Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 5 tsamba 18-tsamba 19 ndime 5
  • Chingalawa cha Nowa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chingalawa cha Nowa
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Nowa Akhoma Chingalawa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Chigumula Chisanachitike, Kodi Ndani Anamvera Mulungu Ndipo Ndani Amene Sanamumvere?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Madzi Alisesa Dziko
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • “Nowa Anayenda ndi Mulungu Woona”
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 5 tsamba 18-tsamba 19 ndime 5
Nowa ndi banja lake akukhoma chingalawa

MUTU 5

Chingalawa cha Nowa

Patapita nthawi, anthu anachuluka padzikoli, koma ambiri ankachita zoipa. Ngakhalenso angelo ena anayamba kuchita zoipa. Iwo anachoka kumwamba n’kubwera padziko lapansi. Kodi ukudziwa chifukwa chake angelowa anachita zimenezi? Ankafuna kuti adzakhale ndi matupi ngati a anthu n’cholinga choti akwatire akazi a padziko lapansi.

Angelowo atakwatira akaziwo, anabereka ana. Anawo anali ataliatali komanso amphamvu kwambiri ndipo ankavutitsa komanso kuzunza anthu. Yehova sanalole kuti zimenezi zipitirire. Choncho anaganiza zobweretsa chigumula kapena kuti chimvula champhamvu kuti chiwononge anthu oipawo.

Nowa ndi banja lake akukhoma chingalawa komanso kukonza chakudya

Koma panali munthu wina yemwe sankachita zoipa ndipo ankakonda Yehova. Dzina lake anali Nowa. Iye anali ndi mkazi ndi ana aamuna atatu. Mayina awo anali Semu, Hamu ndi Yafeti ndipo onsewa anali ndi akazi. Yehova anauza Nowa kuti apange chingalawa choti iye ndi banja lake apulumukiremo. Chingalawacho chinkaoneka ngati chibokosi chachikulu choti chingathe kuyandama pamadzi. Yehova anauzanso Nowa kuti alowetse nyama zambiri m’chingalawamo kuti nazonso zipulumuke.

Nthawi yomweyo, Nowa anayamba kukhoma chingalawacho. Iye ndi banja lake anagwira ntchitoyi kwa zaka 50. Popanga chingalawacho anatsatira malangizo onse a Yehova. Pa nthawi imeneyo, Nowa ankachenjezanso anthu kuti kubwera Chigumula. Koma palibe amene anamumvera.

Kenako inafika nthawi yoti alowe m’chingalawamo. M’mutu wotsatira tiona zimene zinachitika.

“Mofanana ndi mmene masiku a Nowa analili, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.”​—Mateyu 24:37

Mafunso: N’chifukwa chiyani Yehova anaganiza zobweretsa Chigumula? Kodi Yehova anapereka malangizo otani kwa Nowa?

Genesis 6:1-22; Mateyu 24:37-41; 2 Petulo 2:5; Yuda 6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena