CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 74-78
Tizikumbukira Ntchito za Yehova
Tiziganizira zinthu zabwino zimene Yehova wachita
Tikamaganizira zimene tikuphunzira m’Mawu a Mulungu timamvetsa zimene tikuwerengazo komanso timayamba kuona kufunika kwa zimene Yehova amatiphunzitsa
Kuganizira mozama zokhudza Yehova kumatithandiza kuti tizikumbukira ntchito zodabwitsa zimene anachita komanso zimene walonjeza kuti adzachita m’tsogolo
Ntchito za Yehova ndi monga izi:
Kulenga
Tikamaphunzira zambiri zokhudza chilengedwe m’pamenenso timagoma ndi ntchito za Yehova
Kusankha amuna oti azitsogolera mumpingo
Tiyenera kumagonjera anthu amene Yehova wawasankha kuti azititsogolera
Kuteteza atumiki ake
Kukumbukira kuti Yehova amateteza atumiki ake kumatithandiza kuti tizimudalira kwambiri komanso kuti tisamakayikire kuti adzatiteteza