Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 10/14 tsamba 4-6
  • Kodi Mungatani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino?
  • Galamukani!—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wabwino Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Munthu Zikumuyenderadi?
    Galamukani!—2014
  • Chipambano—Pa Mtengo Wonse?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Zimene Mungachite Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 10/14 tsamba 4-6
Charlotte ndi Timothy

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMAONERA CHIYANI KUTI MUNTHU ZIKUMUYENDERA?

Kodi Mungatani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino?

Baibulo limatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino. Siliphunzitsa kuti anthu ochepa okha amwayi ndi amene zinthu zimawayendera bwino. Silinenanso kuti munthu zinthu zikhoza kuyamba kumuyendera bwino ngati atayesetsa kupeza zinthu zonse zimene amalakalaka. Anthu ambiri amakhala ndi maganizo amenewa chifukwa choti ali mwana anaphunzitsidwa zimenezi. Koma pambuyo pake amazindikira kuti zimenezi si zoona ndipo amagwiritsidwa fuwa lamoto.

Koma zoona ndi zoti munthu aliyense zinthu zikhoza kumamuyendera bwino, kungoti pamafunika khama. Taonani mfundo zotsatirazi.

  • Ndalama zachitsulo

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

    “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.”—Mlaliki 5:10.

    ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Kukhala ndi katundu wambiri sikuchititsa kuti munthu akhale wosangalala. Anthu amene ali ndi zinthu zambiri ndi amenenso amakhala osasangalala. Wolemba mabuku wina, dzina lake Jean M. Twenge, analemba m’buku lake lina kuti: “Anthu amene cholinga chawo chachikulu n’kufuna kulemera, nthawi zambiri amakhala ndi nkhawa ndipo amadwala matenda amaganizo kuposa anthu amene amaona kuti chofunika kwambiri n’kukhala bwino ndi ena.” Ananenanso kuti: “Kafukufuku amasonyeza kuti kukhala ndi ndalama zambiri sikuchititsa munthu kukhala wosangalala. Ngakhale munthu amene ali ndi zinthu zochepa pa moyo wake, akhoza kukhala wosangalala.”—Generation Me.

    ZIMENE MUNGACHITE. Musamangokhalira kufunafuna ndalama kapena katundu wambiri. M’malomwake, ganizirani zinthu zimene zingakuthandizeni kukhala wosangalala ndipo muzichita zimenezo. Yesu anati: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.

  • Munthu wonyada

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

    “Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.”—Miyambo 16:18.

    ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Kunyada komanso kuchita zinthu modzionetsera sikungakuthandizeni kukhala wosangalala. Buku lina linanena kuti makampani omwe amayenda bwino, mabwana ake “amakhala odzichepetsa komanso sachita zinthu modzionetsera. Pomwe makampani omwe mabwana ake ndi odzikuza komanso onyada, sayenda bwino mwinanso amatha kumene.” (Good to Great) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Munthu akakhala wodzikuza kapena wonyada, zinthu sizimuyendera bwino.

    ZIMENE MUNGACHITE. M’malo mofuna kutchuka, yesetsani kukhala wodzichepetsa. Baibulo limati: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero, akudzinyenga.” (Agalatiya 6:3) Izi zikusonyeza kuti kutchuka si chizindikiro choti munthu zikumuyendera bwino.

  • Dzanja litagwira hamala

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

    “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa . . . kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.”—Mlaliki 2:24.

    ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Mukakhala ndi chizolowezi chogwira ntchito mwakhama, mumasangalala ndi ntchito yanu. Wolemba mabuku wina, dzina lake Madeline Levine, analemba m’buku lake lina kuti: “Munthu amene zinthu zimamuyendera bwino pa ntchito ndi amene amagwira bwino ntchito yakeyo. Ndipo kuti munthu azigwira bwino ntchito yake, amafunika kukhala wakhama komanso wolimbikira.” (Teach Your Children Well) Munthu wotereyu amathanso kupirira akakumana ndi mavuto pa ntchito yakeyo.

    ZIMENE MUNGACHITE. Yesetsani kuidziwa bwino ntchito yanu ndipo mukakumana ndi mavuto musamafooke. Ngati muli ndi ana, aphunzitseni kudziwa zimene angachite akakumana ndi mavuto. Muzichita zimenezi mogwirizana ndi msinkhu wa anawo. Akakhala ndi vuto, musathamangire kuwathandiza. Asiyeni kuti ayese kuthana nalo okha. Ana akadziwa mmene angathetsere mavuto, amakhala osangalala komanso amaphunzira kuchita zinthu zomwe zingadzawathandize m’tsogolo.

  • Galu

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

    “Galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.”—Mlaliki 9:4.

    ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Ngati mumagwira ntchito yolembedwa, muziiona kuti ndi yofunika pa moyo wanu koma sikuti maganizo anu onse azingokhala pa ntchitoyo. N’kutheka kuti ku ntchito kwanu muli ndi udindo waukulu komanso amakudalirani. Koma mwina mumadzipanikiza kwambiri ndi ntchitoyo ndipo izi zikuchititsa kuti muzidwala matenda osiyanasiyana komanso kuti musamapeze nthawi yochita zinthu zina ndi banja lanu. Kodi pamenepa munganene kuti zinthu zikukuyenderanidi bwino? Munthu amafunika kuti azikhala ndi nthawi yogwira ntchito, yosamalira thanzi lake komanso yochita zinthu zina ndi banja lake. Munthu yemwe akukwanitsa kuchita zimenezi ndi amene tingati zinthu zikumuyenderadi bwino.

    ZIMENE MUNGACHITE. Muzisamalira thanzi lanu ndipo muzipuma mokwanira. Palibe chimene munthu angapindule ngati amangokhalira kugwira ntchito n’kumalephera kupeza nthawi yosamalira thanzi lake, yochita zinthu zina ndi banja lake komanso yocheza ndi anzake. Munthu amene amangokhalira kugwira ntchito, angaoneke ngati zinthu zikumuyendera, koma zimenezi si zoona.

  • Baibulo lotsegula

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

    “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.

    ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Kuphunzira Baibulo komanso kutsatira mfundo zake kungakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino. A Mboni za Yehova amaona kuti kupeza nthawi yokwanira yochita zinthu zauzimu kumawathandiza kuchepetsa nkhawa kusiyana ndi kufuna kupeza zinthu zambirimbiri.—Mateyu 6:31-33.

    ZIMENE MUNGACHITE. Phunzirani Baibulo kuti mudziwe mmene lingakuthandizireni kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Kuti mudziwe zambiri, funsani a Mboni za Yehova a kudera lanulo, kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.pr418.com.

“Ndinkadzinamiza Kuti Zinthu Zikundiyendera”

Charlotte ndi Timothy

Timothy ndi mkazi wake, Charlotte, ankakhala m’chinyumba chachikulu. Anali ndi magalimoto apamwamba atatu ndipo chaka chilichonse ankapita kumalo odula kukasangalala. Koma kenako anaganiza zosintha zina ndi zina n’kuyamba kukhala moyo wotsikirapo. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza ndi Timothy kuti adziwe chimene chinawapangitsa kuchita zimenezi.

Munkagwira ntchito yanji poyamba?

Ndinali wowerengetsera ndalama pakampani ina ya zoimbaimba. Charlotte ankagwira ntchito yopanga anthu masaji ndipo kenako anayamba kugwira ntchito kubanki. Patapita nthawi, tinatsegula malo 4 ometera. Zinkaoneka kuti chilichonse chimene tinkachita chinkatiyendera bwino. Ndipotu, nthawi zambiri sindinkagwira ntchito chifukwa ndinali ndi antchito ambiri. Koma m’kupita kwa nthawi, tinaganiza zochepetsa bizinezi yathu. Choncho tinagulitsa zinthu zina zomwe tinali nazo.

N’chifukwa chiyani munachita zimenezi?

Ngakhale kuti tinali ndi zinthu zambiri, nthawi zina tinkaonabe kuti zinthu sizikutiyendera bwino. Mwachitsanzo, tinkasangalala kwambiri tikagula chinthu koma chisangalalo chimenechi sichinkakhalitsa. Pakangopita nthawi pang’ono tinkaona kuti chinthucho sichikutithandiza kukhala osangalala.

Ndiye munatani kuti zinthu ziyambedi kukuyenderani bwino?

Popeza ndife a Mboni za Yehova nthawi zambiri timakhala tikuuza anthu uthenga wa m’Baibulo. Ngakhale kuti poyamba tinkatha maola 70 pa mwezi tikuphunzitsa ena Baibulo, sikuti maganizo athu onse anali pa zimenezi. Choncho tinagulitsa bizinezi yathu, ndipo tinasamukira kudera lina komwe kuli a Mboni ochepa n’cholinga choti tikathandize pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Panopa tikutumikira kulikulu la Mboni za Yehova la m’dziko la United States. Popeza umenewu ndi utumiki, sitilipidwa kapena kupatsidwa ulemu wapadera. Tili ndi zonse zofunika pa moyo, koma sikuti maganizo athu onse amakhala pa zinthu zomwe tili nazozi.

Kodi panopa mumaona kuti zinthu zikukuyenderani bwino kuposa poyamba?

Kwambiri. Ndikuona kuti poyamba ndinkangodzinamiza kuti zinthu zikundiyendera. Koma panopa ndine munthu wosangalala kwambiri ndipo zimene ndikuchitazi zidzandithandiza mpaka kalekale. Ntchito imene ndikugwira ikuthandiza anthu padziko lonse kudziwa uthenga wa m’Baibulo ndipo uthengawu umasintha moyo wawo.a

a A Mboni za Yehova salipidwa pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imene amagwira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena