Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukhala Okoma Mtima
1 Pokumbukira za tsiku loyambirira limene anakumana ndi wa Mboni za Yehova, mayi wina amene ankadana ndi Mboni anafotokoza kuti: “Sindikukumbukira bwino zimene tinakambirana, koma chimene ndikukumbukira kwambiri n’chakuti mzimayiyo anandikomera mtima kwambiri, analinso wochezeka ndi wodzichepetsa. Ndinam’konda kwambiri chifukwa cha makhalidwe amenewa.” Ndemanga ngati zimenezi zimagogomezera kufunika kosonyeza anthu ena chidwi pamene tikulalikira.—Afil. 2:4.
2 Chikondi Chili Chokoma Mtima: Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakonda ena ndiyo yokhala okoma mtima. (1 Akor. 13:4) Munthu wokoma mtima amafunira ena zinthu zabwino, ndipo amayesetsa kupeza njira zowathandizira. N’zoona kuti timasonyeza kukoma mtima pamene tikulalikira. Koma sikulalikira kokha kumene kumasonyeza kuti timawakondadi anthu. Timasonyezanso chidwi chathu kwa anthu mwa kukhala aubwenzi, aulemu, ndi omvetsera kwambiri, komanso mwa zimene timanena ndi mmene timazinenera zinthuzo. Timasonyezanso zimenezi mwa njira imene timawayang’anira anthu pamene tikulankhula nawo.—Mat. 8:2, 3.
3 Kukonda ena ndi kuwadera nkhawa kumatilimbikitsa kuthandiza ena osati mwa mawu chabe koma m’zochita zathu. Mpainiya wina ali mu ulaliki wa khomo ndi khomo, sanalandiridwe bwino ndi mayi wina wachikulire atadziwa kuti mbaleyo anali wa Mboni. Mayiyo anafotokoza kuti pamene mbaleyo amagogoda, n’kuti iye ali pamwamba pa makwerero ake, akuika babu la magetsi m’khitchini. Mbaleyo anayankha kuti: “Si bwino kuti muziika babu muli nokhanokha.” Atatero mayiyo anamulowetsa m’nyumba mbaleyo. Ndipo mbaleyo anaika babulo. Atamaliza anatsazika ndi kupitiriza ulendo wake. Patangopita nthawi pang’ono, mwana wamwamuna wa mayiyo anabwera kudzaona mayi ake, ndipo anamufotokozera zimene mbaleyo anachita. Izi zinam’sangalatsa mnyamatayo ndipo anayesetsa kumufunafuna mbaleyo kuti am’thokoze. Zotsatira zake, anakambirana bwino kwambiri ndipo mnyamatayo analola kuti aziphunzira Baibulo.
4 Mwa kukhala okoma mtima, timasonyeza chikondi chimene Yehova ali nacho pa anthu ndipo timakometsera uthenga wa Ufumu. Chotero, tiyeni nthawi zonse ‘tidzitsimikizire ife tokha monga atumiki a Mulungu . . . m’kukoma mtima.’—2 Akor. 6:4, 6.