MUTU 6
Anthu 8 Anapulumuka
Nowa ndi banja lake analowa m’chingalawa limodzi ndi nyama. Yehova anatseka chitseko cha chingalawacho ndipo mvula inayamba kugwa. Mvulayo inali yambiri moti chingalawa chija chinayamba kuyandama. Kenako madzi anamiza nthaka yonse. Anthu oipa onse amene anali kunja kwa chingalawacho anafa. Koma Nowa ndi banja lake anapulumuka. Iwo ayenera kuti anasangalala kwambiri podziwa kuti anamvera Yehova.
Mvulayo inagwa kwa masiku 40, masana ndi usiku. Kenako inasiya ndipo madzi anayamba kuphwera. Ndiyeno chingalawacho chinaima paphiri. Koma padzikoli panali padakali madzi ambiri, choncho Nowa ndi banja lakelo anakhalabe m’chingalawacho.
Madziwo ankaphwera pang’onopang’ono. Nowa ndi banja lakelo anakhala m’chingalawacho kupitirira chaka chimodzi. Kenako Yehova anawauza kuti atuluke ndipo zinali ngati akulowa m’dziko latsopano. Iwo anathokoza kwambiri Yehova chifukwa chowapulumutsa moti anapereka nsembe.
Yehova anasangalala kwambiri ndi nsembeyo. Iye analonjeza kuti sadzagwiritsanso ntchito chigumula powononga zinthu padzikoli. Potsimikizira zimenezi, anachititsa kuti kumwamba kuoneke utawaleza woyambirira. Kodi iweyo unaonapo utawaleza?
Kenako Yehova anauza Nowa ndi banja lake kuti akhale ndi ana n’kudzaza dziko lapansi.
“Nowa analowa mʼchingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinkachitika mpaka Chigumula chinafika nʼkuwaseseratu onsewo.”—Mateyu 24:38, 39