Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yc phunziro 10 tsamba 22-23
  • Yesu Anali Womvera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anali Womvera
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Anaphunzira Kumvera
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Uyu Ndiye Mwana Wanga”
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • ‘Anaganizira Tanthauzo la Mawu Onsewo Mumtima Mwake’
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Phunzitsani Ana Anu
yc phunziro 10 tsamba 22-23
Yosefe ndi Mariya apeza Yesu ali m’kachisi

PHUNZIRO 10

Yesu Anali Womvera

Kodi umaona kuti kumvera makolo n’kophweka?— Nthawi zina zimakhala zovuta. Kodi ukudziwa kuti Yesu ankamvera makolo ake komanso Yehova?— Zimene iye ankachita zingakuthandize kuti nawenso uzimvera makolo ako ngakhale kuti nthawi zina zimakhala zovuta. Tiye tikambirane zambiri pa nkhani imeneyi.

Yesu asanabwere padziko lapansi ankakhala kumwamba ndi Atate ake, Yehova. Koma atabwera padziko lapansi anali ndi makolo ena. Mayina awo anali Yosefe ndi Mariya. Kodi ukudziwa kuti zinatheka bwanji kuti Yosefe ndi Mariya akhale makolo a Yesu?—

Yehova anatenga moyo wa Yesu n’kuuika m’mimba mwa Mariya kuti Yesu abadwe padziko lapansi. Zimenezi zinali zodabwitsa kwambiri. Yesu anakula m’mimba mwa Mariya ngati mmene ana onse amakulira. Patapita miyezi 9, Yesu anabadwa. Zimenezi ndi zimene zinachitika kuti Mariya ndi mwamuna wake Yosefe akhale makolo a Yesu.

Yesu ali ndi zaka 12 zokha anachita zinthu zosonyeza kuti amakonda kwambiri Atate wake, Yehova. Zimenezi zinachitika pa nthawi imene Yesu ndi makolo ake anayenda ulendo wautali wopita ku chikondwerero cha Pasika ku Yerusalemu. Pobwerera, Yosefe ndi Mariya anazindikira kuti Yesu wasowa. Kodi ukudziwa kuti anali kuti?—

N’chifukwa chiyani Yesu anapita kukachisi?

Yosefe ndi Mariya anabwerera msangamsanga ku Yerusalemu ndipo anamufufuza Yesu pena paliponse. Atalephera kumupeza, anadandaula kwambiri. Koma patadutsa masiku atatu, anamupeza ali m’kachisi. Kodi ukudziwa chifukwa chimene Yesu anapitira kukachisi?— Chifukwa ankadziwa kuti kukachisiko ndi kumene angaphunzire za Atate wake, Yehova. Yesu ankakonda kwambiri Yehova ndipo ankafuna kudziwa zimene angachite kuti azimusangalatsa. Atakula, Yesu anapitirizabe kumvera Yehova. Ankamveranso Yehova ngakhale pamene zinali zovuta moti ankalolera kuvutika. Kodi Yesu ankamveranso Yosefe ndi Mariya?— Inde, chifukwa Baibulo limanena kuti ankawamvera.

Kodi waphuzira chiyani pa chitsanzo cha Yesu?— Iwenso uyenera kumvera makolo ngakhale pamene kuchita zimenezi kuli kovuta. Kodi iweyo uzichita zimenezi?—

WERENGANI MAVESI AWA

  • Luka 1:30-35; 2:45-52

  • Aefeso 6:1

  • Aheberi 5:8

MAFUNSO:

  • Kodi zinatheka bwanji kuti Yosefe ndi Mariya akhale makolo ake a Yesu?

  • Kodi Yesu atasowa, makolo ake anamupeza ali kuti?

  • Kodi ukuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena