Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rj gawo 5 tsamba 12-15
  • Bwererani kwa ‘M’busa Wanu ndi Woyang’anira Moyo Wanu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwererani kwa ‘M’busa Wanu ndi Woyang’anira Moyo Wanu’
  • Bwererani kwa Yehova
  • Nkhani Yofanana
  • “Bwererani Kwa Ine”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Adzakulimbitsa
    Imbirani Yehova Mosangalala
  • Mulungu Adzakupatsani Mphamvu
    Imbirani Yehova
  • Yehova Amakuonani Kuti Ndinu Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Bwererani kwa Yehova
rj gawo 5 tsamba 12-15

GAWO 5

Bwererani kwa ‘M’busa Wanu ndi Woyang’anira Moyo Wanu’

Kodi inuyo mwakumanapo ndi mavuto ena amene atchulidwa m’kabukuka? Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Atumiki a Mulungu ambirimbiri akale ndiponso a masiku ano akumanapo ndi mavuto ngati amenewa. Yehova anawathandiza ndipo akhoza kukuthandizaninso inuyo.

Yehova adzakulandirani bwino mukabwerera kwa iye

DZIWANI kuti Yehova adzakulandirani bwino mukabwerera kwa iye. Adzakuthandizani kuti musiye kuda nkhawa, kukhumudwa ndiponso kudziimba mlandu. Zikatero mudzakhala ndi mtendere mumtima n’kumatumikira Yehova limodzi ndi anzanu. Mudzafanana ndi Akhristu amene mtumwi Petulo anawalembera kuti: “Munali ngati nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa m’busa wanu ndi woyang’anira miyoyo yanu.”—1 Petulo 2:25.

Mudzachita bwino kwambiri mukabwerera kwa Yehova. Tikutero chifukwa chakuti mudzakondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Kumbukirani kuti Yehova amatha kukhumudwa kapena kusangalala chifukwa cha zochita zathu. Koma iye satikakamiza kumukonda ndiponso kumutumikira. (Deuteronomo 30:19, 20) Katswiri wina wa Baibulo anati: “Palibe munthu amene angatsegule mtima wa munthu wina. Aliyense amatsegula wake.” Ndiyeno tikamatumikira Yehova chifukwa chomukonda kwambiri zimakhala ngati tasankha kutsegula mtima wathu. Munthu amene wachita zimenezi amakhala atapereka kwa Mulungu mphatso yamtengo wapatali ndipo izi zimamusangalatsa kwambiri. Paja Yehova ndi woyenera kulambiridwa choncho palibe chosangalatsa kuposa kumupatsa zimene ayenera kulandira.—Machitidwe 20:35; Chivumbulutso 4:11.

Abale ndi alongo akulandira mlongo amene wabwerera mumpingo

Mukabwerera kwa Yehova mudzapezanso zosowa zanu zauzimu. (Mateyu 5:3) Anthu ambiri padzikoli sadziwa cholinga cha moyo. Amafunitsitsa kupeza mayankho pa nkhaniyi ndipo izi n’zomveka chifukwa Yehova anatilenga ndi mtima wofuna kudziwa zimenezi. Mtima wathuwo umakhala wosangalala kwambiri ngati tikutumikira Yehova chifukwa chomukonda.—Salimo 63:1-5.

Musakayikire zoti Yehova amafunitsitsa kuti mubwerere. Kabukuka kanakonzedwa pambuyo popemphera ndipo ndi umboni wakuti Yehova akukuitanani. N’kutheka kuti mkulu wina kapena Mkhristu wina ndi amene anakupatsani. Ndiyeno inuyo munaona kuti ndi bwino kukawerenga n’kutsatira malangizo ake. Zonsezi zikungosonyeza kuti Yehova sanakuiwaleni. Zili ngati akukukokani mokoma mtima kuti mubwerere.—Yohane 6:44.

N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova saiwala atumiki ake amene asochera. Mlongo wina dzina lake Donna anatsimikizira mfundo imeneyi. Iye anati: “Ndinayamba kusiya Yehova mwapang’onopang’ono. Koma nthawi zambiri ndinkaganizira lemba la Salimo 139:23, 24 lomwe limati: ‘Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga. Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere, ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa, ndipo munditsogolere m’njira yamuyaya.’ Ndinkadziwa kuti ndiyenera kukhala m’gulu la Yehova osati m’dziko loipali. Ndinali ngati mlendo m’dzikoli. Ndiyeno ndinayamba kuona umboni wakuti Yehova sanandisiye. Chofunika chinali kubwerera kwa iye basi ndipo ndikusangalala kuti ndinabwereradi.”

“Ndinayamba kuona umboni wakuti Yehova sanandisiye.

Tikukhulupirira kuti inunso mupeza “chimwemwe chimene Yehova amapereka.” (Nehemiya 8:10) Mukabwerera simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono.

Zimene Mungafune Kudziwa Kuti Mubwerere kwa Yehova

KODI NDIYAMBIRE PATI?

Mlongo wofooka akuwerenga Baibulo

Munthu amene akuchira matenda enaake amafunika kuyamba kuchita zinthu pang’ono ndi pang’ono. Inunso kuti zikuyendereni bwino muyenera kuyamba kuchita zinthu pang’onopang’ono. Musakhale ndi mtima wofuna kuchita zonse nthawi imodzi. Mwina mungayambe ndi kuwerenga Baibulo kwa maminitsi ochepa tsiku lililonse. Apo ayi, mukhoza kumawerenga mabuku athu kapena kuona zinthu pa webusaiti ya jw.org. Mungachitenso bwino kuyamba msanga kupezeka pa misonkhano. Koma chofunika kwambiri ndi kupempha Yehova kuti akuthandizeni. Paja Baibulo limanena kuti ‘tizimutulira nkhawa zathu chifukwa amatidera nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

Mlongo wina dzina lake Eeva anati: “Nditasiya kutumikira Yehova ndinkachita manyazi kupemphera. Koma tsiku lina nditalimba mtima n’kupemphera, mkulu wina mumpingo anabwera kudzandiona. Anandithandiza kuzindikira kuti Yehova sananditaye. Ndiyeno anandilimbikitsa kuti ndiyambe kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Izi zinandipatsa mphamvu kuti ndiyambenso kupezeka pa misonkhano. Kenako ndinayamba kulalikira. Ndikuyamikira kuti Yehova sanandisiye.”

KODI ANTHU MUMPINGO ADZANDILANDIRA BWANJI?

Dziwani kuti anthu mumpingo adzakulandirani mwachikondi. Iwo sadzakukayikirani kapena kukuweruzani koma adzasonyeza kuti amakukondani kwambiri. Adzachita zonse zimene angathe kuti akulimbikitseni.—Aheberi 10:24, 25.

M’bale wina dzina lake Javier anati: “Ndinkachita manyazi kuti ndipite ku Nyumba ya Ufumu. Sindinkadziwa ngati abale ndi alongo angandilandire bwino. Koma tsiku lina nditapita, mlongo wina wachikulire yemwe ndinkasonkhana naye zaka 30 zapitazo anati: ‘Ndakulandira mwana wanga.’ Mawuwo anandikhudza kwambiri. Ndinaona kuti ndafikadi kwathu.”

M’bale wina dzina lake Marco anati: “Ndinapita ku Nyumba ya Ufumu n’kukhala pampando womaliza kuti anthu asandione. Koma anthu ambiri anandizindikira chifukwa ndinkabwera ndili mwana. Iwo anandilandira n’kundihaga moti ndinamva bwino kwambiri mumtima. Ndinaona kuti ndafika kwathu.”

KODI AKULU ADZANDITHANDIZA BWANJI?

Nawonso akulu adzakulandirani bwino. Adzakuyamikirani kwambiri chifukwa choyesetsa kuti mukhalenso ndi ‘chikondi chimene munali nacho poyamba.’ (Chivumbulutso 2:4) Iwo adzakuthandizani mwachifundo kuti mukonze zonse zimene munalakwitsa. (Agalatiya 6:1; Miyambo 28:13) Akuluwo angakonze zoti munthu wina aziphunzira nanu Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku monga Yandikirani kwa Yehova kapena Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’? Dziwani kuti akulu adzakulimbikitsani ndiponso kukuthandizani bwinobwino.—Yesaya 32:1, 2.

M’bale wina dzina lake Victor anati: “Nditasiya kutumikira Yehova kwa zaka 8, akulu ankandiyenderabe. Tsiku lina, mkulu wina anandionetsa zithunzi zimene anatijambula nthawi inayake. Zithunzizo zinandikumbutsa zinthu zosangalatsa zambirimbiri moti ndinayamba kulakalaka nthawi imene ndinkatumikira Yehova. Akuluwo anandithandiza mwachikondi kuti ndikhalenso pa ubwenzi ndi Yehova.”

“Mulungu Adzakulimbitsa”

Alongo awiri akugwiritsa ntchito buku la nyimbo limodzi

M’buku lathu la nyimbo lakuti Imbirani Yehova Mosangalala muli nyimbo zambiri zimene zingakulimbikitseni pamene mukuyambiranso kutumikira Yehova. Taonani mawu a m’nyimbo nambala 38. Nyimboyi yachokera pa 1 Petulo 5:10 ndipo mutu wake ndi wakuti “Mulungu Adzakupatsani Mphamvu.”

  1. Panali chifukwa chimene Mulungu

    Anakupatsira choonadi

    Anaona mtima wofuna kuchita

    Zabwino zomusangalatsadi.

    Unalonjeza kum’tumikira

    Ndipo Iye anakuthandiza.

  2. Mulungu anapereka mwana wake

    Amafunadi zikuyendere.

    Ngati mwana wakeyo sanatimane

    Kukulimbitsa sangalephere.

    Chikondi chako sangaiwale

    Sangasiye konse anthu ake.

    (KOLASI)

    Ndi magazi a Yesu anakuwombola

    Adzakulimbitsa adzakuteteza.

    Adzakutsogolera ndi mzimu woyera

    Adzakulimbitsa adzakuteteza.

Imbirani Yehova

Kuti mumvetsere nyimboyi komanso nyimbo zina za Ufumu, chitani sikani kachidindo aka kapena pitani pa www.pr418.com. Onani pa mutu wakuti MABUKU > NYIMBO.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena