NYIMBO 51
Tadzipereka kwa Mulungu
Losindikizidwa
1. M’lungu wathu watikokera kwa Khristu
Kuti azititsogolera.
Tadziwa choonadi
M’lungu watiphunzitsa.
Tikufuna kuchita
Zofuna zake zokha.
(KOLASI)
Tadzipereka kwa Yehova Mulungu.
Ndife osangalala kwambiri
2. Tamulonjeza Yehova mu pemphero
Kuti tizimutumikira.
Tilidi ndi chimwemwe.
Timauzanso ena
Za dzina la Yehova
Ndi Ufumu wakenso.
(KOLASI)
Tadzipereka kwa Yehova Mulungu.
Ndife osangalala kwambiri
(Onaninso Sal. 43:3; 107:22; Yoh. 6:44.)