Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 91 tsamba 212-tsamba 213 ndime 1
  • Yesu Anaukitsidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anaukitsidwa
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Anakumbukira Mwana Wake
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Manda Opanda Kanthu
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Yesu Ali Moyo
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali Ataukitsidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 91 tsamba 212-tsamba 213 ndime 1
Azimayi akudabwa kuona kuti m’manda a Yesu mulibe thupi lake

MUTU 91

Yesu Anaukitsidwa

Yesu atafa, munthu wina wachuma dzina lake Yosefe anapita kwa Pilato kukapempha kuti atenge thupi la Yesu n’kukaliika m’manda. Yosefe anapaka thupilo mafuta onunkhira n’kulikulunga munsalu yabwino kwambiri kenako n’kukaliika m’manda ochita kusema. Anagubuduza chimwala ndipo anatseka pakhomo la mandawo. Kenako ansembe aakulu anauza Pilato kuti: ‘Tikuganiza kuti ophunzira a Yesu akhoza kukaba thupi lake n’kumanama kuti wauka.’ Pilato anawauza kuti: ‘Pitani mukatseke kwambiri mandawo ndipo muikepo alonda.’

Patapita masiku atatu, azimayi ena analawirira kumandako ndipo anapeza kuti chimwala chija chachotsedwapo. M’mandamo munali mngelo ndipo anawauza kuti: ‘Musachite mantha. Yesu waukitsidwa. Pitani mukauze ophunzira ake kuti akakumane naye ku Galileya.’

Mariya Mmagadala anathamanga kukauza Petulo ndi Yohane kuti: ‘Thupi la Yesu labedwatu!’ Iwo anapita kumandako n’kukapezadi m’mandamo mulibe thupi la Yesu ndipo anabwerera kwawo.

Mariya atabwerera kumanda kuja anaona angelo awiri ali m’manda ndipo anawafunsa kuti: ‘Kodi Ambuye aja apita nawo kuti?’ Kenako anaona munthu wina ndipo ankaganiza kuti ndi wosamalira munda. Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Bambo, ngati ndinu mwawachotsa Ambuye ndiuzeni kumene mwawaika.’ Munthuyo atamuitana kuti: “Mariya!” anazindikira kuti anali Yesu. Choncho anafuula kuti: “Mphunzitsi!” ndipo anamugwira. Yesu anamuuza kuti: ‘Pita ukauze abale anga kuti wandiona.’ Nthawi yomweyo Mariya anapita kukauza ophunzira kuti waona Yesu.

Madzulo a tsiku lomwelo, ophunzira awiri ankayenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Emau. Ndiyeno munthu wina anayamba kuyenda nawo ndipo anawafunsa zimene ankakambirana. Iwo anati: ‘Kodi iwe sunamve? Masiku atatu apitawo ansembe aakulu anapha Yesu. Ndiye panopa azimayi ena akunena kuti ali moyo.’ Munthuyo anawafunsa kuti: ‘Kodi inu simukhulupirira zimene aneneri ananena? Pajatu anati Khristu adzafa kenako adzaukitsidwa.’ Munthuyo anawafotokozera Malemba osiyanasiyana. Atafika ku Emau, ophunzirawo anamupempha kuti apite nawo kwawo. Pa nthawi ya chakudya chamadzulo, munthuyo anapemphera ndipo anamuzindikira kuti anali Yesu. Kenako anasowa.

Nthawi yomweyo ophunzirawo anapita ku Yerusalemu ndipo anakalowa m’nyumba yomwe munali atumwi. Kumeneko anawafotokozera zimene zinachitika. Ali m’nyumbamo, Yesu anatulukira. Poyamba, atumwiwo sanakhulupirire kuti ndi Yesu. Koma iye anawauza kuti: ‘Onani manja angawa, ndigwireni kuti mutsimikize. Paja Malemba ananeneratu kuti Khristu adzaukitsidwa.’

“Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”​—Yohane 14:6

Mafunso: Kodi chinachitika n’chiyani azimayi atapita kumanda a Yesu? Kodi chinachitika n’chiyani pamsewu wopita ku Emau?

Mateyu 27:57-66; 28:1-10; Maliko 15:42-47; 16:1-8; Luka 23:50-56; 24:1-43; Yohane 19:38-42; 20:1-23

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena