Mmene Tingafotokozere Zimene Timakhulupirira Zokhudza Chaka cha 1914
Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tizikhala okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene watifunsa’ zomwe timakhulupirira. Koma amati tizichita zimenezi “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.” (1 Pet. 3:15) Komabe, nthawi zina zimakhala zovuta kufotokoza mfundo zozama za choonadi. Mfundo zimenezi ndi monga yoti, ‘Kodi timadziwa bwanji kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914?’ Pofuna kutithandiza kuti tizitha kufotokoza mfundo zimenezi bwinobwino, patuluka nkhani za mutu wakuti: “Kucheza ndi Munthu Wina—Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira?” Nkhanizi zili mu Nsanja ya Olonda ya October ndi ya November, 2014. Mukamawerenga nkhanizi, ganizirani mayankho a mafunso otsatirawa okhudza zimene Cameron anachita.
Kodi Cameron . . .
anagwiritsa ntchito bwanji mawu oyamikira pofuna kuti apeze poyambira pabwino?—Mac. 17:22.
anasonyeza bwanji kudzichepetsa pomwe ankafotokoza zimene amakhulupirira?—Mac. 14:15.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti anachita bwino . . .
kumabwereza mwachidule zimene akambirana?
kumaima kaye n’kufunsa munthuyo ngati ali limodzi?
kupewa kufotokoza zinthu zambiri nthawi imodzi?—Yoh. 16:12.
Tikuthokoza kwambiri Yehova, yemwe ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ chifukwa amatithandiza kudziwa mmene tingafotokozere mfundo zozama za m’Baibulo kwa anthu amene ali ndi njala yauzimu.—Yes. 30:20.