-
Yesu Anakhala MesiyaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 74
Yesu Anakhala Mesiya
Yohane ankalalikira kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwera.’ Yesu ali ndi zaka 30 anapita kumtsinje wa Yorodano kumene Yohane ankabatiza anthu. Pa nthawiyi Yesu ankachokera ku Galileya. Iye ankafuna kuti Yohane amubatize koma Yohaneyo anati: ‘Ayi, ine si woyenera kubatiza inu. Inuyo ndi amene mukuyenera kundibatiza ine.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Yehova akufuna kuti undibatize.’ Choncho anapita mumtsinje wa Yorodano ndipo Yohane anabatiza Yesu pomuviika thupi lonse m’madzi.
Yesu atavuuka m’madzimo anayamba kupemphera. Ndiyeno kumwamba kunatseguka ndipo mzimu wa Mulungu wooneka ngati nkhunda unatsika n’kudzamutera. Kenako Yehova analankhula ali kumwamba kuti: “Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.”
Mzimu wa Mulungu utafika pa Yesu, Yesuyo anakhala Khristu kapena kuti Mesiya. Tsopano anali wokonzeka kuyamba kugwira ntchito imene Mulungu anamutuma.
Yesu atangobatizidwa anapita m’chipululu ndipo anakhalamo masiku 40. Atachoka m’chipululumo anapita kukaona Yohane. Yohane ataona Yesu akubwera poteropo anati: ‘Uyu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.’ Apa Yohane ankafuna kuti anthu adziwe kuti Yesu ndi Mesiya. Koma kodi ukudziwa zimene zinachitika pamene Yesu anali kuchipululu? Tiona m’mutu wotsatira.
“Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: ‘Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.’”—Maliko 1:11
-
-
Mdyerekezi Anayesa YesuZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 75
Mdyerekezi Anayesa Yesu
Yesu atabatizidwa mzimu woyera unamutsogolera kupita kuchipululu. Sanadye chilichonse kwa masiku 40 choncho anali ndi njala kwambiri. Ndiyeno Mdyerekezi anabwera kudzamuyesa ndipo anamuuza kuti: ‘Ngati ndinudi Mwana wa Mulungu, uzani miyalayi kuti isanduke mitanda ya mkate.’ Koma Yesu anamuyankha potchula zimene Malemba amanena. Anati: ‘Malemba amanena kuti munthu safunika chakudya chokha kuti akhale ndi moyo. Amafunikanso kumvera mawu alionse ochokera m’kamwa mwa Yehova.’
Kenako Mdyerekezi anauza Yesu kuti: ‘Ngati ndinudi Mwana wa Mulungu, mudumphe kuchokera pamwamba pa kachisi. Pajatu Malemba amanena kuti Mulungu adzatumiza angelo ake kuti adzakunyamuleni kuti musavulale.’ Koma Yesu anayankhanso pogwiritsa ntchito Malemba. Iye anati: ‘Malemba amanena kuti usamuyese Yehova.’
Kenako Mdyerekezi anaonetsa Yesu maufumu onse a padziko lapansi ndi chuma chawo. Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Ndikupatsani maufumu onsewa ndi chuma chonsechi ngati mutagwada pansi kamodzi kokha n’kundilambira.’ Koma Yesu anayankha kuti: ‘Choka Satana! Malemba amati, uyenera kulambira Yehova yekha basi.’
Yesu atanena zimenezi, Mdyerekezi anamusiya ndipo angelo anabwera kudzamupatsa chakudya. Izi zitatha, Yesu anayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Imeneyi ndi ntchito imene Mulungu anamutuma kuti adzachite. Anthu ankakonda zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ankamutsatira kulikonse kumene wapita.
“[Mdyerekezi] akamanena bodza, amangosonyeza mmene alili, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yohane 8:44
-
-
Yesu Anayeretsa KachisiZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 76
Yesu Anayeretsa Kachisi
M’chaka cha 30 C.E., Yesu anapita ku Yerusalemu pa nthawi ya chikondwerero cha Pasika. Anthu enanso ambiri anapita ku Yerusalemuko kukachita chikondwererochi. Pa nthawiyi, anthu ankapereka nsembe za nyama pakachisi. Ena ankabweretsa nyamazi, koma ena ankagula ku Yerusalemu komweko.
Yesu atalowa m’kachisi anapeza kuti anthu akugulitsa nyama mmenemo. Tangoganiza! Ankachita malonda m’nyumba mwa Yehova mwenimwenimo! Ndiye kodi Yesu anatani? Nthawi yomweyo anatenga zingwe n’kupanga chokwapulira. Ndiyeno anayamba kuthamangitsa nkhosa ndi ng’ombe zimene zinali m’kachisimo. Anagubuduzanso matebulo a anthu amene ankachita malondawo komanso anakhuthulira pansi ndalama zawo. Iye anauza anthu amene ankagulitsa nkhunda kuti: ‘Chotsani izi muno! Nyumba ya Bambo anga musaisandutse malo ochitira bizinezi!’
Anthu anadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi. Ophunzira ake anakumbukira ulosi wonena za Mesiya wakuti: ‘Ndidzakhala wodzipereka kwambiri panyumba ya Yehova.’
M’chaka cha 33 C.E., Yesu anayeretsanso kachisi kachiwiri pothamangitsa anthu amene ankachita malonda panyumba ya Yehova. Iye sanalole kuti munthu aliyense azinyoza nyumba ya Yehova.
“Simungakhale akapolo a Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”—Luka 16:13
-
-
Yesu Anakumana ndi Mayi PachitsimeZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 77
Yesu Anakumana ndi Mayi Pachitsime
Pasika atatha, Yesu ndi ophunzira ake anayamba ulendo wobwerera ku Galileya ndipo anadutsa ku Samariya. Atafika mumzinda wa Sukari, Yesu anaima pachitsime cha Yakobo. Ophunzira ake anamusiya akupuma, n’kupita kukagula chakudya mumzindawo.
Ndiyeno panafika mayi wina kudzatunga madzi. Yesu anamuuza kuti: “Mundigawireko madzi akumwa mayi.” Mayiyo anati: ‘Bwanji mukupempha madzi kwa ine? Inetu ndine Msamariya. Paja Ayuda salankhula ndi Asamariya.’ Koma Yesu anamuuza kuti: ‘Mukanadziwa kuti ndine ndani, bwenzi mutandipempha kuti ndikupatseni madzi amoyo.’ Mayiyo anafunsa Yesu kuti: ‘Mukutanthauza chiyani? Inu mulibe chotungira ndiye madzi muwatenga kuti?’ Yesu anayankha kuti: ‘Aliyense wakumwa madzi amene ine ndingam’patse sadzamvanso ludzu ngakhale pang’ono.’ Ndiyeno mayiyo anati: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo.”
Kenako Yesu anauza mayiyo kuti: ‘Pitani mukaitane mwamuna wanu.’ Koma mayiyo anati: “Ndilibe Mwamuna.” Yesu anati: ‘Mwanena zoona. Chifukwa mwakwatiwapo ndi amuna 5, ndipo mwamuna amene mukukhala naye panopa si mwamuna wanu.’ Mayiyo atamva zimenezi anati: ‘Ndazindikira kuti ndinu mneneri. Ife timakhulupirira kuti tiyenera kulambira Mulungu m’phiri ili, pamene Ayudanu mumati tiyenera kulambira Mulungu ku Yerusalemu kokha. Koma ndikukhulupirira kuti Mesiya akadzabwera adzatiphunzitsa kuti tizilambira bwanji.’ Ndiyeno Yesu anamuuza zimene anali asanauzepo aliyense. Anati: ‘Ineyo ndine Mesiya.’
Mayiyo anathamanga n’kukauza Asamariya kuti: ‘Ndakumana ndi Mesiya. Akudziwa zonse zokhudza ineyo. Tiyeni mukamuone.’ Anthuwo anapita naye limodzi ndipo Yesu anawaphunzitsa zinthu zambiri.
Asamariyawo anapempha Yesu kuti akhalebe mumzinda wawo. Choncho anakhala nawo kwa masiku awiri n’kumawaphunzitsa ndipo ambiri anamukhulupirira. Iwo anauza mayi uja kuti: ‘Zimene tamva kwa munthuyo zatithandiza kudziwa kuti iyedi ndi mpulumutsi wa dziko.’
“‘Bwera!’ Komanso aliyense amene akumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi opatsa moyo kwaulere.”—Chivumbulutso 22:17
-
-
Yesu Ankalalikira Uthenga wa UfumuZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 78
Yesu Ankalalikira Uthenga wa Ufumu
Yesu atangobatizidwa, anayamba kulalikira kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ Iye ankalalikira mu Galileya ndi mu Yudeya monse ndipo ophunzira ake ankapita naye limodzi. Yesu atabwerera kwawo ku Nazareti, anapita kusunagoge n’kuyamba kuwerenga mokweza mpukutu wa Yesaya. Iye anati: ‘Yehova wandipatsa mzimu woyera kuti ndilalikire uthenga wabwino.’ Anthu a ku Nazareti ankafuna kuona Yesu akuchita zozizwitsa. Koma zimene anawerengazi zikusonyeza kuti, chifukwa chachikulu chimene Mulungu anam’patsira mzimu woyera, chinali choti azilalikira uthenga wabwino. Kenako Yesu anauza anthuwo kuti: ‘Lero ulosi uwu wakwaniritsidwa.’
Yesu atachoka kumeneku anapita kunyanja ya Galileya komwe anakapeza ophunzira ake 4 akuwedza nsomba. Iye anawauza kuti: ‘Nditsatireni, ndikusandutsani asodzi a anthu.’ Ophunzirawa anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Nthawi yomweyo iwo anasiya bizinezi yawo yopha nsomba n’kuyamba kumutsatira. Anayenda naye ku Galileya konse n’kumalalikira za Ufumu wa Mulungu. Ankalalikira m’masunagoge, m’misika komanso m’misewu. Kulikonse kumene ankapita anthu ambiri ankawatsatira. Nkhani yokhudza Yesu inali m’kamwam’kamwa moti mpaka inafika ku Siriya.
Yesu anapatsa otsatira ake ena mphamvu zochiritsa komanso kutulutsa ziwanda. Iye ankalalikira m’mizinda komanso m’midzi limodzi ndi ophunzira ake ena. Azimayi angapo okhulupirika ankathandiza Yesu ndi otsatira ake. Ena mwa azimayiwa anali Mariya Mmagadala, Jowana komanso Suzana.
Kenako Yesu anaphunzitsa otsatira akewa n’kuwatumiza kuti akalalikire. Iwo analalikira ku Galileya konse. Anthu ochuluka anakhala ophunzira a Yesu ndipo anabatizidwa. Ambiri ankafuna kuphunzira moti Yesu anawayerekezera ndi m’munda woti ukufunika kukolola. Anati: ‘Pemphani Yehova kuti atumize antchito okakolola.’ Kenako anasankha ophunzira 70 n’kuwatumiza awiriawiri kuti akalalikire ku Yudeya konse. Iwo ankaphunzitsa anthu onse za Ufumu. Ophunzirawa atabwerako, anafotokozera Yesu zinthu zosangalatsa zimene zinachitika. Mdyerekezi sanathe kulepheretsa ntchito yolalikirayi.
Yesu anathandiza ophunzira akewo kuti adzathe kupitiriza ntchito yofunikayi iye akadzapita kumwamba. Anawauzanso kuti: ‘Muzilalikira padziko lonse komanso muziphunzitsa anthu Mawu a Mulungu ndipo muziwabatiza.’
“Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.”—Luka 4:43
-
-
Yesu Anachita Zozizwitsa ZambiriZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 79
Yesu Anachita Zozizwitsa Zambiri
Yesu anabwera padzikoli kudzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yehova anamupatsa mzimu woyera kuti azitha kuchita zozizwitsa. Anachita zimenezi pofuna kusonyeza zimene Yesu adzachite akamadzalamulira dziko lapansili. Yesu ankatha kuchiritsa matenda alionse. Akapita kulikonse, anthu ankamupempha kuti awachiritse ndipo ankawachiritsadi. Ankachiritsa anthu amene ali ndi vuto losaona komanso losamva, ofa ziwalo ndiponso ankatulutsa ziwanda. Ngakhale kungogwira zovala zake, munthu ankatha kuchira. Kulikonse kumene Yesu wapita, anthu ankamutsatira. Ngakhale pa nthawi imene akufuna kukhala payekha, anthu akamutsatira sankawathamangitsa.
Tsiku lina anthu anabwera ndi munthu wofa ziwalo kunyumba imene Yesu anali. Koma sanathe kulowa chifukwa m’nyumbamo munali anthu ambiri. Choncho anthuwo anaboola padenga n’kutsitsira munthuyo m’kati. Yesu ataona munthuyo anamuuza kuti: ‘Imirira uziyenda.’ Munthuyo anayambadi kuyenda ndipo anthu anadabwa kwambiri.
Yesu akulowa m’mudzi wina anthu akhate 10 anaima chapatali n’kukuwa kuti: ‘Yesu tithandizeni!’ Pa nthawiyo munthu wodwala khate sankaloledwa kukhala pafupi ndi anthu ena. Yesu anauza akhatewo kuti apite kukachisi. Chilamulo cha Yehova chinkati munthu wakhate akachira, azipita kukachisi kukadzionetsa kwa ansembe. Ali m’njira, onse anazindikira kuti achira. Zitatero mmodzi anabwerera n’kupita kukathokoza Yesu ndipo ankatamanda Mulungu. Pa akhate 10 onsewo, ndi mmodzi yekhayu amene anapita kukathokoza.
Panalinso mayi wina amene anadwala kwa zaka 12 ndipo ankafunitsitsa atachira. Choncho ataona Yesu anayamba kumutsatira ndipo kenako anagwira m’mphepete mwa malaya ake akunja. Nthawi yomweyo anachira. Zimenezi zitachitika Yesu anafunsa kuti: “Ndi ndani wagwira malaya anga akunjawa?” Mayiyo anachita mantha, komabe anabwera pafupi n’kumuuza Yesu chilungamo. Yesu anamulimbikitsa pomuuza kuti: ‘Mwanawe, pita mu mtendere.’
Komanso mtsogoleri wina wa sunagoge dzina lake Yairo anapempha Yesu kuti: ‘Tiyeni tipite kunyumba kwanga kuti mukachiritse mwana wanga wamkazi yemwe akudwala kwambiri.’ Koma Yesu asanafike kunyumba kwa Yairo, mwanayo anamwalira. Yesu atafikako, anapeza anthu ambiri amene anabwera kudzakhala ndi banjalo pa nthawi yovutayi. Yesu anawauza kuti: ‘Musalire, mwanayu sanamwalire koma akugona.’ Kenako anagwira dzanja la mwanayo n’kunena kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!” Nthawi yomweyo anadzuka n’kukhala tsonga ndipo Yesu anauza makolo ake kuti amupatse chakudya. Ukuganiza kuti makolo akewo anamva bwanji ataona kuti mwana wawo ali moyo?
“Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera ndi mphamvu. Popeza Mulungu anali naye, anayenda mʼdziko lonse nʼkumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu onse amene Mdyerekezi ankawazunza.”—Machitidwe 10:38
-
-
Yesu Anasankha Atumwi 12Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 80
Yesu Anasankha Atumwi 12
Yesu atalalikira pafupifupi kwa chaka ndi hafu, ankafunika kusankha zinthu zina zofunika kwambiri. Anafunika kusankha anthu apadera oti azigwira nawo ntchito yolalikira. Anthuwa anafunikanso kuwaphunzitsa kuti adzathe kutsogolera mpingo wa Chikhristu iye akadzapita kumwamba. Yesu anaona kuti m’pofunika kuti Yehova amutsogolere posankha anthuwo. Choncho anapita kuphiri kwayekhayekha ndipo anapemphera usiku wonse. Kutacha, anaitana ophunzira ake ena ndipo anasankhapo anthu 12 oti akhale atumwi. Kodi ukukumbukira mayina awo? Anali Petulo, Andireya, Yakobo, Yohane, Filipo, Batolomeyo, Tomasi, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni ndi Yudasi Isikariyoti.
Andireya, Petulo, Filipo, Yakobo
Atumwi 12 amenewa ankayenda ndi Yesu. Kenako atawaphunzitsa, anayamba kumapita okha. Yehova anawapatsa mphamvu kuti azitha kutulutsa ziwanda komanso kuchiritsa odwala.
Yohane, Mateyu, Batolomeyo, Tomasi
Yesu ankaona kuti atumwi 12 amenewa ndi anzake ndipo ankawakhulupirira. Koma Afarisi ankaganiza kuti atumwiwo anali osaphunzira komanso anthu wamba. Komatu Yesu anawaphunzitsa kuti azigwira bwino ntchito yawo. Atumwiwo anakhalabe ndi Yesu pa nthawi yofunika kwambiri pa moyo wake. Mwachitsanzo, analipo Yesu atatsala pang’ono kuphedwa komanso ataukitsidwa. Mofanana ndi Yesu ambiri mwa atumwiwa anali ochokera ku Galileya. Ndipo ena anali okwatira.
Yakobo mwana wa Alifeyo, Yudasi Isikariyoti, Tadeyo, Simoni
Koma atumwiwa sanali angwiro ngati ife tomwe ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Pena ankalankhula asanaganize ndiponso ankasankha molakwika. Nthawi zinanso sankaleza mtima komanso ankakangana kuti wamkulu ndi ndani. Komabe atumwiwa anali anthu abwino ndipo ankakonda Yehova. Iwo ndi amene anali anthu oyamba kukhala mumpingo wa Chikhristu Yesu atapita kumwamba.
“Ndakutchulani kuti anzanga, chifukwa ndakudziwitsani zinthu zonse zimene ndamva kwa Atate wanga.”—Yohane 15:15
-
-
Ulaliki wa PaphiriZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 81
Ulaliki wa Paphiri
Yesu atasankha atumwi ake 12, anatsika m’phiri n’kupita pamalo amene panasonkhana anthu ambiri. Anthuwo anali ochokera ku Galileya, Yudeya, Turo, Sidoni, Siriya komanso kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano. Anamubweretsera anthu odwala matenda osiyanasiyana komanso amene ankavutitsidwa ndi ziwanda. Yesu anawachiritsa onsewo. Kenako anakhala pansi n’kuyamba kuwaphunzitsa. Anafotokoza zimene munthu angachite ngati akufuna kuti Mulungu akhale mnzake. Yesu anatinso tiyenera kuzindikira kuti timafunika kutsogoleredwa ndi Yehova ndipo tiyenera kuphunzira za iye kuti tizimukonda. Koma ananena kuti sitingakonde Mulungu ngati sitikonda anzathu. Komanso tiyenera kuchitira zabwino aliyense, ngakhale adani athu.
Yesu anati: ‘Kungokonda anzanu si kokwanira. Muyenera kukondanso adani anu komanso muzikhululuka kuchokera pansi pa mtima. Ngati wina wakulakwirani, muzipita kukakambirana naye n’kupepesana. Muzichitira anthu zimene mungafune kuti iwonso akuchitireni.’
Yesu anaperekanso malangizo abwino okhudza chuma. Iye anati: ‘Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi ndalama zambiri. Munthu angathe kukuberani ndalama koma sangakubereni ubwenzi wanu ndi Yehova. Siyani kudandaula kuti: “Mawa tidzadya chiyani, tidzamwa chiyani nanga tidzavala chiyani?” Ganizirani za mbalame. Mulungu amaonetsetsa kuti nthawi zonse zili ndi chakudya chokwanira. Kudandaula sikungapangitse kuti mukhale ndi moyo wautali. Musaiwale kuti Yehova amadziwa zimene mukufunikira.’
Anthuwo anali asanamvepo munthu akulankhula ngati mmene Yesu ankalankhulira. Atsogoleri a chipembedzo anali asanawaphunzitsepo zimenezi. N’chifukwa chiyani Yesu ankatha kuphunzitsa bwino chonchi? Chifukwa choti zonse zimene ankaphunzitsa zinkachokera kwa Yehova.
“Senzani goli langa ndipo lolani kuti ndikuphunzitseni, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa ndipo mudzatsitsimulidwa.”—Mateyu 11:29
-
-
Yesu Anaphunzitsa Otsatira Ake KupempheraZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 82
Yesu Anaphunzitsa Otsatira Ake Kupemphera
Afarisi ankakonda kuchita zinthu n’cholinga chongofuna kugometsa anthu. Akachitira munthu zabwino, ankafuna kuti aliyense adziwe. Ankakonda kupemphera pamene pamadutsa anthu ambiri kuti anthuwo aziwaona. Komanso iwo ankaloweza mapemphero n’kumawanena m’masunagoge kapena pamphambano n’cholinga choti anthu azimva. Choncho anthu anadabwa pamene Yesu anawauza kuti: ‘Musamapemphere ngati Afarisi. Iwo ankaganiza kuti Mulungu angachite chidwi ndi mapemphero awo aatali. Pemphero ndi nkhani ya pakati pa Yehova ndi munthu amene akupempherayo. Ndiponso musamabwereze zomwezomwezo popemphera. Yehova amafuna kuti muzimuuza zimene zili mumtima mwanu, osati zongoloweza.’
Yesu ananenanso kuti: ‘Popemphera muzinena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Zofuna zanu zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.”’ Anawauzanso kuti angathe kupempha chakudya cha tsikulo. Komanso angapemphe kuti Mulungu awakhululukire machimo awo ndiponso kuti awathandize pa zinthu zina zokhudza iwowo.
Yesu anati: ‘Musasiye kupemphera. Pitirizani kupempha Atate wanu Yehova kuti akupatseni zinthu zabwino. Makolo amafunitsitsa kupatsa ana awo zinthu zabwino. Mwana wanu atakupemphani chakudya kodi mungamupatse mwala? Komanso ngati atakupemphani nsomba mungamupatse njoka?’
Kenako anati: ‘Ngati inu mumapatsa ana anu zinthu zabwino, ndiye kuli bwanji Atate wanu Yehova? Iye adzakupatsani mzimu woyera. Chofunika ndi kumupempha basi.’ Kodi iweyo umatsatira malangizo a Yesuwa? Kodi ukamapemphera umatchula zinthu ziti?
“Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.”—Mateyu 7:7
-
-
Yesu anadyetsa anthu ambiriZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 83
Yesu Anadyetsa Anthu Ambiri
Tsiku lina atumwi anabwera kuchokera kumene ankalalikira. Apa n’kuti Pasika wa mu 32 C.E. atangotsala pang’ono kufika. Atumwiwo anali atatopa kwambiri ndipo Yesu ananyamuka nawo pa boti kupita ku Betsaida kuti akapume. Koma atayandikira kumtunda anaona kuti anthu ambirimbiri afika kale ndipo akuwadikira. Ngakhale kuti inali nthawi yoti apume ndi ophunzira ake, Yesu anawalandira bwino. Anachiritsa odwala onse ndipo kenako anayamba kuwaphunzitsa. Yesu anawaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu tsiku lonse. Ndiyeno madzulo, atumwi anamuuza kuti: ‘Anthuwatu ali ndi njala. Auzeni azipita kuti akapeze chakudya.’
Yesu anayankha kuti: ‘Asapite. Inuyo muwapatse chakudya.’ Atumwiwo anafunsa kuti: ‘Mukutanthauza kuti tipite kukawagulira chakudya?’ Ndiyeno mtumwi wina dzina lake Filipo anati: ‘Ngakhale tikanakhala ndi ndalama zambiri sitingakwanitse kugula chakudya cha anthu onsewa.’
Yesu anawafunsa kuti: ‘Chakudya chomwe tili nacho n’chochuluka bwanji?’ Andireya anati: ‘N’chochepa kwambiri. Tili ndi mikate 5 ndi nsomba ziwiri basi.’ Kenako Yesu anati: ‘Bweretsani.’ Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pa udzu m’magulu a anthu 50 komanso 100. Yesu anatenga mikate ndi nsombazo n’kuyang’ana kumwamba ndipo anapemphera. Kenako anapereka chakudyacho kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo ankapereka kwa anthu. Panali amuna 5,000 ndiponso akazi ndi ana koma onse anadya n’kukhuta. Atumwiwo anatolera zotsalira n’cholinga choti pasatayidwe kalikonse. Zotsalazo zinadzadza mabasiketi 12. Izitu zinali zodabwitsa kwambiri.
Anthu ataona zimenezi anadabwa kwambiri moti ankafuna kuti Yesu akhale mfumu yawo. Koma Yesu anadziwa kuti imeneyo sinali nthawi imene Yehova ankafuna kuti iye akhale mfumu. Kenako anauza anthu onse kuti azipita ndipo iye ndi atumwi ake anapita tsidya lina la nyanja ya Galileya. Atumwiwo anakwera boti koma Yesu anapita yekha kuphiri kuti akapemphere kwa Atate ake. Yesu ankayesetsa kupeza mpata wopemphera ngakhale kuti ankatanganidwa kwambiri.
“Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chimabweretsa moyo wosatha. Mwana wa munthu adzakupatsani chakudya chimenechi.”—Yohane 6:27
-
-
Yesu Anayenda PanyanjaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 84
Yesu Anayenda Panyanja
Kuwonjezera pa kuchiritsa odwala ndi kuukitsa akufa, Yesu ankathanso kulamulira mphepo komanso mvula. Tsiku lina, Yesu anapita kuphiri kukapemphera, ndiye atamaliza anaona kuti panyanja ya Galileya panali chimphepo ndi mafunde. Atumwi ake anali m’boti ndipo ankalimbana ndi mphepo panyanjapo. Ndiyeno iye anatsika m’phirimo n’kuyamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali boti la atumwi akewo. Atumwiwo ataona munthu akuyenda pamadzi, anachita mantha. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Musachite mantha, ndine.’
Petulo anati: ‘Ambuye ngati ndinuyo, ndiuzeni ndibwere kumene muliko.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Bwera.’ Choncho Petulo anatuluka m’boti muja n’kuyamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. Koma atayandikira, anayang’ana chimphepo chija. Atatero anachita mantha ndipo anayamba kumira. Iye anafuula kuti: ‘Ambuye, ndithandizeni!’ Yesu anamugwira dzanja n’kumufunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani unayamba kukayikira? Chikhulupiriro chako chili kuti?’
Yesu ndi Petulo anakwera m’boti muja ndipo nthawi yomweyo mphepo ija inasiya. Kodi ukuganiza kuti atumwiwo anamva bwanji? Iwo anati: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”
Si nthawi yokhayi pamene Yesu anachita zodabwitsa ngati zimenezi. Pa nthawi ina ali ndi atumwi ake muboti, Yesu anapita chakumbuyo kwa botilo n’kugona. Iye ali m’tulo, panyanjapo panayambika chimphepo. Mafunde ankamenya botilo ndipo mubotimo munalowa madzi. Atumwi anamudzutsa n’kumuuza kuti: ‘Mphunzitsi tifatu, chonde tithandizeni.’ Yesu anadzuka n’kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” Nthawi yomweyo chimphepo chija chinatha ndipo panyanjapo panali bata. Ndiyeno Yesu anafunsa atumwiwo kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Atumwiwo anayamba kuuzana kuti: “Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.” Iwo anaphunzirapo kuti ngati amakhulupirira kwambiri Yesu, sayenera kuopa chilichonse.
“Kodi ndikanakhala ndili kuti ndikanapanda kukhala ndi chikhulupiriro choti ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo?”—Salimo 27:13
-
-
Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la SabataZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 85
Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata
Afarisi ankadana ndi Yesu ndipo ankafuna kuti am’pezere chifukwa kuti amumange. Iwo ankanena kuti Yesu sakuyenera kumachiritsa anthu pa Sabata. Pa tsiku lina la Sabata, Yesu anakumana ndi munthu amene anali ndi vuto losaona amene ankapemphapempha mumsewu. Iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Dikirani muone mmene mphamvu za Mulungu zingamuthandizire munthuyu.’ Kenako Yesu analavulira pansi n’kukanda thope ndi malovuwo. Ndiyeno anapaka thopelo m’maso mwa munthuyo n’kumuuza kuti: “Pita ukasambe m’dziwe la Siloamu.” Munthuyo anapitadi ndipo anayamba kuona.
Anthu anadabwa kwambiri ndi zimenezi moti anati: ‘Kodi munthuyu ndi amene amapemphapempha uja, kapena ndi wina angofanana?’ Munthuyo anati: ‘Ndine ndemwe ndithu ndipo ndinabadwa wosaona.’ Anthuwo anamufunsa kuti: ‘Ndiye chachitika n’chiyani kuti uyambe kuona?’ Atawafotokozera zomwe zachitika, anamutenga n’kupita naye kwa Afarisi.
Munthuyo anauza Afarisiwo kuti: ‘Yesu anakanda thope n’kundipaka m’maso ndipo kenako anandiuza kuti ndikasambe. Ndinapitadi ndipo nditasamba ndinayamba kuona.’ Koma Afarisiwo anati: ‘Ngati Yesu akumachiritsa anthu pa Sabata ndiye kuti mphamvu zake sizingakhale zochokera kwa Mulungu.’ Koma ena anati: ‘Zikanakhala kuti mphamvu zake si zochokera kwa Mulungu, si bwenzi akuchiritsa anthu.’
Afarisi anaitana makolo ake a munthuyo n’kuwafunsa kuti: ‘Zatheka bwanji kuti mwana wanu ayambe kuona?’ Koma makolowo ankaopa chifukwa Afarisi ankachotsa musunagoge munthu aliyense wokhulupirira Yesu. Choncho anangoyankha kuti: ‘Sitikudziwa. Mufunseni mwiniwakeyo.’ Afarisiwo anafunsa munthuyo mafunso ambirimbiri mpaka iye anawayankha kuti: ‘Ndakuuzani kale zonse. N’chifukwa chiyani mukungondifunsabe?’ Afarisiwo anakwiya ndi zimenezi ndipo anamuponyera kunja.
Yesu anapita kumene kunali munthuyo ndipo anamufunsa kuti: ‘Kodi umakhulupirira Mesiya?’ Munthuyo anayankha kuti: ‘Eya ndingamukhulupirire nditakhala kuti ndikumudziwa.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Ineyo ndine Mesiya.’ Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti anali wokoma mtima. Tikutero chifukwa anachiritsa munthuyo komanso anamuthandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro.
“Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.”—Mateyu 22:29
-
-
Yesu Anaukitsa LazaroZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 86
Yesu Anaukitsa Lazaro
Yesu anali ndi anzake atatu apamtima amene ankakhala ku Betaniya. Anzakewo anali Lazaro ndi azichemwali ake awiri, Mariya ndi Marita. Tsiku lina, Yesu ali kutsidya lina la Yorodano, Mariya ndi Marita anamutumizira uthenga wakuti: ‘Lazaro akudwala mwakayakaya. Chonde mubwere mwamsanga.’ Koma Yesu sanapite nthawi yomweyo. Anakhalabe masiku awiri kenako anauza ophunzira ake kuti: ‘Tiyeni ku Betaniya. Lazaro akugona ndiye ndikufuna ndikamudzutse.’ Atumwiwo ananena kuti: ‘Ngati Lazaroyo akugona zimuthandiza kuti apeze bwino mwamsanga.’ Apa tsopano Yesu anawauza kuti: ‘Lazaro wamwalira.’
Pamene Yesu ankafika ku Betaniya n’kuti Lazaro atakhala m’manda masiku 4. Kunali anthu ambiri amene anabwera kudzatonthoza Marita ndi Mariya. Marita atamva kuti Yesu akubwera, anapita kukamuchingamira ndipo atakumana naye anati: ‘Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira.’ Yesu anamuyankha kuti: ‘Mchimwene wako auka. Ukukhulupirira zimenezi Marita?’ Iye ananena kuti: ‘Eya, ndikukhulupirira kuti adzauka pa tsiku lomaliza.’ Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: ‘Ine ndine kuuka ndi moyo.’
Kenako Marita anapita kukauza Mariya kuti: ‘Yesu wabwera.’ Mariya anathamangira kwa Yesu ndipo gulu la anthu linamutsatira. Mariya anagwada pafupi ndi Yesu ndipo ankangolira. Kenako anati: ‘Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wathu sakanamwalira.’ Yesu ataona kuti Mariya ali ndi chisoni kwambiri, nayenso anayamba kulira. Anthu ataona kuti Yesu akugwetsa misozi anati: ‘Taonani, koma ndiyetu Yesu ankamukonda kwambiri Lazaro.’ Koma ena anayamba kufunsa kuti: ‘Ndiye n’chifukwa chiyani sanamuthandize kuti asafe?’ Kodi Yesu anatani?
Yesu ndi anthuwo anapita kumanda ndipo anapeza kuti pamandapo atsekapo ndi chimwala. Iye anauza anthu kuti: ‘Chotsani chimwalachi.’ Koma Marita anati: ‘Wakhalatu m’manda kwa masiku 4. Ayenera kuti wayamba kununkha.’ Koma anthu anachotsabe mwalawo ndipo Yesu anapemphera kuti: ‘Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikupemphera mokweza chonchi kuti anthuwa adziwe zoti inuyo munanditumiza.’ Kenako anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Atatero panachitika zodabwitsa. Lazaro uja anatuluka ali wokulungidwa ndi nsalu zamaliro. Yesu anati: “Mʼmasuleni kuti athe kuyenda.”
Anthu ambiri amene anaona zimenezi anakhulupirira Yesu. Koma ena anapita kukauza Afarisi ndipo Afarisiwo anayamba kufuna kupha Lazaro ndi Yesu. Mmodzi mwa atumwi 12 aja dzina lake Yudasi, anazemba n’kupita kwa Afarisi kukawauza kuti: ‘Mundipatsa ndalama zingati ndikakuthandizani kupeza Yesu?’ Anagwirizana naye kuti amupatsa ndalama 30 zasiliva. Choncho Yudasi anayamba kufufuza mpata woti apereke Yesu.
“Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa. Ndipo Yehova Ambuye Wamkulu Koposa amatipulumutsa ku imfa.”—Salimo 68:20
-
-
Chakudya Chamadzulo ChomalizaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 87
Chakudya Chamadzulo Chomaliza
Ayuda ankachita chikondwerero cha Pasika pa tsiku la 14 la mwezi wa Nisani. Ankachita zimenezi pokumbukira zimene Mulungu anachita powapulumutsa ku Iguputo kuti akakhale m’Dziko Lolonjezedwa. Mu 33 C.E., Yesu ndi atumwi ake anachita mwambowu ku Yerusalemu m’chipinda cham’mwamba. Pomaliza, Yesu ananena kuti: ‘Mmodzi wa inu adzandipereka.’ Atumwiwo anadabwa kwambiri ndipo anafunsa Yesu kuti: ‘Mukunena ndani?’ Yesu anayankha kuti: ‘Amene ndimupatse mkatewu.’ Kenako anapereka mkate kwa Yudasi Isikariyoti. Nthawi yomweyo Yudasi anatuluka.
Yesu anapemphera ndipo kenako ananyemanyema mkate n’kupereka kwa atumwiwo. Ndipo anati: ‘Idyani mkatewu. Ukuimira thupi langa limene ndidzapereke chifukwa cha inu.’ Kenako anapempheranso n’kupereka vinyo kwa atumwiwo. Ananena kuti: ‘Imwani vinyoyu. Akuimira magazi anga amene ndidzapereke n’cholinga choti machimo a anthu akhululukidwe. Muzichita zimenezi chaka chilichonse pondikumbukira. Ndikukulonjezani kuti tidzakalamulira limodzi kumwamba.’ Kuyambira nthawi imeneyo, otsatira a Khristu amachita mwambo wokumbukira imfa yake chaka chilichonse. Mwambo umenewu umatchedwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.
Atangomaliza mwambowu, atumwiwo anayamba kukangana. Nkhani yake inali yoti wamkulu ndi ndani. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Wamkulu kwambiri pa nonsenu, ndi amene amadziona kuti ndi wamng’ono kwambiri.
‘Inutu ndinu anzanga. Ndimakuuzani chilichonse chimene Atate wanga wafuna kuti ndikuuzeni. Posachedwapa ndipita kumwamba kwa Atate anga. Anthu adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mumakondana. Choncho muzikondana ngati mmene ine ndimakukonderani.’
Pomaliza, Yesu anapempha Yehova kuti ateteze ophunzira ake onse. Anapemphanso kuti awathandize kuti azichita zinthu mogwirizana komanso mwamtendere. Kenako anapempha kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. Ndiyeno Yesu ndi atumwiwo anaimba nyimbo zotamanda Yehova kenako anatuluka m’chipindamo. Apa tsopano nthawi yoti Yesu amangidwe inali itayandikira.
“Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani Ufumu.”—Luka 12:32
-
-
Yesu AnamangidwaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 88
Yesu Anamangidwa
Yesu ndi atumwi ake anadutsa m’chigwa cha Kidironi n’kupita kuphiri la Maolivi. Apa n’kuti nthawi itapitirira 12 koloko ya usiku ndipo mwezi unali wathunthu. Atafika m’munda wa Getsemane Yesu anauza atumwiwo kuti: “Khalani pansi panopa, ine ndikupita uko kukapemphera.” Kenako anapita chapatali ndipo anagwada n’kuyamba kupemphera. Iye anali ndi nkhawa kwambiri ndipo anapemphera kwa Yehova kuti: “Zimene inu mukufuna zichitike.” Yehova anatumiza mngelo kuti adzalimbikitse Yesu. Atapita pamene panali atumwi paja, anapeza atumwiwo akugona. Iye anawauza kuti: ‘Dzukani! Ino si nthawi yogona. Nthawi yoti ndiperekedwe kwa adani yayandikira.’
Pasanapite nthawi Yudasi anatulukira ali ndi gulu la anthu amene ananyamula malupanga ndi zibonga. Yesu ndi atumwi ake ankakonda kupita kumunda wa Getsemani. Choncho Yudasi ankadziwa kuti Yesu angapezeke kumeneku. Iye anali atauza anthuwo kuti akachita zinazake kuti iwo athe kuzindikira Yesu. Choncho anangofikira pamene panali Yesu n’kunena kuti: ‘Muli bwanji Mphunzitsi?’ Kenako anamukisa. Koma Yesu anati: ‘Yudasi, kodi ukundipereka pondikisa?’
Yesu anayandikira gululo n’kulifunsa kuti: “Mukufuna ndani?” Anthuwo anayankha kuti: “Yesu Mnazareti.” Ndiyeno iye anayankha kuti: “Ndi ineyo.” Koma anthuwo anabwerera m’mbuyo n’kugwa pansi. Yesu anawafunsanso kuti: ‘Ndati mukufuna ndani?’ Iwo anayankhanso kuti: “Yesu Mnazareti.” Yesu anawauza kuti: ‘Ndakuuzani kuti, ndi ineyo. Asiyeni awa azipita.’
Nthawi yomweyo Petulo anasolola lupanga lake n’kudula khutu la Makasi, yemwe anali wantchito wa mkulu wa ansembe. Koma Yesu anatenga khutulo n’kuliika pamalo ake ndipo anamuchiritsa. Kenako anauza Petulo kuti: ‘Bwezera lupangalo pamalo ake. Ukamapha anthu ndi lupanga, nawenso udzaphedwa ndi lupanga.’ Asilikaliwo anagwira Yesu n’kumumanga ndipo atumwi aja anathawa. Kenako asilikaliwo anatenga Yesu n’kupita naye kwa wansembe wamkulu, dzina lake Anasi. Atamufunsa mafunso anamutumiza kwa mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa. Koma kodi atumwi aja zinawathera bwanji?
“Mʼdzikomu mukumana ndi mavuto aakulu, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”—Yohane 16:33
-
-
Petulo Anakana YesuZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 89
Petulo Anakana Yesu
Yesu ali m’chipinda chapamwamba, anauza atumwi ake kuti ‘Usiku uno, nonse mundithawa n’kundisiya ndekha.’ Koma Petulo anati: ‘Koma ine ayi. Ngakhale ena onsewa atathawa, ine ndekha sindingakusiyeni.’ Koma Yesu anamuuza kuti: ‘Tambala asanalire, iweyo udzanena katatu kuti sukundidziwa.’
Pa nthawi imene anthu anagwira Yesu kupita naye kwa Kayafa, atumwi onse anathawa komabe awiri ankatsatira gululo. Mmodzi wa amene ankatsatirawo anali Petulo. Iye analowa nawo m’nyumba ya Kayafayo n’kumawotha moto ndi anthu ena. Ndiyeno mtsikana wina wantchito anazindikira Petulo n’kunena kuti: ‘Bambo inu ndakudziwani. Munali ndi Yesu.’
Petulo anayankha kuti: ‘Ayi, ine sindinali ndi ameneyo. Komanso zimene ukunenazo sindikuzidziwa.’ Zitatero ananyamuka n’kumapita cha kugeti. Koma mtsikana winanso wantchito atamuona anauza anthu kuti: ‘Bambo awa analinso ndi Yesu.’ Koma Petulo anati: ‘Inetu Yesuyo sindikumudziwa ngakhale pang’ono.’ Kenako bambo wina anati: ‘Ndiwe wophunzira wa Yesu. Kalankhulidwe kako kakugwiritsa kuti ndiwe wa ku Galileya.’ Koma Petulo analumbira kuti: ‘Ndithu ine sindikumudziwa ameneyo.’
Nthawi yomweyo tambala analira. Kenako Yesu anatembenuka n’kuyang’ana Petulo. Zitatero, Petulo anakumbukira zimene Yesu ananena zija ndipo anapita kunja n’kukayamba kulira kwambiri.
Oweruza mu Khoti Lalikulu la Ayuda anasonkhana m’nyumba ya Kayafa kuti ayambe kuzenga mlandu wa Yesu. Anali atagwirizana kale zoti aphe Yesu moti apa ankangofuna kupeza chifukwa. Koma sanachipeze. Kenako Kayafa anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?’ Yesu anayankha kuti: ‘Inde.’ Zitatero, Kayafa anati: ‘Sipakufunikanso umboni wina. Ameneyu akunyoza Mulungu.’ Oweruza onse anavomereza ndipo anati: ‘Aphedwe basi.’ Kenako ena anaomba Yesu mbama komanso kumulavulira. Ankamuphimba nkhope n’kumumenya, kenako n’kumanena kuti: ‘Ngati ndiwe mneneri tiuze amene wakumenya.’
Kutacha, anapita naye kubwalo loweruzira milandu ndipo anamufunsanso kuti: ‘Kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?’ Yesu anayankha kuti: ‘Mukunena nokha kuti ndine Mwana wa Mulungu.’ Apa anamupeza ndi mlandu wonyoza Mulungu ndipo anapita naye kwa bwanamkubwa wa Chiroma dzina lake Pontiyo Pilato. Kodi kumeneko zinatha bwanji? Tiona m’mutu wotsatira.
“Nthawi . . . yafika kale, pamene nonse mubalalika, aliyense kupita kunyumba kwake ndipo mundisiya ndekha. Koma sindikhala ndekha, chifukwa Atate ali ndi ine.”—Yohane 16:32
-
-
Yesu Anaphedwa ku GologotaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 90
Yesu Anaphedwa ku Gologota
Ansembe aakulu anatenga Yesu n’kupita naye kwa bwanamkubwa wina dzina lake Pilato. Pilatoyo anafunsa anthuwo kuti: ‘Kodi munthuyu walakwa chiyani?’ Iwo anayankha kuti: ‘Akunena kuti ndi mfumu yathu.’ Ndiyeno Pilato anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?’ Yesu anayankha kuti: ‘Ufumu wanga si wapadzikoli.’
Zitatero, Pilato anatumiza Yesu kwa Herode, amene anali wolamulira chigawo cha Galileya, kuti akaone ngati Yesuyo alidi ndi mlandu. Koma Herode anapeza kuti Yesu sanalakwe chilichonse. Choncho anamutumizanso kwa Pilato. Ndiyeno Pilato anauza anthuwo kuti: ‘Ine ndi Herode taona kuti munthuyu ndi wosalakwa. Choncho ndimumasula.’ Koma anthuwo anakuwa kuti: ‘Mupheni! Mupheni!’ Asilikali anayamba kukwapula Yesu, kumulavulira komanso kumumenya. Anamuvekanso chipewa chaminga n’kumamunyoza kuti: ‘Muli bwanji Mfumu ya Ayuda?’ Pilato anauzanso anthuwo kuti: ‘Ine sindinam’peze ndi mlandu uliwonse munthuyu.’ Koma anthuwo anakuwanso kuti: “Apachikidwe ameneyo!” Choncho Pilato anawapatsa Yesu kuti akamupachike.
Ndiyeno anapita naye kumalo otchedwa Gologota ndipo anakamukhomerera pamtengo n’kuimika mtengowo. Koma Yesu anapemphera kuti: ‘Atate, muwakhululukire chifukwa sakudziwa zimene akuchita.’ Anthu anayamba kunyoza Yesu n’kumanena kuti: ‘Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, tsika pamtengopo. Dzipulumutse wekha.’
Wachifwamba wina amene anapachikidwa pafupi ndi Yesu anamuuza kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.” Atatero, Yesu anamulonjeza kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Masana kunagwa mdima m’dziko lonselo kwa maola atatu. Mayi ake komanso ophunzira ake ena anali chapafupi. Yesu anauza Yohane kuti azisamalira Mariya ngati mayi ake enieni.
Kenako Yesu anauza Mulungu kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” Ndiyeno anaweramira pansi n’kumwalira. Pa nthawi imeneyo panachitika chivomerezi champhamvu. Komanso chinsalu cha m’kachisi chomwe chinkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa chinang’ambika pakati. Mkulu wa asilikali ataona zimenezi anati: ‘Uyu analidi Mwana wa Mulungu.’
“Malonjezo a Mulungu, kaya akhale ambiri bwanji, akhala “inde” kudzera mwa iye.”—2 Akorinto 1:20
-
-
Yesu AnaukitsidwaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 91
Yesu Anaukitsidwa
Yesu atafa, munthu wina wachuma dzina lake Yosefe anapita kwa Pilato kukapempha kuti atenge thupi la Yesu n’kukaliika m’manda. Yosefe anapaka thupilo mafuta onunkhira n’kulikulunga munsalu yabwino kwambiri kenako n’kukaliika m’manda ochita kusema. Anagubuduza chimwala ndipo anatseka pakhomo la mandawo. Kenako ansembe aakulu anauza Pilato kuti: ‘Tikuganiza kuti ophunzira a Yesu akhoza kukaba thupi lake n’kumanama kuti wauka.’ Pilato anawauza kuti: ‘Pitani mukatseke kwambiri mandawo ndipo muikepo alonda.’
Patapita masiku atatu, azimayi ena analawirira kumandako ndipo anapeza kuti chimwala chija chachotsedwapo. M’mandamo munali mngelo ndipo anawauza kuti: ‘Musachite mantha. Yesu waukitsidwa. Pitani mukauze ophunzira ake kuti akakumane naye ku Galileya.’
Mariya Mmagadala anathamanga kukauza Petulo ndi Yohane kuti: ‘Thupi la Yesu labedwatu!’ Iwo anapita kumandako n’kukapezadi m’mandamo mulibe thupi la Yesu ndipo anabwerera kwawo.
Mariya atabwerera kumanda kuja anaona angelo awiri ali m’manda ndipo anawafunsa kuti: ‘Kodi Ambuye aja apita nawo kuti?’ Kenako anaona munthu wina ndipo ankaganiza kuti ndi wosamalira munda. Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Bambo, ngati ndinu mwawachotsa Ambuye ndiuzeni kumene mwawaika.’ Munthuyo atamuitana kuti: “Mariya!” anazindikira kuti anali Yesu. Choncho anafuula kuti: “Mphunzitsi!” ndipo anamugwira. Yesu anamuuza kuti: ‘Pita ukauze abale anga kuti wandiona.’ Nthawi yomweyo Mariya anapita kukauza ophunzira kuti waona Yesu.
Madzulo a tsiku lomwelo, ophunzira awiri ankayenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Emau. Ndiyeno munthu wina anayamba kuyenda nawo ndipo anawafunsa zimene ankakambirana. Iwo anati: ‘Kodi iwe sunamve? Masiku atatu apitawo ansembe aakulu anapha Yesu. Ndiye panopa azimayi ena akunena kuti ali moyo.’ Munthuyo anawafunsa kuti: ‘Kodi inu simukhulupirira zimene aneneri ananena? Pajatu anati Khristu adzafa kenako adzaukitsidwa.’ Munthuyo anawafotokozera Malemba osiyanasiyana. Atafika ku Emau, ophunzirawo anamupempha kuti apite nawo kwawo. Pa nthawi ya chakudya chamadzulo, munthuyo anapemphera ndipo anamuzindikira kuti anali Yesu. Kenako anasowa.
Nthawi yomweyo ophunzirawo anapita ku Yerusalemu ndipo anakalowa m’nyumba yomwe munali atumwi. Kumeneko anawafotokozera zimene zinachitika. Ali m’nyumbamo, Yesu anatulukira. Poyamba, atumwiwo sanakhulupirire kuti ndi Yesu. Koma iye anawauza kuti: ‘Onani manja angawa, ndigwireni kuti mutsimikize. Paja Malemba ananeneratu kuti Khristu adzaukitsidwa.’
“Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6
-
-
Yesu Anakumana ndi asodziZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 92
Yesu Anakumana ndi Asodzi
Patapita nthawi kuchokera pamene Yesu anakumana ndi atumwi, Petulo anaganiza zokapha nsomba kunyanja ya Galileya. Tomasi, Yakobo ndi Yohane nawonso anapita naye. Iwo anagwira ntchito yosodza usiku wonse koma sanaphe kalikonse.
Kutacha, anaona munthu wina ataima m’mbali mwa nyanja. Munthuyo anawafunsa kuti: ‘Koma mwapha nsomba inu?’ Iwo anayankha kuti: ‘Ayi ndithu.’ Ndiyeno anawauza kuti: ‘Ponyani ukonde wanuwo mbali yakumanja.’ Atatero mu ukondemo munadzadza nsomba zambiri moti analephera kuzikokera kumtunda. Nthawi yomweyo, Yohane anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu ndipo anati: ‘Aa eti ndi Ambuye!’ Petulo atangomva zimenezi analumphira m’madzi n’kuyamba kusambira kupita kumtunda. Ophunzira enawo anamutsatira pa ngalawa.
Atafika kumtunda, anapeza nsomba ndi mkate zili pamoto. Yesu anawauza kuti amupatseko nsomba zina kuti awonjezere chakudyacho. Kenako anawauza kuti: ‘Bwerani tidye chakudya cham’mawa.’
Atatha kudya, Yesu anafunsa Petulo kuti: ‘Kodi umandikonda kuposa ntchito yausodzi?’ Petulo anayankha kuti: ‘Inde Ambuye. Inunso mukudziwa zimenezo.’ Yesu anati: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga.’ Kenako Yesu anafunsanso kuti: ‘Petulo, kodi umandikonda?’ Iye anayankha kuti: ‘Ambuye, inu mukudziwa kuti ndimakukondani.’ Yesu anati: “Weta ana a nkhosa anga.” Ndiyeno anamufunsanso kachitatu ndipo Petulo anamva chisoni n’kuyankha kuti: ‘Ambuye, inu mumadziwa zonse. Mukudziwa kuti ndimakukondani.’ Yesu ananenanso kuti: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga.’ Kenako anamuuzanso kuti: “Pitiriza kunditsatira.”
“[Yesu] anawauza kuti: ‘Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.’ Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.”—Mateyu 4:19, 20
-
-
Yesu Anabwerera KumwambaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 93
Yesu Anabwerera Kumwamba
Yesu ndi ophunzira ake anakumana ku Galileya. Kumeneko anawapatsa lamulo lofunika kwambiri lakuti: ‘Pitani mukaphunzitse anthu a m’mayiko onse kuti akhale ophunzira anga. Mukawaphunzitse zimene ndinakuphunzitsani ndipo mukawabatize.’ Kenako anawalonjeza kuti: ‘Ndikhala nanu limodzi.’
Yesu ataukitsidwa anakhala padzikoli masiku 40 ndipo anaonana ndi ophunzira ake ambiri ku Galileya ndi ku Yerusalemu. Anawaphunzitsa zinthu zambiri komanso anachita zodabwitsa. Kenako anakumana ndi atumwi ake komaliza paphiri la Maolivi. Anawauza kuti: ‘Musachoke ku Yerusalemu. Mudikire zimene Atate analonjeza.’
Atumwi akewo sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza. Moti anamufunsa kuti: ‘Kodi tsopano mukhala Mfumu ya Aisiraeli?’ Koma iye anawayankha kuti: ‘Nthawi ya Mulungu yoti ndikhale Mfumu sinakwane. Mudzalandira mphamvu ya mzimu ndipo mudzakhala mboni zanga. Mudzaphunzitsa anthu ku Yerusalemu, ku Yudeya, ku Samariya mpaka kumalekezero a dziko.’
Kenako Yesu anayamba kukwera kumwamba ndipo anabisika m’mitambo. Atumwi akewo ankangoyang’anabe kumwamba koma Yesu anali atapita.
Ndiyeno atumwiwo anachoka paphiri la Maolivi n’kupita ku Yerusalemu. Nthawi zonse ankakumana m’chipinda cham’mwamba n’kumapemphera. Ankadikira kuti Yesu awapatse malangizo ena.
“Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14
-