Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 2/15 tsamba 3
  • Kodi Mfundo za M’Baibulo N’zothandizabe Masiku Ano?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mfundo za M’Baibulo N’zothandizabe Masiku Ano?
  • Galamukani!—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Malangizo a M’Baibulo ndi Othandizabe Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
  • Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala
    Galamukani!—2013
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Makolo ndi Ana Ayenera Kulankhulana Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 2/15 tsamba 3
Baibulo lotsegula

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mfundo za M’baibulo N’zothandizabe Masiku Ano?

‘Ndinayamba kuona kuti ndine wosangalala kwambiri kuposa poyamba.’

HILTON ankakonda kwambiri masewera a nkhonya. Ali ndi zaka 7, anali katswiri wa masewerawa ndipo ankakondanso kuchita ndewu. Ali kusekondale, iye ndi anzake ankachita kuputa dala anthu n’cholinga choti amenyane nawo. Hilton anati: “Ndinkaba, kuonera zolaula, kuchitira akazi zachipongwe komanso kutukwana makolo anga. Chifukwa cha makhalidwe anga oipawa makolo anga ankaganiza kuti sindingasinthenso. Nditamaliza sukulu, ndinachoka panyumba.”

Patatha zaka 12, Hilton anabwereranso kwawo, koma makolo ake sanamuzindikire chifukwa anali atasintha kwambiri. Anali wodekha komanso waulemu. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti asinthe chonchi? Pa nthawi yomwe anachoka panyumba, anayamba kuganizira za kuipa kwa khalidwe lake. Anayambanso kuwerenga Baibulo kuti aone ngati lingamuthandize kusintha. Hilton anati: “Kuwerenga Baibulo kunandithandiza kudziwa kuti ndiyenera kusiya khalidwe langa. Komanso palemba la Aefeso 6:2, 3 ndinawerenga kuti ndiyenera kumalemekeza makolo anga, ndipo ndinayambadi kuchita zimenezi. Tsopano ndinayamba kuona kuti ndine wosangalala kwambiri kuposa poyamba. Makolo anganso anasangalala kwambiri ataona kuti ndasintha ndipo zinathandiza kuti asamadandaulenso ngati poyamba paja.”

Nkhani ya Hilton ikusonyeza kuti Baibulo lili ndi mphamvu yotha kusintha munthu ndipo mfundo zake n’zothandiza kwambiri. (Aheberi 4:12) Tiyeni tikambirane zina mwa mfundo zimenezi ndi kuona mmene zingatithandizire. Mfundo zake ndi kufunika kochita zinthu mwachilungamo, kusakwiya msanga, kukhulupirika m’banja komanso chikondi.

KODI BAIBULO LINATHA NTCHITO?

Bini yodzaza ndi zipangizo za kompyuta zotha ntchito

Anthu ena amaganiza kuti Baibulo linatha ntchito chifukwa lili ngati buku la malangizo a chipangizo chamakono chomwe anasiya kuchipanga. Koma zimenezi si zoona. Opanga zipangizo zamakono amasiya kupanga zipangizo zina n’kuyamba kupanga zatsopano. Zikatere, mabuku amalangizo a zipangizo zakale zija, amatha ntchito. Koma Baibulo silinathe ntchito chifukwa zimene anthu amafuna sizisintha. Mwachitsanzo kuyambira kale, anthu amafuna kukondedwa, amadana ndi kusakhulupirika m’banja komanso amafuna kuti anthu aziwachitira zinthu mokoma mtima. Choncho pa zinthu ngati zimenezi, “palibe chatsopano padziko lapansi pano.”—Mlaliki 1:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena