-
Kodi Ubwino Wowerenga Baibulo Ndi Wotani?Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI?
Kodi Ubwino Wowerenga Baibulo Ndi Wotani?
“Ndinkaganiza kuti Baibulo ndi lovuta kumvetsa.”—Jovy
“Ndinkaona ngati nkhani zake n’zotopetsa.”—Queennie
“Ndinkaona kuti Baibulo ndi lalikulu kwambiri moti sindinkafuna n’komwe kuliwerenga.”—Ezekiel
Kodi munaganizapo zowerenga Baibulo koma kenako n’kugwa ulesi mofanana ndi anthu amene tawatchula pamwambawa? Anthu ambiri amaona kuti sangakwanitse kuwerenga Baibulo. Koma kodi mungafune kuliwerenga mutadziwa kuti likhoza kukuthandizani kukhala ndi moyo wosangalala? Nanga mungamve bwanji mutadziwa kuti pali zinthu zimene zingakuthandizeni kuti kuwerenga Baibulo kuzikusangalatsani?
Taonani zimene anthu ena ananena atayamba kuwerenga Baibulo n’kuona ubwino wake.
Ezekiel, yemwe ndi wazaka za m’ma 20, anati: “Poyamba ndinkachita zinthu ngati munthu amene akuyendetsa galimoto popanda kwenikweni kumene akupita. Koma kuwerenga Baibulo kwandithandiza kukhala ndi moyo wabwino chifukwa lili ndi malangizo amene amandithandiza tsiku ndi tsiku.”
Mtsikana wina dzina lake Frieda, yemwenso ndi wazaka za m’ma 20, ananena kuti: “Sindinkachedwa kuyambana ndi anzanga. Koma panopa ndimatha kuugwira mtima chifukwa chowerenga Baibulo. Zimenezi zandithandiza kuti ndisamavutike kugwirizana ndi anthu ena, moti panopa ndili ndi anzanga ambiri.”
Mayi wina wazaka za m’ma 50, dzina lake Eunice, anati: “Baibulo landithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kusiya zinthu zoipa.”
Baibulo lingakuthandizeni kukhala ndi moyo wosangalala mofanana ndi mmene lathandizira anthu amene tawatchulawa komanso anthu ena ambiri. (Yesaya 48:17, 18) Mwachitsanzo, likhoza kukuthandizani kusankha zinthu mwanzeru, kupeza anzanu abwino, kuchepetsa nkhawa ndiponso kuphunzira mfundo zoona zokhudza Mulungu, chomwe ndi chinthu chofunika kwambiri. Malangizo a m’Baibulo amachokera kwa Mulungu ndipo sangakugwiritseni fuwa la moto. Zili choncho chifukwa Mulungu sangapereke malangizo olakwika.
Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuyamba kuwerenga Baibulo komanso kusangalala poliwerenga?
-
-
Kodi Ndingayambe Bwanji?Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI
Kodi Ndingayambe Bwanji?
Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzipindula powerenga Baibulo? Taonani mfundo 5 zimene zathandiza anthu ambiri.
Muzipeza malo abwino. Muziyesetsa kupeza malo aphee komanso opanda zinthu zimene zingakulepheretseni kuika maganizo pa zimene mukuwerenga. Malowo azikhala owala mokwanira ndiponso odutsa mpweya wabwino n’cholinga choti muzipindula ndi zimene mukuwerengazo.
Muzikhala ndi maganizo oyenera. Baibulo ndi lochokera kwa Atate wathu wakumwamba. Choncho mukamaliwerenga, mungachite bwino kukhala ndi maganizo ofanana ndi a mwana yemwe amafunitsitsa kuphunzira zinthu kwa bambo ake achikondi. Ngati muli kale ndi zikhulupiriro kapena maganizo enaake okhudza Baibulo, muziyesetsa kuti musamaganizire zimenezo powerenga. Zimenezi zingachititse kuti Mulungu azikuthandizani kuzindikira mfundo zoona.—Salimo 25:4.
Muzipemphera musanayambe kuwerenga. Maganizo amene ali m’Baibulo ndi a Mulungu. Choncho iyeyo ndi amene angatithandize kuti tilimvetse. Mulungu analonjeza kuti azipereka “mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Mzimuwu ungakuthandizeni kumvetsa maganizo a Mulungu. Mukapitiriza kumadalira mzimuwu, ukhoza kukuthandizani kumvetsa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”—1 Akorinto 2:10.
Muzimvetsa zimene mukuwerenga. Musamangoti bola kuwerenga. Muziganizira kwambiri zimene mukuwerengazo. Muzidzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi munthu wa m’nkhani imene ndawerengayi anali ndi makhalidwe abwino ati? Kodi ndingasonyeze bwanji makhalidwewa pa moyo wanga?’
Muzikhala ndi cholinga. Kuti muzipindula mukamawerenga Baibulo, muziyesetsa kuphunzira mfundo inayake imene ingakuthandizeni pa moyo wanu. Mukhoza kukhala ndi zolinga monga kuphunzira zinthu zambiri zokhudza Mulungu, kuphunzira mfundo zimene zingakuthandizeni kukhala munthu wabwino, kapena zimene zingathandize kuti banja lanu liziyenda bwino. Kenako mungasankhe nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kukwaniritsa zolingazo.a
Mfundo 5 zimenezi zingakuthandizeni kuyamba kuwerenga Baibulo. Koma kodi mungatani kuti kuwerengako kuzikhala kosangalatsa kwambiri? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.
a Ngati simukudziwa nkhani za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanu, a Mboni za Yehova angakuthandizeni.
-
-
Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI
Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?
Kodi mumaona kuti kuwerenga Baibulo n’kotopetsa, kapena kosangalatsa? Zimene mumachita powerenga n’zimene zingachititse kuti muzisangalala kapena ayi. Tiyeni tione zimene mungachite kuti muzisangalala powerenga Baibulo.
Muziwerenga Baibulo lolondola komanso losavuta. Ngati mutamawerenga Baibulo limene lili ndi mawu ambiri ovuta kapena akalekale omwe simukuwadziwa, kuwerengako sikungakusangalatseni. Choncho mungachite bwino kupeza Baibulo losavuta kumva limene lingakufikeni pamtima. Komabe muyenera kutsimikizira kuti Baibulolo linamasuliridwa molondola.a
Mungawerenge pogwiritsa ntchito chipangizo chamakono. Masiku ano mukhoza kuwerenganso Baibulo pa intaneti kapena kulichita dawunilodi kuti muziwerengera pakompyuta, tabuleti kapena pafoni. Mabaibulo ena amakhala ndi zinthu zokuthandizani kuona mwamsanga mavesi osiyanasiyana okhudza nkhani imene mukuwerenga komanso kuona mmene Mabaibulo ena anamasulirira mavesi amene mukuwerenga. M’zilankhulo zina, Baibulo limapezekanso longomvetsera. Anthu ambiri amakonda kumvetsera Baibulo akakwera basi, akamachapa kapena kuchita zinthu zina. Kodi mungayeseko zina mwa zinthu zimene tatchulazi?
Muzigwiritsa ntchito zinthu zothandiza pophunzira Baibulo. Pali zinthu zina zimene zingakuthandizeni kwambiri powerenga Baibulo. Mwachitsanzo, pali mapu a madera otchulidwa m’Baibulo omwe angakuthandizeni kudziwa pamene pali malo enaake ndiponso kumvetsa nkhani imene mukuwerenga. Nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda kapena za pachigawo chakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa” pawebusaiti ya jw.org, zingakuthandizeni kumvetsa nkhani zambiri za m’Baibulo.
Muzisinthasintha njira zowerengera. Ngati mumaona kuti kuwerenga Baibulo kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso n’kovuta, mukhoza kuyamba ndi nkhani imene imakusangalatsani kwambiri. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza anthu otchuka a m’Baibulo, mungayambe ndi kuwerenga za anthuwo. Mukhoza kuwerenga malemba amene ali m’bokosi lakuti “Anthu a M’Baibulo Amene Mungawerenge Nkhani Zawo.” Apo ayi, mwina mungafune kuwerenga malemba onse okhudza nkhani inayake kapena kuwerenga potsatira nthawi imene zinthu zinachitika. Mungachite bwino kuyesa imodzi mwa njira zimene tatchulazi.
a Anthu ambiri amaona kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ndi lolondola, lodalirika komanso losavuta kuwerenga. Baibuloli linapangidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezeka m’zilankhulo zoposa 130. Mukhoza kuchita dawunilodi Baibulo limeneli pawebusaiti ya jw.org kapena pa pulogalamu ya JW Library. Komanso ngati mungakonde, a Mboni za Yehova akhoza kukupatsani Baibuloli.
b Mabukuwa akupezeka m’Chingelezi.
-
-
Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI
Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?
Baibulo ndi lapadera kwambiri chifukwa lili ndi malangizo ochokera kwa Mlengi wathu. (2 Timoteyo 3:16) Uthenga wake ukhoza kutithandiza kwambiri. Ndipotu limanena kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheberi 4:12) Baibulo likhoza kutithandiza m’njira ziwiri. Lili ndi mfundo zotithandiza pa moyo wathu watsiku ndi tsiku komanso limatithandiza kudziwa Mulungu ndiponso zimene analonjeza.—1 Timoteyo 4:8; Yakobo 4:8.
Lingakuthandizeni pa moyo wanu panopa. Baibulo lingakuthandizeni pa zinthu zambiri. Mwachitsanzo, lili ndi malangizo okhudza:
Kugwirizana ndi anthu ena.—Aefeso 4:31, 32; 5:22, 25, 28, 33.
Zaumoyo.—Salimo 37:8; Miyambo 17:22.
Makhalidwe abwino.—1 Akorinto 6:9, 10.
Nkhani zachuma.—Miyambo 10:4; 28:19; Aefeso 4:28.a
Banja lina lachinyamata ku Asia linathandizidwa kwambiri ndi malangizo a m’Baibulo. Mofanana ndi anthu ambiri amene angolowa kumene m’banja, iwo ankavutika kuzolowerana komanso kukambirana zinthu momasuka. Koma kenako anayamba kugwiritsa ntchito zimene ankawerenga m’Baibulo. Kodi zimenezi zinawathandiza bwanji? Mwamuna wa m’banjali, dzina lake Vicent, anati: “Zimene ndinkawerenga m’Baibulo zinandithandiza kuthetsa mavuto a m’banja lathu mwachikondi. Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwatithandiza kukhala ndi banja losangalala.” Mkazi wake, dzina lake Annalou, ananenanso kuti: “Kuwerenga nkhani za anthu otchulidwa m’Baibulo kwatithandiza kwambiri. Panopa ndikuona kuti zinthu zikuyenda bwino m’banja lathu ndipo tonse tili ndi zolinga zabwino zimene tikufuna kukwaniritsa.”
Lingakuthandizeni kudziwa Mulungu. Kuwonjezera pa zimene ananena zokhudza banja lake, Vicent anati: “Ndimaona kuti kuwerenga Baibulo kwandithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kuposa kale.” Izi zikusonyeza kuti Baibulo lingakuthandizeni kuti mudziwe bwino Mulungu. Mukamawerenga Baibulo, malangizo a Mulungu amakuthandizani kwambiri ndipo mumayamba kuona kuti iye ndi mnzanu weniweni. Mudzaonanso kuti Mulungu anafotokoza zinthu zosangalatsa zokhudza nthawi imene tidzakhale ndi ‘moyo weniweni,’ womwe sudzatha. (1 Timoteyo 6:19) Kunena zoona, palibe buku lina lililonse lomwe lingafotokoze zimenezi.
Mukayamba kuwerenga Baibulo komanso kupitiriza kuchita zimenezi, mukhoza kupindula kwambiri. Mukhoza kukhala ndi moyo wosangalala panopa komanso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Komabe mukamawerenga Baibulo mukhoza kukhala ndi mafunso ambiri. Zikatero, muzikumbukira chitsanzo chabwino cha nduna ya ku Itiyopiya imene inakhala ndi moyo zaka zoposa 2,000 zapitazo. Ndunayi inali ndi mafunso ambiri okhudza nkhani za m’Baibulo. Iye atafunsidwa ngati ankamvetsa zimene akuwerenga, anati: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?”b Kenako analola kuti athandizidwe ndi Filipo, yemwe anali wophunzira wa Yesu ndipo ankadziwa bwino Baibulo. (Machitidwe 8:30, 31, 34) Ngati nanunso mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Baibulo, mukhoza kupita pawebusaiti ya www.pr418.com/ny n’kulemba fomu yopempha munthu woti aziphunzira nanu Baibulo. Mukhozanso kulemba kalata pogwiritsa adiresi yoyenera yomwe ili m’magaziniyi. Apo ayi, mungapeze a Mboni za Yehova amene muli nawo pafupi kapena mungapite ku Nyumba ya Ufumu yam’dera lanu. Mungachite bwino kwambiri kuyamba lero kuwerenga Baibulo n’kulola kuti lizikuthandizani pa moyo wanu.
Ngati mumakayikira zimene Baibulo limanena, tikukulimbikitsani kuti muonere vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? Mungapeze vidiyoyi mukapita pa jw.org/ny pamene palembedwa kuti MABUKU > MAVIDIYO > BAIBULO
a Kuti mudziwe malangizo ena amene ali m’Baibulo, pitani pawebusaiti yathu ya jw.org/ny pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.
b Onaninso nkhani yakuti “Kusamvetsa Zinthu Kukhoza Kutipweteketsa.”
-