CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 11-18
Ndani Angakhale Mlendo M’chihema cha Yehova?
Kuti munthu akhale mlendo m’chihema cha Yehova ayenera kukhala mnzake wa Mulungu ndipo ayenera kumukhulupirira ndi kumumvera. Salimo 15 limafotokoza zimene Yehova amafuna kuti mabwenzi ake azichita.
MLENDO WA YEHOVA AYENERA . . .
kukhala ndi mtima wosagawanika
kunena zoona, ngakhale mumtima mwake
kulemekeza atumiki a Yehova anzake
kukwaniritsa zimene walonjeza ngakhale ataona kuti n’zovuta kuchita zimenezo
kuthandiza anthu ovutika popanda kuyembekezera kuti amubwezere
MLENDO WA YEHOVA AMAPEWA . . .
miseche ndi bodza
kuchitira anzake zoipa
kudyera masuku pamutu Akhristu anzake
kugwirizana ndi anthu amene satumikira kapena kumvera Yehova
kulandira ziphuphu