Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ana ayenera kuphunzitsidwa zinthu ziti kuti akule mwauzimu?
Makolo achikhristu amayesetsa kulera ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Mwachitsanzo, makolo ena amaona kuti zimathandiza kukambirana ndi ana awo lemba la tsiku m’mawa uliwonse. Pa nthawi ya kulambira kwa pabanja kapena pa nthawi ina, amaonera vidiyo inayake n’kukambirana zimene aonerazo. Amaphunziranso nkhani zina m’buku la Zimene Achinyamata Amafunsa, kuchita sewero la nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kuyeserera mmene anawo angayankhire wina atawafunsa funso pa nkhani ina. Koma kuti ana ‘akhwime mwauzimu,’ ayeneranso kuphunzitsidwa mfundo zozama za m’Baibulo.—Aheb. 6:1.
Taganizirani zimene timaphunzitsa anthu amene timakumana nawo mu utumiki. Pa ulendo woyamba kapena wobwereza, timayesetsa kuyambitsa phunziro pogwiritsa ntchito buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Tikamaliza buku limeneli, timayamba kuphunzira nawo buku lakuti, “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu.” Kodi n’chifukwa chiyani timachita zimenezi? Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, limathandiza munthu kudziwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Pamene buku la ‘Chikondi cha Mulungu,’ limathandiza munthu kudziwa mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Kuphunzira mabuku awiriwa kumathandiza anthu atsopano kuti akhale “ozikika” mwa Khristu komanso kuti ‘akhazikike m’chikhulupiriro.’ (Akol. 2:6, 7) Kodi si zoona kuti mabuku amenewa angathandizenso ana anu? Nawonso amafunika kuphunzitsidwa zokhudza dipo, Ufumu wa Mulungu komanso zimene zimachitika munthu akamwalira. Ayeneranso kudziwa chifukwa chake Mulungu walola kuti padzikoli pazichitika mavuto komanso chifukwa chake timakhulupirira kuti ano ndi masiku otsiriza. Ayenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa ndi choonadi. Ana afunikanso kumvetsa mfundo za m’Baibulo komanso kuphunzitsa “mphamvu zawo za kuzindikira.” (Aheb. 5:14) N’zoona kuti makolo ayenera kuganizira msinkhu wa ana awo komanso zinthu zimene anawo angathe kuzimvetsa. Komabe ana ambiri angathe kuphunzira mfundo zozama za m’Baibulo ngakhale ali aang’ono.—Luka 2:42, 46, 47.
Pofuna kuthandiza makolo kuphunzitsa ana awo, pa webusaiti yathu ya jw.org/ny pakupezeka zinthu zothandiza kuphunzira Baibulo zomwe mfundo zake zachokera m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kuti mupeze zinthu zimenezi, pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA. M’tsogolomu, pa webusaitiyi pazidzapezekanso zinthu zothandiza kuphunzira Baibulo zomwe mfundo zake zizidzachokera m’buku la ‘Chikondi cha Mulungu.’ Koma mungathenso kugwiritsa ntchito mabuku awiriwa pophunzitsa ana anu. Makolo angasankhe kugwiritsa ntchito zinthu zopezeka pa webusaitizi pochita Kulambira kwa Pabanja, kuphunzira Baibulo ndi mwana wina kapena pophunzitsa mwana kuphunzira payekha.