpaka mumalize.” Mwina mungaganize kuti makolowa anachita zinthu monyanyira, komatu anatero poopa kudzanong’oneza bondo.
Yesetsani kuti muzichita zinthu zosiyanasiyana limodzi ndi ana anu monga kucheza ndi anzawo ndiponso kuchita nawo ntchito ya kusukulu yochitira ku nyumba. Ngati mwana wanu akupita kwinakwake ndi anzake akusukulu kapena anthu ena, dziwani zonse zofunika kudziwa zokhudza kumene akupitako. Katswiri wina wothandiza anthu omwe ali ndi vuto la m’maganizo, yemwe wakhala zaka 33 akuthandiza anthu omwe anachitidwapo zachipongwe zoterezi, ananena kuti waonapo ana ambirimbiri amene sakanachitidwa zachipongwe zoterezi ngati makolo awo akanawateteza potsatira njira zinazake zosavuta. Iye anagwira mawu munthu wina amene anamangidwa chifukwa chogona ana. Munthuyo anati: “Makolo amachita kutipatsa okha ana awo. . . . Kunena zoona, ineyo sindinkavutika kupeza ana owagona.” Musaiwale kuti zidyamakanda zambiri zimakonda kupezerera ana osavuta kuwachita zachipongwe zoterezi. N’zovuta kupezerera ana amene makolo awo amayesetsa kuchita nawo limodzi zinthu zambiri.
Njira ina imene mungakhalire chitetezo choyamba kwa ana anu ndiyo kumamvetsera mosamala zimene akukuuzani. Nthawi zambiri ana saulula kuti achitidwa zachipongwe chifukwa cha manyazi ndi mantha. Motero, khalani osamala kwambiri kuti muone ngati pali china chilichonse chokayikitsa.a Mwana wanu akanena zinazake zokayikitsa, musapupulume. Mufunseni modekha kuti afotokoze bwinobwino. Akakuuzani kuti sakufuna kuti enaake amene amamusamalira apitirize kubwera, mufunseni chifukwa chake. Akakuuzani kuti munthu winawake wamkulu amachita naye masewera enaake amene mwanayo akulephera kuwafotokoza bwinobwino, mufunseni kuti: “Masewera ake ndi otani makamaka? Amakutani?” Akakuuzani kuti winawake amamugwiragwira, mufunseni kuti: “Amakugwiragwira pati?” Musamafulumire kuganiza kuti mwanayo akungonena zachibwana. Munthu amene amagona ana angauze mwanayo kuti, ngati ataulula palibe amene angamukhulupirire, ndipotu nthawi zambiri izi n’zimene zimachitikadi. Kwa mwana amene wachitidwa zachipongwe zoterezi, m’pofunika kwambiri kuti makolo akhulupirire zimene akuwauza. Zimenezi zimathandiza kuti mwanayo akhazikike maganizo.
Phunzitsani Ana Anu Nkhaniyi
Buku lina lonena za nkhani ya kugona ana linagwira mawu a munthu wina amene anamangidwa chifukwa chogona ana. Munthuyo anati: “Ndikapeza mwana amene sakudziwa chilichonse chokhudza zogonana ndimangoti, uwu ndi mwayi wanzama.” Mawu ochititsa nthumanziwa ayenera kuthandiza makolo kuona kuti nkhaniyi si yofunika kuitenga mwachibwana ayi. Ana amene sakudziwa chilichonse chokhudza nkhani ya kugonana savuta kuchitidwa chipongwe ndi anthu ogona ana. Baibulo limati kudziwa zinthu ndiponso kukhala ndi nzeru kungatiteteze kwa “anthu onena zokhota.” (Miyambo 2:10-12) Kodi simungafune kuti ana anu akhale otetezeka kwa anthu otero? Mukachita zimenezi tsatirani njira yachiwiri yofunika kwambiri yotetezera ana anu. Njira yake ndiyo kuwaphunzitsa za nkhani yofunikayi.
Komano kodi mungachite bwanji zimenezi? Makolo ambiri sakhala omasuka kukambirana ndi ana awo nkhani ya kugonana. Ana anu angakhalenso omangika kwambiri kukambirana nkhaniyi ndi inuyo ndipo n’zokayikitsa kwambiri kuti angaiyambitse n’komwe. Motero inuyo ndiye muyenera kuiyambitsa. A Linda anati: “Tinayamba kuwaphunzitsa za mayina a ziwalo zam’thupi adakali ana aang’ono kwambiri. Tinkawauza mayina enieni, osati mayina omwe ana amatchula. Tinkatero kuti anawo adziwe kuti nkhani yokhudza ziwalo zawo si yoseketsa kapena yochititsa manyazi.” Mukatero sizivuta kuyamba kuwaphunzitsa anawo zoti pali anthu omwe angathe kuwachita zachipongwe. Makolo ambiri amangouza ana awo kuti asamalole munthu aliyense kuwaonera, kapena kuwagwira zam’kabudula kapena m’diresi.
A Zione, omwe tawatchula m’nkhani yoyamba ija anati: “Ine ndi a Phiri tinauza mwana wathu kuti asamalole munthu aliyense kuona kapena kugwira chokodzera chake, ndiponso kuti si choseweretsa ayi. Tinamuuza kuti asamalole aliyense kuseweretsa chokodzeracho kaya ndi ineyo, bambo ake, ngakhalenso adokotala. Tikapita naye kuchipatala, ndinkamuuza kuti adokotala akungofuna kuti aone kuti zonse zili bwinobwino, motero mwina angathe kumugwira chokodzera.” Makolo onse azikhalapo pokambirana zimenezi ndi mwana wawo, ndipo azim’limbikitsa kawirikawiri kuti nthawi iliyonse angathe kuwauza ngati wina aliyense anamugwira m’njira yosayenera, kapena yomwe mwanayo sanasangalale nayo. Akatswiri a zosamalira ana ndi zopewa khalidwe logona ana amati ndi bwino kuti makolo onse azikambirana ndi ana awo m’njira imeneyi.
Anthu ambiri aona kuti buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Walusob n’lothandiza kwambiri pophunzitsa ana nkhani imeneyi. Mutu 32 wakuti, “Mmene Yesu Anatetezedwera,” umaphunzitsa ana molimbikitsa ndiponso momveka bwino za kuopsa kwa khalidwe logona ana ndiponso kuti m’pofunika kudziteteza. A Linda anati: “Bukuli latithandiza kutsendera m’maganizo a ana athu mfundo zimene takhala tikuwauza.”
Masiku ano, ana amafunika kudziwa kuti pali anthu ena amene amafuna kugwiragwira ana kapenanso kuti anawo aziwagwira iwowo malo osayenerera. Sikuti mukachenjeza ana anu za anthu amenewa ndiye kuti anawo azikhala mwamantha kapena asiya kukhulupirira anthu onse akuluakulu. A Zione anati: “Kupewa kuposa kuchiza. M’pofunika kwambiri kuti ana athu tiziwalangiza za nkhani imeneyi monga mmene timawalangizira za nkhani zina zosiyanasiyana. Mwana wathu titamulangiza za nkhaniyi sanayambe kuchita mantha ngakhale pang’ono.”
Pophunzitsa mwana wanuyo zimenezi, onetsetsani kuti akumvetsa kuti ayenerabe kukhala mwana womvera. Kuphunzitsa mwana kukhala womvera n’kofunika kwambiri koma si kophweka ayi. (Akolose 3:20) Ndipotu mukapanda kusamala mungathe kuchita zinthu monyanyira. Mwachitsanzo, si bwino kuuza mwana wanu kuti nthawi zonse azimvera chilichonse chimene munthu aliyense wamkulu akumuuza. Chifukwatu kutero n’kuika mwana wanuyo pangozi. Anthu ogona ana sachedwa kudziwa kuti mwana uyu amangomvera zilizonse. Makolo anzeru amaphunzitsa ana awo kuti asamangomvera zilizonse. Kwa Akhristu, iyi si nkhani yovuta kwambiri chifukwa amangofunikira kumuuza mwanayo kuti: “Ngati wina aliyense atakuuza kuti uchite zinthu zimene Yehova Mulungu amadana nazo, osalola ayi. Ngakhale n’takhala ineyo kapena bambo akowa, usamalole. Ndipo ngati winawake akufuna kuti uchite zinthu zolakwika uzimunenera kwa ineyo kapena kwa bambo ako.”
Potsiriza, langizani ana anu kuti asamalole aliyense kuwauza kuti asunge chinsinsi chinachake, osakuuzani inuyo. Auzeni kuti munthu aliyense akawauza kuti anawo asakuuzeni zinazake, azibwera kudzam’nenera. Ngakhale munthuyo atawaopseza, kapena ngakhale anawo atachita zolakwa zinazake pawokha, gogomezerani kuti asamaope ngakhale pang’ono kudzakuuzani. Musawauze malangizowa mowachititsa mantha ana anuwo. Atsimikizireni kuti anthu ambiri aakulu sangawachite zinthu zoterezi. Sangawagwiregwire malo osayenera, kuwauza kuti achite zinthu zosamvera Mulungu, kapena kuwauza kuti asauze makolo awo zinazake. Awa ndi malangizo ongothandiza kuti musadzanong’oneze bondo, ndipo mwina anawo sadzakumana ndi zoterezi ayi.
Phunzitsani Ana Anu Mmene Angadzitetezere
Njira yachitatu imene tikambirane ndiyo kuphunzitsa mwana wanu zinthu zingapo zosavuta zimene ayenera kuchita ngati munthu wina akufuna kumuchita zachipongwe inuyo palibe. Mungamuphunzitse njira imeneyi mokhala ngati mukuchita naye masewera. Inuyo mungamufunse kuti: “Ungatani ngati patachitika zakutizakuti?” Ndiyeno mwanayo ayankhe. Mwachitsanzo mungamufunse kuti: “Ungatani ngati titasowana mu msika? Kodi ungatani kuti undipeze?” Mwina mwanayo sangayankhe mmene mukufunira, koma mungathe kumuthandiza kuyankha molondola mwina pomuuza kuti: “Taganizira njira ina yabwino kuposa imeneyi.”
Mungathe kumufunsa mwana wanu mafunso ngati amenewa pomuphunzitsa njira yabwino kwambiri yoti azitsatira ngati munthu winawake atafuna kumugwira malo osayenera. Ngati mwana wanuyo amachita manyazi kwambiri akafunsidwa mafunso oterewa, mungathe kumuuza ngati kuti mukunena za mwana wina. Mwachitsanzo, mungamuuze kuti: “Tiyerekezere kuti kamtsikana kenakake kali ndi achibale, mwina amalume ake, ndiyeno iwowo akufuna kuyamba kukagwiragwira malo osayenera. Ukuganiza kuti kamtsikanako kayenera kutani kuti kadziteteze?”
Kodi mwana wanuyo muyenera kum’phunzitsa kuti azitani akakumana ndi zoterezi? Munthu wina wolemba mabuku anati: “N’zodabwitsa kuti njira imene imathandiza kwambiri ndiyo kukana mwamphamvu ponena kuti, “Choka!” kapena “Osandigwira!” kapenanso “Tandisiya!” Mwanayo akalankhula motere, anthu ofuna kum’chita zachipongwe amachita naye mantha n’kumusiya.” M’thandizeni mwana wanu kuyeserera kukuwa, ndi kuthawa mwamsanga, n’kudzakuuzani zonse zimene zachitikazo. Ngakhale mutaona kuti mwanayo wamvetsa bwinobwino zimene mwamuphunzitsazo, angathe kuiwala zonsezi pakangotha milungu kapena miyezi yochepa chabe. Motero muzimuphunzitsa mobwerezabwereza.
Anthu onse amene amathandiza pa ntchito yosamalira mwanayo, aakazi ndi aamuna omwe, kaya ndi abambo ake enieni, kaya omupeza, kapenanso wachibale wina aliyense, ayenera kukhalapo pom’phunzitsa zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa choti onse amene akukhalapo pophunzitsa mwanayo amakhala ngati kuti akulonjeza kuti iwowo sadzamuchita chipongwe chilichonse mwanayo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ana ambiri amachitidwa chipongwe choterechi ndi achibale awo. Nkhani yotsatirayi ifotokoza mmene mungatetezere banja lanu m’dziko la anthu amakhalidwe oipali.
[Mawu a M’munsi]
a Akatswiri ankhaniyi amanena kuti ngakhale kuti ana ambiri amene anachitidwapo chipongwe choterechi saulula, amachita zinthu zoonetsa kuti zinazake sizili bwino. Mwachitsanzo, mukaona mwana atayambanso mosadziwika bwino kuchita zizolowezi zimene anasiya kale, monga kukodza pamphasa, kusafuna kusiyana nanu, kapena kuopa kukhala yekha, dziwani kuti kalipokalipo. Koma sikuti mukangoona zimenezi basi ndiye kuti mwana wanu anachitidwa zachipongwe. Mufunseni mwana wanu modekha kuti akufotokozereni zimene zikumuvutitsa maganizo kuti muthe kumulimbikitsa, ndi kum’teteza bwinobwino.
b Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Khalani chitetezo choyamba kwa mwana wanu
[Mawu Otsindika patsamba 7]
Phunzitsani mwana wanu nkhani imeneyi
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Phunzitsani mwana wanu mmene angadzitetezere
[Bokosi patsamba 4]
VUTOLI N’LOFALA PADZIKO LONSE
Mu 2006, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations anapereka lipoti ku nyumba ya malamulo ya bungweli lofotokoza za ana amene akuchitidwa nkhanza padziko lonse. Lipotili linakonzedwa ndi katswiri wina amene bungweli linam’pempha kufufuza nkhaniyi. Lipotilo linati chaka china chaposachedwapa, atsikana pafupifupi 150 miliyoni ndiponso anyamata pafupifupi 73 miliyoni osakwanitsa zaka 18 “agwiriridwapo kapena kuchitidwa zachipongwe zina zotere.” Awatu ndi ana ambiri zedi, koma lipotili linati: “Chiwerengero chimenechi n’chochepa chifukwa n’chongoyerekezera chabe.” Ataunikanso zimene ofufuza anapeza m’mayiko 21 anapeza kuti m’madera ena pafupifupi akazi 36 pa akazi 100 aliwonse ndiponso pafupifupi amuna 29 pa amuna 100 aliwonse anachitidwapo zachipongwe zinazake zoterezi ali ana. N’zochititsa nthumanzi kuti ambiri mwa anthu amenewa anachitidwa zachipongwezi ndi wachibale.
[Bokosi patsamba 6]
ALI NDI NJIRA ZAWO ZOKOPERA ANA
Nthawi zambiri munthu wogona ana amakhala wochenjera kwambiri moti sachita kugwiririra anawo pogwiritsira ntchito mphamvu. Koma amakonda kuwanyengerera mwapang’onopang’ono. Amatero posankha mwana winawake amene akum’funa, ndipo amakonda ana amene ali osavuta kuwanyengerera, amene amangomvera zilizonse. Kenaka munthuyo amayamba kuchita zinthu zofuna kum’kopa mwanayo. Amayesanso kuchita zinthu zoti makolo a mwanayo azimukhulupirira. Nthawi zambiri anthu ogona ana amakhala akathyali odziwa kunamizira kuti amam’kondadi mwana wanuyo ndiponso kuti amakonda banja lanu.
Patsogolo pake, chidyamakandayo angathe kuyamba kunyengerera mwanayo pang’onopang’ono kuti mpaka adzafike podzamuchita zachipongwezo. Kenaka amayamba kumuchita mwanayo zinthu zinazake zooneka ngati zabwinobwino, monga kusewera naye masewera omagwetsana pansi ndiponso kum’girigisha. Angayambe kumam’patsa mphatso zikuluzikulu n’kuyamba kumakhala naye yekhayekha, popanda anzake, azibale ake ndiponso makolo ake. Kenaka angathe kumuuza mwanayo kuti asunge kachinsinsi kenakake, osauza makolo ake. Kachinsinsiko kangakhale kokhudzana ndi mphatso inayake imene akufuna kum’patsa kapena kukonza zopita naye kwinakwake kokayenda. Amagwiritsira ntchito njira zimenezi pofuna kulambula bwalo. Ndiyeno, munthuyo amayambapo zakezo akaona kuti mwana uja ndiponso makolo ake ayamba kum’khulupirira.
Komabe amayamba mosamala, ndipo sagwiritsa ntchito mphamvu ayi. Popeza kuti nthawi zina ana amafuna kudziwa zinthu zosiyanasiyana zokhudza kugonana, munthuyo angathe kupezerapo mwayi womuuza mwanayo zoti iyeyo azimuphunzitsa zimenezi ndipo angamuuze kuti azisewera masewera enaake odziwa awiri basi. Angathenso kumam’sonyeza mwanayo zithunzi zolaula kuti aziona ngati kuti palibe cholakwika kuchita zimenezo.
Akam’chita mwanayo zachipongwezo, amayesetsa kuti mwanayo asauze zimenezi munthu aliyense. Angatero pogwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana, monga kumuopseza kuti asayerekeze kuuza aliyense, komanso kuti akangotero akam’nenera zolakwa zinazake zimene mwanayo anachita pa nthawi ina. Mwinanso angathe kugwiritsa ntchito njira ziwiri zonsezi. Mwachitsanzo, munthuyo angamuuze kuti: “Wolakwa ndi iweyo. Sunandiuze kuti ndisiye.” Iye anganenenso kuti: “Ukangoyerekeza kuuza makolo ako, udziwe kuti akaitana apolisi kuti adzandigwire n’kukanditsekera kundende mpaka kalekale.” Mwinanso angamuuze kuti: “Zimenezi n’zodziwa awirife basi. Ukauza wina aliyense, palibe amene akhulupirire. Komanso samala, chifukwa ndikangomva zoti makolo ako adziwa zimenezi, ndiwachita zoopsa.” Pali njira zambirimbiri zaukathyali zimene achidyamakanda oterewa angagwiritsire ntchito.
[Chithunzi patsamba 5]
Muzikhala naye mwana wanu pa zochita zake zosiyanasiyana
[Chithunzi patsamba 7]
Musamachite manyazi kuphunzitsa mwana wanu nkhani zokhudza kugonana
[Chithunzi patsamba 8]
Phunzitsani mwana wanu kuchita zinthu molimba mtima ngati winawake akufuna kumuchita zachipongwe
-
-
Tetezani Ana M’Banja LanuGalamukani!—2007 | October
-
-
Tetezani Ana M’Banja Lanu
“OPANDA chikondi chachibadwa.” Baibulo limanena zimenezi pofotokoza mmene anthu ambiri alili “m’masiku otsiriza” ano. (2 Timoteyo 3:1, 3, 4) Kufala kwa vuto la kuchita chipongwe ana panyumba kukutsimikizira kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa. Kwenikweni, mawu a Chigiriki akuti asʹ-tor-gos, omwe m’Chichewa amati “opanda chikondi chachibadwa,” amasonyeza kusowa chikondi chimene chimayenera kukhalapo pakati pa achibale, makamaka pakati pa makolo ndi ana awo.a Ndipotu nthawi zambiri achibale ndi amene amachita ana zachipongwe zotere.
Ofufuza ena amati anthu ambiri amene amakonda kuchita ana zachipongwe amakhala bambo a anawo kapena mwamuna amene ali ndi udindo wa bambo pabanjapo. Komanso amuna ambiri amene ali achibale ndi amene amatha kum’chita mwanayo zachipongwe. Ambiri mwa ana amene amachitidwa zachipongwe ndi atsikana, koma zimenezi zimachitikanso ngakhale kwa anyamata ambiri. Ndipotu pali akazi ambiri amene amachita zachipongwe zoterezi tianyamata. Palinso ana ambiri amene amachitidwa zachipongwe ndi ana anzawo pakhomopo koma n’kutheka kuti sanena ayi. Mwina amachitidwa zachipongwezi ndi mkulu wawo kapena m’bale wawo wina yemwe amawapezerera. Kaya iyeyo ndi wamkazi kapena wamwamuna, angakakamize mlongo wake wamng’onoyo kuchita naye zopusa. N’zoona kuti zimenezi zingakunyanseni kwambiri monga makolo.
Kodi mungatani kuti mavuto ngati amenewa asachitike m’banja mwanu? N’zoonekeratu kuti aliyense m’banjamo ayenera kudziwa bwino mfundo zosiyanasiyana zoteteza ana kuti asachitidwe zachipongwe. Komanso aliyense azidziwa kufunika kwa mfundo zimenezi. Mfundo zothandiza kwambiri pankhani imeneyi zimapezeka m’Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo.
Zimene Mawu a Mulungu Amanena pa Nkhani ya Kugonana
Kuti ana akhale otetezeka m’banja lanu, m’pofunika kuti anthu onse m’banjamo azitsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino. Baibulo limanena mosapita m’mbali za nkhani ya kugonana. Limanena nkhaniyi mwaulemu, koma mosapsatira mawu. Limafotokoza kuti Mulungu anakonza zoti mwamuna ndi mkazi omwe anakwatirana ndiwo ayenera kugonana ndipo limati amenewa ndi madalitso. (Miyambo 5:15-20) Koma limaletsa kugonana popanda kukwatirana. Mwachitsanzo, Baibulo limaletseratu kugonana pachibale. Mu Levitiko chaputala 18, analembamo zinthu zosiyanasiyana zomwe Baibulo limaletsa zokhudza kugonana ndi wachibale. Taonani mawu awa: “Asasendere mmodzi wa inu kwa m’bale wake kum’vula [kapena kuti kugona naye]; ine ndine Yehova.”—Levitiko 18:6.
Yehova anaika khalidwe la kugonana ndi wachibale m’gulu la ‘zinthu zonyansa’ zimene chilango chake chinali imfa. (Levitiko 18:26, 29) N’zoonekeratu kuti Mlengi wathu ali ndi mfundo zapamwamba kwambiri pankhani imeneyi. Maboma ambiri masiku ano, amaona nkhaniyi chimodzimodzi ndipo akhazikitsa malamulo oletsa khalidweli. Malamulo a mayiko ambiri amati mwana akagonedwa ndi munthu wamkulu ndiye kuti wagwiriridwa. N’chifukwa chiyani amanena choncho ngakhale pamene mwanayo sanachite kum’kakamiza?
Maboma ambiri ayamba kuzindikira kuti zimene Baibulo linanena kalekale zokhudza ana n’zoona. Baibulo limati ana nthawi zambiri satha kuganiza ngati akuluakulu. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 22:15, limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” Ndipo mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali . . . kuganiza ngati kamwana, kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.”—1 Akorinto 13:11.
Zinthu zokhudza kugonana n’zoti mwana sangazimvetse, ndipo sangadziwe mmene kugonana kungakhudzire tsogolo lake. Motero, anthu ambiri amavomereza kuti, poti nzeru za mwana n’zopewera, n’zosamveka kunena kuti mwana angavomerezedi mwakufuna kwake kugonana ndi munthu winawake wamkulu. Kapena tinene kuti, munthu wamkulu, kapena mwana wina wosinkhukirapo, akagonana ndi mwana wamng’ono, sanganamizire kuti anachita zimenezi chifukwa choti mwanayo sanakane kapena kuti anafuna yekha. Mfundo imakhala yakuti mwanayo wachita kum’gwiririra basi. Nthawi zambiri chilango cha mlandu woterewu n’kutsekeredwa kundende. Pamenepa ndiye kuti munthu wamkuluyo ndiye ali ndi mlandu wogwiririra mwana wosalakwayo.
Komano n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri okhala ndi milandu yotereyi salangidwa n’komwe masiku ano. Mwachitsanzo, ku Australia akuti mwina ndi anthu 10 okha pa anthu 100 aliwonse ogona ana amene amaimbidwa mlandu, ndipo ndi ochepa chabe amene amalangidwa. M’mayiko enanso n’chimodzimodzi. Mabanja achikhristu sangadalire boma lokha kuti ndilo liziteteza ana awo, motero amagwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo chifukwa ndizo zili zothandiza kwambiri.
Akhristu oona amazindikira kuti Mulungu yemwe anachititsa kuti mfundo zimenezi zilembedwe m’Mawu ake sanasinthe ayi. Iyeyu amaona chilichonse chimene timachita, ngakhale zinthu zimene anthu ambiri sangathe kuziona. Baibulo limati: “Zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.”—Aheberi 4:13.
Tizidziwa kuti Mulungu amationa tikamaphwanya malamulo ake ndi kuchita zinthu zoipa kwa anzathu. Komanso, iye amatidalitsa tikamayesetsa kutsatira malamulo ake opindulitsa banja. Kodi ena mwa malamulo amenewa ndi ati?
Banja Lizikhala Logwirizana ndi Lachikondi
Baibulo limati chikondi ndi “chomangira umodzi changwiro.” (Akolose 3:14) Baibulo limafotokoza kuti chikondi si kudololedwa kokha ayi. Limati chikondi chimaonekera pa zinthu zimene munthu akuchita, kapena kuti khalidwe limene akusonyeza ndiponso zinthu zimene amadziletsa kuchita. (1 Akorinto 13:4-8) Kusonyezana chikondi m’banja kumatanthauza kulemekeza aliyense m’banjamo ndi kum’chitira zinthu mokoma mtima. Kumatanthauzanso kuti m’banjamo aliyense aziona mnzake mogwirizana ndi mmene Mulungu amamuonera. Mulungu anapatsa munthu aliyense m’banja udindo wofunikira.
Poti bambo ndiye mutu wa banja, iye ayenera kukhala patsogolo posonyeza chikondi. Iye amadziwa kuti kukhala bambo wachikhristu si chilolezo chochitira nkhanza mkazi kapena ana ake. M’malo mwake, iye amasonyeza umutu wake motsanzira Khristu. (Aefeso 5:23, 25) Motero iye amasamalira mkazi wake ndi kum’konda ndipo amaleza mtima ndi ana ake n’kumawakondanso kwambiri. Amawateteza nthawi zonse ndipo amayesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti anawo asaone zoopsa zilizonse, zomwe zingawasokoneze maganizo n’kuwachititsa kuti asamakhulupirire anthu ndiponso kuti azikhala mwamantha.
Mayi nayenso ali ndi udindo wosangalatsa ndiponso wolemekezeka. Pofotokoza mmene Yehova ndi Yesu amatetezera anthu, Baibulo limapereka chitsanzo cha mmene nyama zazikazi zimagwiritsira ntchito nzeru zachibadwa poteteza ana awo. (Mateyo 23:37) Choncho, nawonso amayi ayenera kuchita khama poteteza ana awo. Mwachikondi, mayi amaonetsetsa kuti ana ake akuwateteza kwambiri. Mayi kapena bambo sayenera kuchitirana nkhanza, kuzunzana, kuopsezana kapena kuchita zinthu zoterezi kwa ana awo. Komanso asamalole kuti ana awo azichita zimenezi kwa ana anzawo.
Munthu aliyense m’banjamo akamalemekeza anzake sizivuta kukambirana zinthu momasuka. Wolemba mabuku wina dzina lake William Prendergast anati: “Tsiku lililonse, makolo ayenera kukambirana zakukhosi ndi ana awo aang’ono kapenanso osinkhukirapo.” Iye anatinso: “Zikuoneka kuti imeneyi ndi njira yothandiza kwambiri pothetsa vuto la kugona ana.” Ndipotu izi n’zimene Baibulo limalimbikitsa. (Deuteronomo 6:6, 7) Mukamatsatira malangizo amenewa, aliyense panyumba panu amakhala womasuka kulankhula zakukhosi kwake, popanda kuopa chilichonse.
N’zoona kuti tikukhala m’dziko loipa ndipo n’zosatheka kuthandiza ana onse kuti asachitidwe zachipongwe. Komabe, kuika chitetezo chokwanira panyumba panu kungathandize kwambiri. Ndipo ngati winawake m’banjamo wachitidwa zachipongwe ndi anthu ena osakhala a m’banjamo, amadziwa kopita kuti akalimbikitsidwe. Pakhomo pakakhala potero, ana amakhala otetezekadi ngakhale kuti tikukhala m’dziko loipa. Yesetsani kuchita khama kuteteza ana pakhomo panu ndipo Mulungu adzakudalitsani.
[Mawu a M’munsi]
a Mabuku ena amamasulira mawu a Chigiriki chakalewa motere: “Kuumira mtima achibale.” Motero, Baibulo lina linamasulira vesi imeneyi motere: “Adzakhala . . . osowa chikondi cha pa abale awo.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]
NJIRA ZINA ZOTETEZERA ANA ANU PANYUMBA
Intaneti: Ngati ana anu amagwiritsa ntchito Intaneti, muyenera kuwaphunzitsa bwinobwino mmene angaigwiritsire ntchito mosamala. Pa Intaneti pali malo ambirimbiri okhala ndi zinthu zolaula, ndiponso malo amene anthu amatumiziranapo mauthenga. Zidyamakanda zimapezerapo mwayi pa malo oterewa n’kumatumiza mauthenga awo kuti zikope ndi kunyengerera tiana. Motero, n’chinthu chanzeru kuika kompyuta pamalo oonekera, kuti makolo azitha kuona bwinobwino zimene ana akuchita pa Intanetipo. Popanda kuyang’aniridwa ndi makolo, ana asamatumize zinthu monga adiresi yawo kapena nambala yawo ya foni kwa munthu aliyense amene amudziwira pa Intaneti.—Salmo 26:4.
Zakumwa Zoledzeretsa: Nthawi zambiri ana amene amachitidwa chipongwe ndi anthu ogona ana, amakhala kuti anamwetsedwa mowa. Odziwa bwino za nkhani ya kugona ana amati anthu amene amamwa kwambiri zakumwa zoledzeretsa nthawi zambiri satha kudziletsa; moti ena amachita zinthu zimene sangachite atakhala bwinobwino. Mulimonsemo, zimenezi zikuthandiza kuona ubwino wotsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizipewa kuledzera ndi kumwa mosadziletsa.—Miyambo 20:1; 23:20, 31-33; 1 Petulo 4:3.
Apatseni Ulemu: Mayi wina amakumbukira kuti: “Mayi anga atamwalira, ndi bambo anga okha amene chipinda chawo chinali ndi chitseko ndiponso makatani. Ena tonsefe tinalibe malo aliwonse okhala mobisika, ngakhale kubafa.” Bambo amene akunenedwayu ankawagona ana ake onse aakazi. Ngakhale achibale ayenera kudziwa kuti kupatsa ana ulemu n’kofunika kwambiri. Makolo amafuna kupatsidwa ulemu kuti azitha kuchita zinthu zina pa malo obisika. Ananso amafunanso kuti makolo aziwapatsa ulemu wotere akamakula. Makolo anzeru amachitira ena zinthu zimene amafuna kuti enawo aziwachitiranso iwowo.—Mateyo 7:12.
-