Miyezo Ikasintha Imakayikitsa
M’nthaŵi ya Mfumu Henry woyamba wa ku England (1100-1135) yadi imodzi ankati inali yaitali kuchokera pamphuno ya Mfumuyo mpaka kumapeto kwa chala chachitali cha dzanja lake akaliwongola chakutsogolo. Kodi timitengo toyezera totalika yadi imodzi tam’nthaŵi ya Mfumu Henry tinali tolondola motani? Munthu yekhayo wokacheza ndi mfumuyo ndiye anali kudziŵa bwino utali weniweni wa muyezowo.
MIYEZO masiku ano n’njolondola kwambiri ndipo ili ndi mayina ake. Mwakuti, mita imatanthauza mtunda womwe kuwala kumayenda m’mulengalenga pa sekondi imodzi, n’kugaŵa ndi 299,792,458. Kunena zoona, kuwala kumeneku sikusintha ndipo kumatulutsidwa ndi makina apadera. Ngati ali ndi chipangizo chomwe ndi muyezo wosasintha, ndiye kuti anthu kwina kulikonse atha kuona ngati kutalika kwa mlingo wawo kukufanana ndi wa wina aliyense.
Miyezo yoyesera zinthu ikasintha, ngakhale pang’ono chabe, zingachititse zinthu kukhala zosatsimikizika. Pa chifukwa ichi, anthu akuyesetsa kuteteza miyezo imeneyi. Mwachitsanzo, ku Britain mwala wolemera kilogalamu imodzi womwe anaupanga posakaniza pulatinamu ndi iridiyamu ndiwo muyezo woyezera zinthu. Mwala umenewu amausunga kumalo ofufuzirako zinthu a National Physical Laboratory. Chifukwa cha utsi woipa wa magalimoto ndiponso ndege zomwe zimadutsa kumalo ameneŵa, mwalawo ukuwonjezera kulemera kwake tsiku ndi tsiku. Komanso mwala umenewu ndi wofanana ndi muyezo wapadziko lonse umene amausunga m’mabotolo agalasi atatu m’chipinda chapansi ku International Bureau of Weights and Measures ku Sèvres, France. Komabe, muyezo wapadziko lonse umenewu kulemera kwake kukusintha chifukwa cha kuwonongeka kovuta kukuzindikira. Ndiyetu n’chifukwa chake mpaka lero akatswiri a za miyezo sanapezebe muyezo wokhazikika.
Ngakhale kuti kusintha kochepa chabe kwa miyezo kumaoneka kuti sikudandaulitsa anthu ambiri, kusintha kotheratu kwa miyezo kungayambitse chisokonezo. Ku Britain, kusintha miyezo yamakedzana yoyezera zinthu (pounds ndi ounces) n’kuyamba miyezo yamakono (makilogalamu ndi magalamu) kunayambitsa kusakhulupirirana kwakukulu, ndipo zinalidi zomveka. Eni masitolo ena opanda khalidwe anatengerapo mwayi wobera makasitomala awo chifukwa ambiri sanali kudziŵa bwino za kayezedwe katsopanoka.
Miyezo Yabanja Ndiponso Yamakhalidwe
Bwanji nanga za kusintha kwa miyezo ya banja ndiponso makhalidwe? Kusintha koteroko kumadzetsa zotsatira zowononga kwambiri. Malipoti aposachedwapa a kutha kwa mabanja, kugonana kwachisawawa, kufala kwa khalidwe lozunza ana ndi uchidyamakanda, zikudabwitsa anthu ambiri ndipo zikutsimikiza kuti tikukhaladi m’nthaŵi yomwe miyezo ikucheperachepera mphamvu. Mabanja a kholo limodzi, ana oleredwa ndi “makolo” okwatirana amuna kapena akazi okhaokha, ndiponso kugona ana amene boma likuwalera ndi zina mwa zomwe zikuchitika chifukwa chakuti anthu akukana miyezo yovomerezeka. Monga momwe Baibulo linaneneratu zaka masauzande aŵiri zapitazo, anthu ambiri akukhala “odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, . . . osakonda abwino, . . . okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”—2 Timoteo 3:1-4.
Kuloŵa pansi kwa miyezo ya makhalidwe abwino kumayendera limodzi ndi kuchita zinthu mosadalirika. Posachedwapa, zinali zoonekeratu kuti miyezo ya zachipatala sinali kutsatiridwa ku Hyde, tauni yomwe ili kumpoto kwa dziko la England, komwe anthu akumeneko, “amadalira ndiponso kukhulupirira” madokotala awoawo. Koma chikhulupiriro chawocho chinawagwiritsa mwala momvetsa chisoni. Motani? Malipoti a mlandu wokhudza dokotala anavumbula kuti, iye anapha odwala ake achikazi pafupifupi 15. Inde, apolisi anafufuzanso nkhani yokhudza dokotala yemweyu za imfa za anthu oposa 130. Anadabwa kwambiri pamene dokotalayo anamupezadi kuti n’ngolakwa ndi kum’lamula kukakhala m’ndende. Maofesala aŵiri a ndendeyo amene amayi awo ayenera kuti anaphedwa ndi dokotalayo anawapatsa ntchito zina kuti asasamalire mkaidi woopsayo. Mpake kuti lipoti la mlanduwo m’nyuzipepala ya The Daily Telegraph linatchula munthuyo kuti “Dokotala ‘woipitsitsa.’”
Malinga ndi kusinthasintha ndiponso kuloŵa pansi kwa miyezo m’mbali zambiri za moyo, kodi tingakhulupirire ndani popanda kum’kayikira? Kodi tingaipeze kuti miyezo yosasintha yovomerezeka ndi boma lomwe lili ndi mphamvu zotha kuisungabe? Nkhani yotsatirayi ikuyankha mafunso ameneŵa.