Ndandanda ya Mlungu wa June 2
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 2
Nyimbo Na. 22 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 12 ndime 8-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ekisodo 38-40 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 40:20-38 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Sabata Limatanthauza Chiyani kwa Akhristu?—rs tsa. 349 ndime 3—tsa. 350 ndime 2; mfundozi zafotokozedwanso mu w11 7/15 tsa. 28 ndime 16-17 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Nkhani za Anthu Amene Anaukitsidwa Zopezeka M’Baibulo?—bh tsa. 70-71 ndime 11-15 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a June. Nkhani yokambirana. Pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino, yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwo. Kenako kambiranani zitsanzozo, kuyambira poyamba mpaka pamapeto. Pomaliza, limbikitsani ofalitsa onse kuti awerenge magaziniwo n’cholinga choti awadziwe bwino komanso alimbikitseni kuti adzagawire nawo magaziniwa.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzikonzekera Mawu Oyamba.” Kenako apempheni kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo.
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero