MUTU 2
Mulungu Analenga Mwamuna ndi Mkazi Oyamba
Yehova anakonza munda wa Edeni. M’mundamo munali maluwa, mitengo ndiponso nyama zosiyanasiyana. Kenako Mulungu anatenga dothi n’kuumba munthu ndipo anamupatsa dzina lakuti Adamu. Iye anauzira mpweya m’mphuno mwa Adamuyo. Ukudziwa zimene zinachitika? Munthuyo anakhala wamoyo. Yehova anauza Adamu kuti aziyang’anira mundawo komanso kuti nyama iliyonse aipatse dzina.
Koma Yehova anamupatsanso lamulo lofunika kwambiri lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya, kupatula za mtengo umodzi wokha. Ukadzadya zipatso za mtengo umenewu udzafa.’
Kenako Yehova ananena kuti: ‘Ndikufuna ndipange mnzake wa Adamu kuti azimuthandiza.’ Ndiyeno anamugonetsa kwambiri Adamuyo. Kenako anamuchotsa nthiti ndipo anagwiritsa ntchito nthitiyo n’kumupangira mkazi. Mkaziyo dzina lake anali Hava. Choncho Adamu ndi Hava anali banja loyamba. Kodi Adamu anamva bwanji Mulungu atamupangira mkazi? Anasangalala kwambiri moti ananena kuti: ‘Ndikusangalala kwambiri kuti Yehova wagwiritsa ntchito nthiti yanga n’kundipangira mkazi. Tsopano ndapeza mnzanga.’
Yehova anauza Adamu ndi Hava kuti abereke ana ndipo adzaze dziko lapansi. Iye ankafuna kuti anthuwo azigwira ntchito limodzi mosangalala n’kukonza dziko lonse kuti likhale paradaiso wokongola ngati munda wa Edeni. Koma zinthu sizinayende mmene Yehova ankafunira. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Tidzakambirana m’mutu wotsatira.
“Amene analenga anthu pachiyambi anawalenga mwamuna ndi mkazi.”—Mateyu 19:4