Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Yona
1. Kodi Yona anali ndi makhalidwe abwino ati?
1 Kodi n’chiyani chimene mumaganizira mukamva za mneneri Yona? Anthu ena amaganiza kuti anali munthu wamantha kapena wouma mtima. Komabe, iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa, wolimba mtima komanso wodzipereka. Choncho, kodi ‘tingatengere’ bwanji makhalidwe ake abwino amenewa?—Yak. 5:10.
2. Kodi tingatengere bwanji kudzichepetsa kwa Yona?
2 Anali Wodzichepetsa: Poyamba, Yona anathawira kwina posafuna kupita kudera limene anatumidwa. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Asuri anali anthu achiwawa ndipo mzinda wa Nineve unkatchedwa “mzinda wokhetsa magazi.” (Nah. 3:1-3) Komabe, Yehova atamudzudzula, Yona sanakanenso kupita kumene anauzidwa. Zimenezi zikusonyeza kuti iye anali wodzichepetsa. (Miy. 24:32; Yona 3:1-3) Ngakhale kuti poyamba Yona anathawa, pamapeto pake anachita zimene Yehova anamuuza. (Mat. 21:28-31) Kodi ifenso timakhala odzipereka kulalikira uthenga wabwino ngakhale titapatsidwa uphungu winawake kapena tikulalikira m’gawo limene anthu ake safuna kumva uthenga wathu?
3. Kodi ndi mbali ziti za utumiki wanu zimene zimafuna kuti mukhale wolimba mtima komanso wodzipereka?
3 Anali Wolimba Mtima Komanso Wodzipereka: Pamene Yona anaona kuti anthu amene anali m’chombocho akhoza kufa chifukwa cha zimene iye anachita, analolera kufa m’malo mophetsa anthu ena. (Yona 1:3, 4, 12) Kenako, Yona atapita ku Nineve kukagwira ntchito imene Yehova anamuuza, anapita mkatikati mwa mzinda, mwina poona kuti malowo ndiye anali abwino olengezera uthenga wa chiweruzo cha Yehova. Zimenezitu zikusonyeza kuti Yona sanali wamantha, koma anali mneneri wolimba mtima. (Yona 3:3, 4) Nanga bwanji ife masiku ano? Kulimba mtima n’kofunika kuti tizitha kulalikira molimba mtima tikakumana ndi anthu amene amatsutsa ntchito yathu. (Mac. 4:29, 31) Timafunika kukhala odzipereka kuti tizitha kupeza nthawi komanso kugwiritsa ntchito chuma chathu mu utumiki.—Mac. 20:24.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeza nthawi yophunzira pa zitsanzo zabwino za aneneri a Yehova?
4 Kuti mupindule ndi nkhani inayake yokhudza mneneri wa Yehova, nthawi zonse muziona mmene mukanachitira zikanakhala kuti zinthuzo zikuchitikira inuyo. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndikanakhala ine ndikanatani? Kodi ndingatengere bwanji makhalidwe ake abwino?’ (Aheb. 6:11, 12) M’tsogolomu, tidzaphunzira za aneneri ena okhulupirika a Yehova m’nkhani zina za mu Utumiki Wathu wa Ufumu.