Mawu Oyamba
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
Kodi Baibulo ndi lachikale kapena ndi lothandizabe masiku ano? Baibulo limati: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16, 17.
Nsanja ya Olonda iyi ikusonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo anzeru komanso ikufotokoza zimene mungachite kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo.