Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 8 tsamba 26-tsamba 27 ndime 1
  • Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Abulahamu Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Abrahamu—Bwenzi la Mulungu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Abrahamu ndi Sara Mungatsanzire Chikhulupiriro Chawo!
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Abulahamu Anali “Bwenzi” la Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 8 tsamba 26-tsamba 27 ndime 1
Abulahamu ndi Sara akulongedza katundu wawo kuti achoke ku Uri

MUTU 8

Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu

Pafupi ndi mzinda wa Babele panali mzinda wina wotchedwa Uri. Anthu a mumzinda umenewu ankalambira milungu ina yambiri koma sankalambira Yehova. Koma mumzindawu munali munthu wina amene ankalambira Yehova yekha. Dzina lake anali Abulahamu.

Tsiku lina Yehova anauza Abulahamu kuti: ‘Samuka mʼdziko lako ndi kuchoka pakati pa abale ako ndipo upite kudziko limene ndidzakuonetse.’ Kenako Mulungu anamulonjeza kuti: ‘Ndidzapangitsa kuti ukhale mtundu waukulu, ndipo anthu ambiri padziko lonse lapansi ndidzawachitira zinthu zabwino chifukwa cha iwe.’

Abulahamu sankadziwa kumene Yehova ankafuna kuti apite, koma ankakhulupirira kwambiri Yehovayo. Choncho iye ndi mkazi wake, Sara analongedza katundu n’kuyamba ulendo wautali. Pa ulendowu ananyamukanso ndi bambo ake, dzina lawo a Tera komanso Loti yemwe anali mwana wa mng’ono wake.

Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu ali ndi zaka 75. Ndipo iye ndi banja lake atayenda kwa nthawi yaitali, anafika m’dziko limene Yehova anawauza. Dziko lake linali la Kanani. Ali kumeneko, Mulungu analankhula ndi Abulahamu n’kumulonjeza kuti: ‘Dziko lonseli ndidzalipereka kwa ana ako.’ Komatu pa nthawiyi Abulahamu ndi Sara n’kuti ali okalamba ndipo analibe ana. Ndiye kodi Yehova akanakwaniritsa bwanji lonjezo lakeli?

Abulahamu ndi banja lake ali pa ulendo wopita ku Kanani

“Chifukwa cha chikhulupiriro, Abulahamu . . . anamvera nʼkupita kumalo amene ankayembekezera kuwalandira ngati cholowa. Iye anapitadi, ngakhale kuti sankadziwa kumene akupita.”​—Aheberi 11:8

Mafunso: Kodi Yehova anauza Abulahamu kuti achite chiyani? Kodi Yehova analonjeza Abulahamu zinthu ziti?

Genesis 11:29-32; 12:1-9; Machitidwe 7:2-4; Agalatiya 3:6; Aheberi 11:8

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena