Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/05 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira October 10
  • Mlungu Woyambira October 17
  • Mlungu Woyambira October 24
  • Mlungu Woyambira October 31
  • Mlungu Woyambira November 7
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 10/05 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira October 10

Nyimbo Na. 17

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kusonyeza chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya October 15 ndi Galamukani! ya November 8. Pamapeto pa chitsanzo chilichonse, fotokozaninso mfundo zofunikira kwambiri m’chitsanzocho. Sonyezaninso nkhani zina m’magaziniwo zimene anthu m’gawo lanu angasangalale nazo. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: Kodi Mumakonda Kuwerenga? Nkhani yokambirana ndi omvera kuchokera mu buku la Sukulu ya Utumiki, masamba 21 mpaka 26 malinga ndi zigawo zimene zili m’munsimu. Kodi pa ndandanda yanu yowerenga pali chiyani? (tsa. 21, bokosi) Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kumawerenga mabuku amene timalandira? (tsa. 23, ndime 2) Kodi n’chiyani chomwe chili chofunika kuti tikhale ndi pulogalamu yabwino yowerenga? (tsa. 26, ndime 2 ndi 3) Kodi nthawi yowerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mumaipeza bwanji? Kodi zimenezi zakupindulirani motani?

Mph. 20: “Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zimene zimachititsa kuti kukhale kovuta kuti munthu alimbe mtima ndi kulalikira. N’chiyani chomwe chawathandiza kulimba mtima?

Nyimbo Na. 78 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 17

Nyimbo Na. 36

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito gawo 3 la mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2005, bwerezani mfundo imodzi kapena ziwiri zosonyeza momwe mungagwiritsire ntchito bwino Malemba pamene mukuchititsa maphunziro a Baibulo.

Mph. 20: Zoona Zake za Ufiti. Nkhani yokambirana ndi omvera. Ikambidwe ndi mkulu kuchokera mu bulosha la Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? masamba 16 mpaka 18, ndime 10 mpaka 17. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwa. Pemphani omvera afotokoze Malemba amene agwidwa mawu m’ndimezo.

Mph. 15: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukhala Okoma Mtima.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze momwe tingakomere ena mtima pamene tili mu utumiki wa kumunda. Mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa m’tsogolomu, tidzakambirana njira zinanso zomwe tingasonyezere chidwi anthu amene timawalalikira.

Nyimbo Na. 2 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 24

Nyimbo Na. 68

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa masitetimenti. Pogwiritsira ntchito mfundo za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005 kapena njira ina imene ingakhale yoyenerera gawo lanu, chitani chitsanzo chosonyeza momwe mungagawire mabuku ogawira m’mwezi wa November.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsa. 8, ndime 5.

Mph. 20: Kumsonkhano Wachigawo Wakuti “Kumvera Mulungu”—Kodi Tinaphunzirako Chiyani? Kubwereza mfundo zazikulu za kumsonkhano zimene ofalitsa aona kuti zingawathandize mu utumiki wa kumunda, m’banja ndi kumpingo wa anthu a Yehova. Funsani ofalitsa awiri kapena atatu kuti afotokoze mmene akupindulira ndi zimene anaphunzira kumsonkhano.

Mph. 15: Kutsatira Miyezo ya Yehova mwa Kavalidwe ndi Kudzikongoletsa Kwathu. Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvera. Ikambidwe ndi mkulu kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2002, masamba 17 mpaka 19. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene kaonekedwe kathu kabwino kangaperekere mwayi wolalikira.

Nyimbo Na. 153 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 31

Nyimbo Na. 209

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa October. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo cha momwe tingagawire Nsanja ya Olonda ya November 1 ndi Galamukani! ya November 8. Pachitsanzo chimodzi, sonyezani mmene mungakonzekere ulendo wobwereza polozera mwininyumba kabokosi kakuti “Zimene Zili M’magazini Yotsatira.”—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1998, tsa. 8, ndime 7 ndi 8. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: Khalani ndi Anthu Oti Muzikawapatsa Magazini Kuti Chidwi Chawo Chikule. Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvera yochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2005, tsamba 8. Kodi tingachite chiyani kuti tikhale ndi anthu oti tizikawagawira magazini? (ndime 1) Kodi tingakonzekere bwanji kuti tizikambirana ndi anthuwo lemba limodzi lokha pa ulendo uliwonse? (ndime 3) Kodi n’chifukwa chiyani tifunikira kuchita zambiri m’malo mongowerenga lemba lokha? (ndime 4) Kodi mungatani kuti munthu amene mumakamupatsa magazini ayambe phunziro la Baibulo? (ndime 5) Phatikizanipo chitsanzo cha wofalitsa akukambirana ndi munthu amene amakamupatsa magazini ndi kuwerenga naye lemba limodzi.

Mph. 20: Achinyamata Osasunthika Koma Aulemu. Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2002, masamba 23 ndi 24, pamutu wakuti “Kanani Mwaulemu.” Konzani pasadakhale zoti wachinyamata mmodzi kapena awiri adzafotokoze za mavuto amene anakumana nawo kusukulu ndi zimene zinawathandiza kuti athane nawo bwinobwino mavutowo.

Nyimbo Na. 222 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 7

Nyimbo Na. 39

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 20: Ongolerani Kamvedwe Kanu pa Misonkhano. Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2002, tsamba 12-14, ndime 11 mpaka 14. Fotokozani mfundo zomwe zaperekedwa, ndipo pemphani omvera kuti afotokoze zimene zawathandiza kuti apindule kwambiri ndi misonkhano ya mpingo.

Mph. 20: “Khalani ndi Luso Lothandiza Ena Kuona Mfundo Yofunika.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani ofalitsa angapo kuti afotokoze zimene zawathandiza kukambirana ndi anthu osiyanasiyana m’gawo la mpingo wanu.

Nyimbo Na. 50 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena