Ndandanda ya Mlungu wa October 27
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 27
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 3 ndime 11-18 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 11-13 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: “Kodi Tingatani Kuti Tiziona Kuti Ntchito Yolalikira Ndi Yofunika Kwambiri?” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akugawira buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena kapepala kalikonse.
Mph. 15: Muzikonzekera Bwino Kuti Muzilalikira Modzipereka. Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2014, tsamba 14-15, ndime 14 mpaka 20. Pemphani omvera kuti anene nkhani kapena mafunso amene anthu a m’dera lanu amaganizira nthawi zambiri. Kodi tingathandize bwanji anthu amenewa tikamalalikira? Pemphani apainiya awiri kapena mwamuna ndi mkazi wake kuti achite chitsanzo chosonyeza mmene ofalitsa angagwiritsire ntchito ndime zimenezi kukonzekera ulaliki wogwira mtima kwa anthu a m’dera lanu. Ochita chitsanzochi angasankhe buku limene angagwiritse ntchito.
Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero