Mutu 5
“Uyu Ndiye Mwana Wanga”
MUNTHU ALI YENSE ali ndi atate. Inu muli ndi atate. Ndipo ine ndiri ndi atate. Pamene mtsikana amachita zinthu zabwino, atate wache amakondwera kuwauza ena kuti: “Uyu ndiye mwana wanga wamkazi.” Ndipo pamene mnyamata amachita chimene chiri choyenera, atate wache amanyadira kunena kuti: “Uyu ndiye mwana wanga.”
Yesu nthawi zonse amachita chimene chimakondweretsa Atate wache. Chotero Atate wache amakondwera naye. Ndipo kodi mukuchidziwa chimene Atate wa Yesu anachichita—Iye analankhula kuchokera kumwamba komweko kuwauza anthu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga.”
Yesu amawakondadi Atate wache. Iye anachisonyeza chimenechi ngakhale iye asandze ku dziko lapansi. Iye anali ndi malo odabwitsa kumwamba limodzi ndi Atate wache, Yehova Mulungu. Koma Mulungu anali ndi nchito yapadera kuti Yesu aichite. Kuti aichite nchito imeneyo, Yesu anafunikira kuchoka kumwamba. Iye anafunikira kubadwa monga khanda pa dziko lapansi. Yesu anali wofunitsitsa kuichita imeneyi chifukwa chakuti Yehova anamfuna iye kuichita iyo.
Kuti abadwe monga khanda pa dziko lapansi, Yesu anafunikira kukhala ndi mai. Kodi mukumdziwa amene iye anali—Dzina lache linali Mariya.
Yehova anamtuma mngelo wache Gabrieli kuchokera kumwamba kudzalankhula ndi Mariya. Gabrieli anamuuza Mariya kuti iye adzakhala ndi mwana wamwamuna. Mwanayo akachedwa Yesu. Kodi ndani amene akakhala atate wa mwanayo—Mngeloyo ananena kuti atate wa mwanayo akakhala Yehova Mulungu. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene Yesu akachedwera Mwana wa Mulungu.
Kodi mukuganiza kuti Mariya anamva motani ponena za chimenechi—Kodi iye ananena kuti, ‘Sindifuna kuchita chimenecho’? Kodi iye ananena kuti, ‘Sindifuna kukhala mai wa Yesu’?—
Ai, Mariya anali wokonzekera kuchita chimene Mulungu anafuna. Iye anali wofunitsitsa kwambiri kumumvetsera mngelo wa Mulungu. Kunali ngati kumvetsera Mulungu! Ndipo Mariya anafuna kumumvetsera Mulungu. Iye anamkonda Mulungu ndipo anali wokondwa kuchita chimene Yehova Mulungu anamfuna iye kuchita.
Koma kodi ndi motani mmene Yehova akadamchititsira Mwana wache kumwamba kuti abadwe monga khanda pa dziko lapansi—Yehova ali wamphamvu kopambana kuli konse. Iye angathe kuzichita zinthu zimene palibe wina ali yense angazichite. Chotero Yehova anautenga moyo wa Mwana wache kuchokera kumwamba ndi kuuika uwo m’mimba mwa Mariya. Yesu anayamba kukula m’mimba mwa Mariya monga momwe makanda ena amakulira m’mimba mwa amai ao. Pambuyo pa chimenecho Mariya anakwatiwa ndi Yosefe.
Ndiyeno nthawi inafika yakuti Yesu abadwe. Iye anabadwira mu mzinda wa Betelehemu. Mariya ndi mwamuna wache Yosefe anali kumauchezera mzinda umenewo. Koma Betelehemu anali wodzaza ndi anthu. Munalibe ngakhale chipinda kumene Mariya ndi Yosefe akadakhala pa usiku umene Yesu anabadwa. Iwo anakakamizika kuliika khandalo Yesu modyera ng’ombe. Modyera ng’ombe ndiwo malo m’mene mumakhala chakudya kaamba ka ng’ombe ndi nyama zina kuti zidye.
Zinthu zodabwitsa zinachitika pa usiku umene Yesu anabadwa. Pafupi ndi Betelehemu mngelo analankhula ndi abusa ena. Iye anawauza abusawo mmene Yesu analiri munthu wofunika. Iye anati kwa iwo: ‘Taonani ine ndiri kukuuzani inu mbiri yabwino imene idzawapangitsa anthu kukhala achimwemwe. Lero munthu wina anabadwa amene adzawapulumutsa anthu.’ Yesu akawachitira zinthu zabwino zambiri anthu amene amamkonda Mulungu.—Luka 2:10, 11.
Imeneyi inali mbiri yabwino! Angelo ena kumwamba anayamba kugwirizana pamodzi m’kumamtamanda Mulungu. Iwo anali achimwemwe! Abusawo anatha kumva zimene iwo anazinena.
Tsopano abusawo anafuna kumuona Yesu. Mngeloyo anawauza iwo kuti iwo akadatha kumpeza Yesu mu Betelehemu. Chotero iwo anapita kumeneko. Pamene abusawo anafika kumeneko kudzamuona Yesu, iwo anamuuza Yosefe ndi Mariya zinthu zonse zabwino zimene iwo anazimva. Ichi chinampangitsa Yosefe ndi Mariya kukhala othokoza kwambiri kwa Mulungu. Kodi mungayerekezere chimwemwe chache chimene Mariya anali nacho kuti iye adakhala wofunitsitsa kukhala mai wa Yesu?
Pambuyo pache, Yosefe ndi Mariya anamtengera Yesu ku mzinda wa Nazarete. Kumeneko ndiko kumene Yesu anakulirako. Pamene iye anali wamkulu, iye anayamba nchito yache yaikuru yophunzitsa. Imeneyi inali mbali ya nchito imene Yehova Mulungu anamfuna Mwana wache kuichita pa dziko lapansi.
Pafupifupi zaka zitatu pambuyo pache, Yesu ndi ena a atsatiri ache anakwera pamwamba pa phiri lalitari. Kodi nchiani chimene chinachitika pamenepo?—Pamene enawo anali chipenyere, zobvala za Yesu zinayamba kuwala monyezimira. Ndiyeno mau a Mulungu mwini anamvedwa. Yehova anati ponena za Yesu: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa.” Mulungu anali wokondwera ndi Mwana wache.—Marko 9:2-8.
Yesu nthawi zonse anachita chimene chinali choyenera. Iye sanayerekezere kukhala munthu wina amene iye kwenikweni sanali. Iye sanawauze anthu kuti iye anali Mulungu. Mngelo Gabrieli anali atamuuza Mariya kuti Yesu akachedwa Mwana wa Mulungu. Yesu mwiniyo ananena kuti iye anali Mwana wa Mulungu. Ndipo iye sanawauze anthu kuti iye anadziwa zochuruka koposa Atate wache. Iye anati: “Atate ali wamkuru ndi Ine.”—Yohane 14:28.
Pamene Atate wa Yesu anampatsa iye nchito kuti aichite, Yesu anaichita iyo. Iye sananene kuti, ‘Inde, ndidzaichita,’ koma kenaka kuchita kanthu kenanso. Iye anamkonda Atate wache. Chotero iye anamvetsera chimene Atate wache anachinena.
Ifenso tikufuna kumkondweretsa Yehova, ati—Pamenepo ife tiyenera kusonyeza kuti ife timamumvetseradi Mulungu, monga momwe Yesu anachitira. Mulungu amalankhula kwa ife kupyolera m’Baibulo. SIkukakhala koyenera kuyerekezera kumumvetsera Mulungu, koma kenaka kukhulupilira ndi kuchita zinthu zimene ziri zosemphana ndi Baibulo, kodi kukakhala koyenera—Ndipo kumbukirani kuti, ife sitidzakupeza kukhala kobvuta kumkondweretsa Yehova ngati ife timkondadi iye.
(Malemba ena omasonyeza chifukwa chache ife tifunikira kuchidziwa ndi kuchikhulupilira chimene Baibulo limachinenadi ponena za Yesu: Mateyu 7:21-23; 1 Timoteo 2:5, 6 ndi Yohane 4:25, 26.)