Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 June tsamba 7
  • Tizitsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizitsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Yehova
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 June tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizitsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Yehova

Yehova Mulungu anakhazikitsa mfundo za makhalidwe abwino zoti anthu azitsatira. Mwachitsanzo, iye ananena kuti banja ndi mgwirizano wapakati pa mwamuna ndi mkazi basi. (Mat. 19:4-6, 9) Yehova amadana ndi khalidwe lachiwerewere la mtundu uliwonse. (1 Akor. 6:9, 10) Amaperekanso malangizo pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa, zomwe zimasiyanitsa anthu ake ndi ena.​—Deut. 22:5; 1 Tim. 2:9, 10.

Masiku ano anthu ambiri m’dzikoli safuna kutsatira mfundo za Yehova. (Aroma 1:18-32) Iwo amangotsatira maganizo a anthu ena pa nkhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa komanso khalidwe lawo. Ambiri amadzitamandira chifukwa chochita zoipa ndipo amanyoza anthu amene amatsatira mfundo zosiyana ndi zawo.​—1 Pet. 4:3, 4.

Popeza kuti ndife Mboni za Yehova, tiyenera kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino. (Aroma 12:9) Tingachite zimenezi pouza anthu ena zimene Yehova amafuna. Komanso ifeyo tisasiye kutsatira mfundozo. Mwachitsanzo, tikamasankha masitayilo a zovala komanso kudzikongoletsa, tingadzifunse kuti: ‘Kodi zimene ndasankhazi zikugwirizana ndi mfundo za Yehova kapena za dzikoli? Kodi mmene ndimavalira komanso mmene ndimadzikongoletsera zimasonyeza kuti ndine Mkhristu?’ Tikamasankha mafilimu kapena mapulogalamu a pa TV, tingadzifunse kuti: ‘Kodi Yehova angasangalale ndi pulogalamuyi? Kodi ikulimbikitsa mfundo za ndani? Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda sizingawononge makhalidwe anga? (Sal. 101:3) Kodi sizingakhumudwitse anthu a m’banja langa kapena anthu ena?’​—1 Akor. 10:31-33.

Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kuti tizitsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino? Posachedwapa Yesu Khristu adzawononga anthu oipa komanso adzachotsa zoipa zonse. (Ezek. 9:4-7) Amene adzapulumuke ndi okhawo omwe amachita zimene Mulungu amafuna. (1 Yoh. 2:15-17) Choncho tiyeni tipitirize kutsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino kuti anthu akaona khalidwe lathu labwino azilemekeza Mulungu.​—1 Pet. 2:11, 12.

Mayi akusankha zovala

Kodi zimene ndimasankha pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa zimasonyeza kuti ndili ndi khalidwe lotani?

ONERANI VIDIYO YAKUTI KHALANI BWENZI LA YEHOVA​—MWAMUNA MMODZI, MKAZI MMODZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani kutsatira mfundo za Yehova n’kofunika kwambiri?

  • N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuyamba kuphunzitsa ana awo adakali aang’ono mfundo za Yehova za makhalidwe abwino?

  • Kodi ana ndi akuluakulu omwe, angathandize bwanji anthu kuti apindule ndi ubwino wa Mulungu?

KODI MUNGAYANKHE BWANJI WINA ATANENA KUTI . . .

  • “Kodi inuyo mumaiona bwanji nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha?”

  • “Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha zimalimbikitsa tsankho.”

  • “Anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha sangasinthe chifukwa ndi mmene anabadwira.”

(yp1 mutu 23; yp2 mutu 28)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena