Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira October 27, 2014.
Malinga ndi Numeri 21:5, n’chifukwa chiyani Aisiraeli ankadandaulira Mulungu ndi Mose, nanga ife tikuphunzirapo chiyani? [Sept. 1, w99 8/15 tsa. 26-27]
N’chifukwa chiyani Yehova anakwiyira Balamu? (Num. 22:20-22) [Sept. 8, w04 8/1 tsa. 27 ndime 2]
Kodi lemba la Numeri 25:11 limasonyeza kuti Pinihasi anali ndi mtima wotani, nanga tingamutsanzire bwanji? [Sept. 8, w04 8/1 tsa. 27 ndime 4]
Kodi Mose anapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya kudzichepetsa? (Num. 27:5, 15-18) [Sept. 15, w13 2/1 tsa. 5]
Kodi Yoswa ndi Kalebe anasonyeza bwanji kuti anthu omwe si angwiro akhoza kutsatira mfundo za Mulungu ngakhale pamene akutsutsidwa? (Num. 32:12) [Sept. 22, w93 11/15 tsa. 14 ndime 13]
Kodi mfundo yakuti ana a Tselofekadi anali omvera ingathandize bwanji Mkhristu amene sali pa banja? (Num. 36:10-12) [Sept. 29, w08 2/15 tsa. 4-5 ndime 10]
Kodi Aisiraeli anakumana ndi zotani chifukwa chong’ung’udza ndiponso kukhala ndi mtima wodandauladandaula? Nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi? (Deut. 1:26-28, 34, 35) [Oct. 6, w13 8/15 tsa. 11 ndime 7]
Kodi Aisiraeli anayenera kuchita zinthu ziwiri ziti kuti Yehova awadalitse ndiponso kuti adzakhale ndi moyo wabwino m’Dziko Lolonjezedwa? (Deut. 4:9) [Oct. 13, w06 6/1 tsa. 29 ndime 15]
Kodi zinatheka bwanji kuti zovala za Aisiraeli zisathe ndiponso mapazi awo asatupe pamene ankayenda m’chipululu? (Deut. 8:3, 4) [Oct. 20, w04 9/15 tsa. 26 ndime 1]
Kodi tingatsatire bwanji malangizo amene Aisiraeli anapatsidwa akuti ‘azimamatira’ Yehova? (Deut. 13:4, 6-9) [Oct. 27, w02 10/15 tsa. 16 ndime 14]