Ntchito yolalikira uthenga wabwino ku Ghana
Zitsanzo za Ulaliki
NSANJA YA OLONDA
Funso: Anthu ena amaganiza kuti Baibulo ndi lachikale, pomwe ena amaona kuti ndi lothandizabe. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Lemba: 2 Tim. 3:16, 17
Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ikusonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo anzeru komanso ikufotokoza zimene mungachite kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo.
KUPHUNZITSA CHOONADI
Funso: Kodi n’zoona kuti mapeto a dzikoli ali pafupi?
Lemba: Mat. 24:3, 7, 14
Zoona Zake: Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Mfundoyi ndi yosangalatsa chifukwa ikusonyeza kuti mavuto athu atsala pang’ono kutha.
KODI MUKUFUNA KUDZIWA CHOONADI?
Perekani Kapepalako: Kapepalaka kali ndi malemba ena amene akuyankha funsoli komanso kali ndi mayankho a mafunso ena 5 ofunika kwambiri.
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.