Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzikonzekera Mawu Oyamba
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Mawu athu oyamba akakhala osakopa chidwi, munthu amene tikumulalikirayo akhoza kutiuza kuti sakufuna kuti tikambirane naye. Choncho ofalitsa ambiri amaona kuti mawu oyamba okopa chidwi ndi ofunika kwambiri. Ngakhale kuti mu Utumiki Wathu wa Ufumu komanso m’buku la Kukambitsirana mumakhala zitsanzo za ulaliki, zitsanzozi sizikhala ndi mawu oyamba okwanira oti tingathe kuwagwiritsa ntchito pa nyumba iliyonse. Ngakhale zitakhala kuti chitsanzo cha ulaliki chili ndi zonse, ofalitsa angathe kuchisintha zina ndi zina kapena kukonza okha ulaliki umene akufuna kugwiritsa ntchito pa tsikulo. Choncho tingachite bwino kumakonzekera mawu oyamba okopa chidwi, m’malo momangonena zilizonse zimene zabwera m’maganizo mwathu tikafika pakhomo la munthu. Kukonzekera mawu oyamba kungathandize kuti tizilalikira mogwira mtima.—Miy. 15:28.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Mukamachita kulambira kwa pabanja, muzipatula nthawi yokonzekera mawu oyamba amene mungakagwiritse ntchito mu utumiki.
Mukakhala mu utumiki, uzani amene mwayenda nayeyo mawu oyamba amene mwakonzekera. (Miy. 27:17) Mukaona kuti mawu oyamba amene munakonzekera sakuthandiza, khalani wokonzeka kusintha.