Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 2 tsamba 10-tsamba 11 ndime 1
  • Mulungu Analenga Anthu Awiri Oyamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Analenga Anthu Awiri Oyamba
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mwamuna ndi Mkazi Oyamba
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kufa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa—Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 2 tsamba 10-tsamba 11 ndime 1
Adamu ndi Hava ali m’munda wa Edeni

MUTU 2

Mulungu Analenga Mwamuna ndi Mkazi Oyamba

Yehova anakonza munda wa Edeni. M’mundamo munali maluwa, mitengo ndiponso nyama zosiyanasiyana. Kenako Mulungu anatenga dothi n’kuumba munthu ndipo anamupatsa dzina lakuti Adamu. Iye anauzira mpweya m’mphuno mwa Adamuyo. Ukudziwa zimene zinachitika? Munthuyo anakhala wamoyo. Yehova anauza Adamu kuti aziyang’anira mundawo komanso kuti nyama iliyonse aipatse dzina.

Koma Yehova anamupatsanso lamulo lofunika kwambiri lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya, kupatula za mtengo umodzi wokha. Ukadzadya zipatso za mtengo umenewu udzafa.’

Kenako Yehova ananena kuti: ‘Ndikufuna ndipange mnzake wa Adamu kuti azimuthandiza.’ Ndiyeno anamugonetsa kwambiri Adamuyo. Kenako anamuchotsa nthiti ndipo anagwiritsa ntchito nthitiyo n’kumupangira mkazi. Mkaziyo dzina lake anali Hava. Choncho Adamu ndi Hava anali banja loyamba. Kodi Adamu anamva bwanji Mulungu atamupangira mkazi? Anasangalala kwambiri moti ananena kuti: ‘Ndikusangalala kwambiri kuti Yehova wagwiritsa ntchito nthiti yanga n’kundipangira mkazi. Tsopano ndapeza mnzanga.’

Yehova anauza Adamu ndi Hava kuti abereke ana ndipo adzaze dziko lapansi. Iye ankafuna kuti anthuwo azigwira ntchito limodzi mosangalala n’kukonza dziko lonse kuti likhale paradaiso wokongola ngati munda wa Edeni. Koma zinthu sizinayende mmene Yehova ankafunira. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Tidzakambirana m’mutu wotsatira.

“Amene analenga anthu pachiyambi anawalenga mwamuna ndi mkazi.”​—Mateyu 19:4

Mafunso: Kodi Yehova anapatsa Adamu ntchito yotani? Kodi Mulungu ananena kuti n’chiyani chidzachitike Adamu ndi Hava akadzadya zipatso za mtengo umene anawaletsa?

Genesis 1:27-31; 2:7-9, 15-23; Salimo 115:16; Mateyu 19:4-6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena