Akulalikira munthu wothyola tiyi ku Cameroon
Zitsanzo za Ulaliki
NSANJA YA OLONDA
Funso: Kwa zaka zambiri, anthu ena akhala akuchita zinthu zosiyanasiyana kuti Baibulo lisapezekenso, koma mpaka pano lidakalipobe. Kodi umenewu si umboni wokwanira woti linachokeradi kwa Mulungu?
Lemba: Yes. 40:8
Perekani Magaziniyo: Nkhani zomwe zili m’magaziniyi zikufotokoza zimene anthu akhala akuchita pofuna kuti Baibulo lisapezekenso.
NSANJA YA OLONDA (tsamba lomaliza)
Funso: Ndikufuna kumva maganizo anu pa funso ili. [Werengani funso loyamba patsamba 16.] Anthu ena amakhulupirira kuti anthu ndi amene anayambitsa zipembedzo. Koma ena amaganiza kuti Mulungu ndi amene anayambitsa chipembedzo kuti anthu azimulambira. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Lemba: Yak. 1:27
Perekani Magaziniyo: Nkhaniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi. Ndidzabweranso kuti tidzakambirane mfundo zina za m’nkhaniyi.
UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU
Funso: Nkhani zimene anthu amawerenga m’nyuzipepala masiku ano ndi zimene Baibulo linaneneratu. Kodi ndi zinthu ziti zimene Baibulo linaneneratu zomwe inuyo munamva kapena kuona zikuchitika?
Lemba: 2 Tim. 3:1-5
Perekani Kabukuko: Kabukuka kakufotokoza kuti anthu amene amakonda Mulungu amaona kuti zikuchitikazi ndi chizindikiro choti tili m’masiku otsiriza. [Muonetseni funso lachiwiri pamutu woyamba.]
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.