Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm gawo 7 tsamba 10
  • Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Nkhani Yofanana
  • Phunzirani Njira za Yehova
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Mose Anasankha Kuti Azilambira Yehova
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Mose ndi Aroni Aona Farao
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Eksodo
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm gawo 7 tsamba 10
Mose wanyamula miyala iwiri pamene pali Malamulo Khumi

GAWO 7

Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli

Yehova anabweretsa miliri m’dziko la Iguputo, ndipo Mose anatsogolera ana a Isiraeli potuluka m’dzikomo. Mulungu anapereka Chilamulo kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose

ANA a Isiraeli anakhala ku Iguputo kwa zaka zambiri ndipo zinthu zinkawayendera bwino ndiponso anachulukana. Komabe, Farao watsopano anayamba kulamulira dzikolo ndipo iye sankadziwa Yosefe. Farao ameneyu anali wankhanza kwambiri ndipo anasandutsa Aisiraeli kukhala akapolo komanso analamula kuti ana awo onse aamuna akhanda aziwaponya mumtsinje wa Nailo. Iye anachita zimenezi chifukwa ankaopa Aisiraeli omwe ankachuluka kwambiri. Koma mayi wina wolimba mtima anateteza mwana wake wamwamuna wakhanda pomuika mukabokosi, ndipo anakabisa kabokosiko m’mabango. Kenako mwana wamkazi wa Farao atapeza mwanayo, anam’tenga n’kumupatsa dzina lakuti Mose, ndipo anamulera m’banja lachifumu ku Iguputo komweko.

Mose atafika zaka 40, analowa m’mavuto chifukwa anayesa kuteteza kapolo wachiisiraeli amene ankazunzidwa ndi woyang’anira ntchito wa ku Iguputo. Chifukwa cha zimenezi, Mose anathawa n’kukakhala kudziko lina lakutali kwambiri. Koma Mose ali ndi zaka 80, Yehova anamuuza kuti abwerere ku Iguputo kukauza Farao kuti amasule anthu a Mulungu mu ukapolo.

Farao anakanitsitsa kwa mtu wagalu ndipo Mulungu anabweretsa miliri 10 m’dziko la Iguputo. Nthawi iliyonse imene Mose anapita kukaonekera kwa Farao kukam’pempha kuti amasule Aisiraeli, zomwe zikanamuthandiza kupewa mliri wina, Farao ankakana mwamwano kumvera Mose ndi Mulungu wake Yehova. Kenako, mliri womaliza unapha ana onse oyamba kubadwa m’dzikolo, kupatulapo ana a m’mabanja amene anapaka magazi a nkhosa pafelemu pomvera lamulo la Yehova. Mngelo wa Mulungu amene ankapha ana onse oyamba kubadwa, anapitirira nyumba zimenezi. Kenako Aisiraeli anayamba kuchita chikondwerero cha Pasika chaka ndi chaka pokumbukira kupulumutsidwa kodabwitsa kumeneku.

Mwana wa Farao wamwamuna woyamba kubadwa ataphedwa pa mliriwo, iye analamula Mose ndi ana onse a Isiraeli kuti achoke m’dziko la Iguputo. Nthawi yomweyo Mose anasonkhanitsa khamu la anthu n’kuyamba ulendo wotuluka m’dzikolo. Koma kenako Farao anasintha maganizo ndipo anayamba kuwatsatira ali ndi asilikali ndiponso magaleta ambiri. Aisiraeli atafika pamalo ena m’mbali mwa Nyanja Yofiira, ankaoneka ngati alibe kothawira. Kenako Yehova analekanitsa Nyanja Yofiira kuti Aisiraeli adutse pouma, pakati pa makoma awiri a madzi. Koma nawonso Aiguputo atalowa m’nyanjayo potsatira Aisiraeli, Mulungu anachititsa kuti madzi aja abwerere ngati mmene analili poyamba ndipo Farao pamodzi ndi asilikali ake anamira.

Kenako Aisiraeli anasonkhana m’mbali mwa phiri la Sinai ndipo Yehova anachita nawo pangano. Kudzera mwa Mose, Mulungu anapereka malamulo kwa Aisiraeli kuti aziwatsogolera komanso kuwateteza pa moyo wawo watsiku ndi tsiku. Ngati Aisiraeli akanapitiriza kuvomereza mokhulupirika ulamuliro wa Yehova Mulungu, iye akanapitiriza kukhala nawo ndiponso akanadalitsa anthu ena kudzera mumtunduwo.

Komabe, Aisiraeli ambiri anakhumudwitsa Mulungu chifukwa chosamukhulupirira. Motero, Yehova anachititsa kuti anthu a m’badwo umenewo azingoyenda m’chipululu mpaka zaka 40. Ndiyeno Mose anasankha Yoswa, yemwe anali wolungama, kuti apitirize kutsogolera Aisiraeli. Kenako nthawi inakwana yakuti Aisiraeli alowe m’dziko limene Mulungu analonjeza Abulahamu.

​—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Ekisodo, Levitiko, Numeri, Deuteronomo komanso pa Salimo 136:10-15 ndi pa Machitidwe 7:17-36.

  • Kodi chinachitika n’chiyani kuti Mulungu agwiritse ntchito Mose populumutsa Aisiraeli?

  • N’chifukwa chiyani Aisiraeli anayamba kuchita mwambo wa Pasika?

  • Kodi Yehova anapulumutsa bwanji Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo?

LAMULO LALIKULU KWAMBIRI

Pa malamulo okwana pafupifupi 600, amene Mulungu anapereka kudzera mwa Mose, Malamulo Khumi amene analembedwa pa Ekisodo 20:1-17, angakhale odziwika bwino kwambiri. Komabe, anthu ena atafunsa Yesu Khristu kuti lamulo lalikulu kwambiri pa malamulo onse a Mulungu ndi liti, iye anasankha lamulo limodzi lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.”—Maliko 12:28-30; Deuteronomo 6:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena