CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 69-73
Anthu a Mulungu ndi Odzipereka Potumikira Yehova
Tiyenera kumachita zinthu zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu
Pa moyo wake wonse, Davide anali wodzipereka kwambiri potumikira Yehova
Davide sankalola kuti anthu azinyoza dzina la Yehova
Akhristu achikulire angathandize achinyamata kukhala odzipereka
Munthu amene analemba Salimo limeneli, yemwe mwina ndi Davide, ankafunitsitsa kudzalimbikitsa m’badwo wa m’tsogolo
Makolo komanso Akhristu odziwa zambiri, angathandize achinyamata kuti azikonda Yehova