Nyimbo 202
Tadzipatulira kwa Mulungu!
1. Tayandikizitsidwa kwa Kristu ndi Ya.
Watitumizira cho’nadi.
Kuchoka kumwamba
Kuŵala kwafika.
Tadzikana ndipo
chidaliro chikukula.
Kwa M’lungu tadzipereka.
Tinasankha.
Tikondwa naye ndi Mwana’ke.
2. Onse odzipereka aphunzitsidwa;
Kukhala aminisitala.
Aimbadi onse
Nyimbo Yaufumu,
Mukhamu limodzi,
Popeza ndi a Mulungu.
Alumbiritsitsa mwakubatizidwa;
Nalalikira uthengawo.
3. Mwa kudzipereka kwathu tiyankhidwe
Tikhale ndi chikumbumtima.
Chimwemwe chambiri
Tichigaŵanetu
—Kusonyeza dzina.
Timfikire ndi pemphero.
Kwa M’lungu tadzipereka; tisamale
Tisunge kaimidwe kathu.