Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 January tsamba 2
  • Tizigwira Nawo Ntchito Yomanga Komanso Kukonza Malo Olambirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizigwira Nawo Ntchito Yomanga Komanso Kukonza Malo Olambirira
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE TINGACHITE
  • Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Malo Olambirira Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Pakufunika Kumanga Nyumba za Ufumu Mofulumira
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 January tsamba 2

MOYO WACHIKHRISTU

Tizigwira Nawo Ntchito Yomanga Komanso Kukonza Malo Olambirira

Ntchito yomanga kachisi wa Yehova inali yaikulu. Koma Aisiraeli anadzipereka kwambiri mpaka anamaliza. (1 Mbiri 29:2-9; 2 Mbiri 6:7, 8) Kachisiyu atamalizidwa, ankafunika kukonzedwanso. Ndiyeno zimene Aisiraeli ankachita pa ntchito yokonzayi zinkasonyeza ngati amakonda Yehova kapena ayi. (2 Maf. 22:3-6; 2 Mbiri 28:24; 29:3) Masiku anonso, Akhristu amadzipereka kwambiri pa ntchito yomanga, kukonza komanso kuyeretsa Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano. Ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito zimenezi chifukwa ndi utumiki wopatulika.—Sal. 127:1; Chiv. 7:15.

ZIMENE TINGACHITE

  • Akuyeretsa pamene anakhala m’Nyumba ya Ufumu

    Kuyeretsa malo tikangomaliza misonkhano. Ngati tilibiretu nthawi tikhoza kungotola tizinyalala pafupi ndi pamene takhala.

  • Akuyeretsa Nyumba ya Ufumu

    Tizigwira nawo ntchito yoyeretsa kapena kukonza Nyumba ya Ufumu. Ntchito ikamagwiridwa ndi anthu ambiri imasangalatsa komanso imapepuka.—lv 92-93 ndime 18.

  • Akuponya ndalama m’bokosi

    Tizipereka ndalama zothandiza pa ntchitoyi. Yehova amasangalala kwambiri ngakhale ndalama zathuzo zitakhala ngati ‘timakobidi tiwiri tating’ono.’—Maliko 12:41-44.

  • Akukonza malo olambirira

    Ngati n’zotheka tizidzipereka kugwira nawo ntchito yomanga komanso kukonza malo olambirira. Sikuti tiyenera kukhala ndi luso lapadera kuti tigwire nawo ntchitoyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena