MUTU 7
Nsanja ya ku Babele
Chigumula chitatha, ana a Nowa anabereka ana ambiri. Choncho anawo anayamba kukhala m’madera osiyanasiyana padziko lapansi. Izi ndi zimene Yehova anawauza.
Koma panali anthu ena amene sanamvere Yehova. Iwo anauzana kuti: ‘Tiyeni timange mzinda kuti tizingokhala pompano. Timange nsanja yaitali yoti mpaka ikafike kumwamba. Tikatero titchuka.’
Yehova sanasangalale ndi zimene anthuwa ankachita ndipo anaganiza zowaletsa. Kodi ukudziwa zimene anachita? Yehova anachititsa kuti mwadzidzidzi anthuwo ayambe kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana. Popeza sankathanso kumvana, anasiya ntchito yomangayo. Mzinda umene ankamangawo unatchedwa Babele kutanthauza “Chisokonezo.” Ndiyeno anthuwo anayamba kuchoka n’kumakakhala m’malo osiyanasiyana padziko lapansili. Koma anapitirizabe kuchita zoipa m’madera osiyanasiyana amene ankakhala. Kodi panali ena amene ankakondabe Yehova? Tikambirana zimenezi m’mutu wotsatira.
“Aliyense wodzikweza adzachititsidwa manyazi, koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.”—Luka 18:14