Mutu 15
“Sindingathe Kukhala Chete”
1. N’chifukwa chiyani Yeremiya ndi aneneri ena a Yehova sanakhale chete?
MNENERI wa Mulungu ankauza anthu m’misewu ndi m’mabwalo a ku Yerusalemu uthenga wakuti: “Tamverani mawu a Yehova.” Iye ankalengeza uthengawu mosatopa, ndipo anayamba kugwira ntchitoyi mu 647 B.C.E. Patapita zaka 40, iye anabwerezanso kulengeza uthengawu, ndipo pa nthawiyi mzindawo unali utawonongedwa. (Yer. 2:4; 42:15) Mulungu Wamphamvuyonse ankatumiza aneneri pofuna kuonetsetsa kuti Ayuda akumva malangizo ake ndiponso kuti alape. Monga taonera kale m’bukuli, Yeremiya anali mneneri wodziwika bwino kwambiri poyerekezera ndi aneneri anzake. Pamene Mulungu ankauza Yeremiya kuti akhale mneneri wake, anamuuza kuti: “Upite kukawauza zonse zimene ndikulamule kuti ukawauze. Usagwidwe ndi mantha.” (Yer. 1:17) Utumiki umene Yeremiya anapatsidwa unali wovuta kwambiri. Iye anakumana ndi mavuto amene anamuchititsa kumva ululu m’thupi komanso m’maganizo, komabe anayesetsa kukwaniritsa utumiki wake. Choncho iye anati: “Mtima wanga ukuvutika. Sindingathe kukhala chete.”—Yer. 4:19.
2, 3. (a) Kodi ophunzira a Yesu anatsanzira bwanji Yeremiya? (b) N’chifukwa chiyani muyenera kutsatira chitsanzo cha Yeremiya?
2 Mmene Yeremiya anagwirira ntchito yake yauneneri, zinapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa atumiki a Yehova am’tsogolo. (Yak. 5:10) Patangopita nthawi yochepa kuchokera pa Pentekosite mu 33 C.E., akuluakulu a Ayuda anamanga mtumwi Petulo ndi mtumwi Yohane n’kuwauza kuti asiye kulalikira. Inuyo muyenera kuti munawerengapo zimene iwo anayankha. Iwo anati: “Sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:19, 20) Atsogoleriwo anaopseza Petulo ndi Yohane kuti adzawakhaulitsa kwambiri akapanda kusiya kulalikira ndipo atatero, anawamasula. Komabe mukudziwa zimene zinachitika pambuyo pake. Amuna okhulupirikawo anachitadi zimene ananena ndipo sanasiye kulalikira.
3 Kodi mukutha kuona kuti mawu a Petulo ndi Yohane olembedwa pa Machitidwe 4:20 akusonyeza kuti amuna amenewa anali olimba mtima mofanana ndi Yeremiya? Inuyo ndinunso mtumiki wa Yehova Mulungu ndipo mukutumikira m’masiku otsiriza komanso ovuta ano. Choncho kodi mudzanenanso kuti ‘Sindingathe kukhala chete,’ posonyeza kuti ndinu wotsimikiza mtima ngati mmene analili Yeremiya? Tiyeni tione zimene tingachite kuti tikhalebe olimba mtima ngati Yeremiya n’cholinga choti tipitirizebe kulalikira uthenga wabwino, ngakhale kuti zinthu zikuipiraipira m’dzikoli.
PITIRIZANI NGAKHALE ANTHU ASAMASONYEZE CHIDWI
4. Kodi kale ku Yerusalemu anthu ambiri anali ndi mtima wotani?
4 Kodi simukukhulupirira kuti zimene Mulungu walonjeza zoti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo muno mu ulamuliro wa Mwana wake, ndi uthenga wabwino kwambiri umene anthu akufunika kuumva? Komabe, anthu ambiri akamva za uthengawu masiku ano amayankha ngati mmene Ayuda ena anachitira atamva uthenga wa Yeremiya. Iwo anati: “Ife sitimvera mawu amene watiuza m’dzina la Yehova.” (Yer. 29:19; 44:16) Yeremiya ankauzidwa mawu amenewa kawirikawiri. N’chimodzimodzinso atumiki a Yehova masiku ano, chifukwa anthu ambiri amayankha kuti, “Sindikufuna kumva zimenezo.” Atumiki ena a Mulungu akhoza kufooka ngati akamalengeza uthenga wa Ufumu, nthawi zambiri amakumana ndi anthu opanda chidwi. N’kutheka kuti anthu ambiri m’gawo lanu sachita chidwi ndi uthenga wanu ndipo mwina zimenezi zayamba kufooketsa ena mumpingo mwanu, kapenanso zakufooketsani inuyo. Ngati zili choncho, kodi mungatani?
5. (a) Kodi Yeremiya anamvetsa mfundo iti ngakhale kuti anthu omwe ankawalalikira analibe chidwi ndi uthenga wake? (b) N’chifukwa chiyani anthu amene akukana kumva uthenga wabwino moyo wawo uli pangozi?
5 Taganizirani mtima umene Yeremiya anali nawo ataona kuti Ayuda ambiri sankafuna kumva uthenga wake. Chakumayambiriro kwa utumiki wake, Yehova anamuuziratu za chiweruzo chimene anali atatsala pang’ono kupereka kwa anthuwo. (Werengani Yeremiya 4:23-26.) Zimenezi zinathandiza mneneriyu kuona kuti anthu ambirimbiri moyo wawo unali pangozi, ndipo ankafunika kumva uthenga umene iye ankalengeza, n’kusintha. N’chimodzimodzinso ndi anthu masiku ano, kuphatikizapo a m’gawo lanu. Ponena za tsiku la Mulungu lopereka chiweruzo, lomwe iye adzaweruze dziko loipali, Yesu anati tsikulo “lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi. Chotero khalani maso ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) Mukaona mawu amene Yesu ananenawa, mungathe kuona kuti anthu onse amene amakana uthenga wabwino moyo wawo uli pangozi.
6. N’chifukwa chiyani muyenera kupitiriza kulalikira, ngakhale kwa anthu amene sachita chidwi kwenikweni ndi uthenga wanu?
6 Komabe, anthu amene amayamba kuchita chidwi ndi mawu a Yehova amene timawalalikira n’kusintha moyo wawo, adzalandira madalitso ochuluka. Mulungu akupereka njira yotithandiza kuti tidzapulumuke n’kulowa m’dziko latsopano. Mwanjira ina, zimenezi zikufanana ndi utumiki wa Yeremiya chifukwa ukanathandiza Ayuda kuti apulumuke. (Werengani Yeremiya 26:2, 3.) Pofuna kuwathandiza, Yeremiya anathera zaka zambirimbiri akulimbikitsa anthu kuti ‘amvere ndi kubwerera,’ kapena kuti ayambe kutsatira mawu a Mulungu woona. Sitikudziwa kuti ndi anthu angati amene analapa n’kusintha moyo wawo chifukwa cha uthenga umene mneneriyu ankalengeza. Komabe ena analapa, ndipo masiku anonso anthu ambiri achita chimodzimodzi. Pamene tikupitiriza kulalikira uthenga wabwino, kawirikawiri timamva nkhani zokhudza mmene anthu ena, omwe poyamba analibe chidwi, anasinthira. (Onani bokosi lakuti “Anthu Opanda Chidwi Angasinthe,” patsamba 184.) Kodi chimenechi si chifukwa chinanso chotithandiza kuti tizichita mwakhama utumiki wathu wolalikira uthenga wabwino, podziwa kuti ntchito imeneyi ndi yopulumutsa miyoyo?
N’chifukwa chiyani mwatsimikiza kuti mupitiriza kulalikira uthenga wabwino ngakhale muzikumana ndi anthu opanda chidwi?
TIKHOZA KUPAMBANA NGAKHALE ANTHU AZITITSUTSA
7. Kodi adani a Yeremiya anachita zotani pofuna kusokoneza ntchito ya mneneriyu?
7 Ena mwa mavuto aakulu amene Yeremiya ankakumana nawo nthawi zonse mu utumiki wake ndi oti anthu ankamutsutsa komanso ankafuna kusokoneza utumiki wakewo. Aneneri onyenga ankamutsutsa pamaso pa anthu. (Yer. 14:13-16) Yeremiya akamayenda m’misewu ya mu Yerusalemu, anthu ankamukuwiza n’kumamunenera mawu achipongwe. (Yer. 15:10) Adani ake ena anapeza njira zina zomunyozera n’cholinga choti anthu asamam’khulupirire. (Yer. 18:18) Ndipo ena anayamba kuuza anthu zinthu zoipa zokhudza Yeremiya, n’cholinga choti anthu oona mtima asakhulupirire choonadi chochokera kwa Mulungu chimene mneneriyu ankalalikira. (Maliro 3:61, 62) Kodi Yeremiya anagwa ulesi n’kusiya kulalikira? Ayi, iye anapitirizabe. Kodi n’chiyani chinamuthandiza?
8. Kodi Yeremiya anachita chiyani adani ake atayamba kumutsutsa mowirikiza kwambiri?
8 Chida chachikulu chimene Yeremiya ankagwiritsa ntchito polimbana ndi adaniwo chinali chikhulupiriro chake mwa Yehova. Kumayambiriro kwa utumiki wa Yeremiya, Mulungu anamulonjeza kuti adzamuthandiza ndi kumuteteza. (Werengani Yeremiya 1:18, 19.) Yeremiya anakhulupirira kwambiri lonjezo limeneli, ndipo Yehova anachitadi zimene anamulonjezazo. Ndipotu kulimba mtima komanso kupirira kwa Yeremiya kunawonjezereka pamene anthu otsutsa anayamba kumuzunza komanso kumutsutsa mowirikiza kwambiri. Tiyeni tione mmene kulimba mtima komanso kupirira kunam’thandizira.
9, 10. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachitikira Yeremiya zimene zingakuthandizeni kukhala olimba mtima?
9 Nthawi ina anthu ampatuko, monga ansembe komanso aneneri, anagwira Yeremiya n’kupita naye kwa akalonga a ku Yuda pofuna kuti akamuweruze kuti aphedwe. Kodi Yeremiya anachita mantha kwambiri ndi zimenezo n’kusiya kugwira ntchito yake? Ayi. Ndipo zimene ananena poyankha mlanduwo, zinasonyezeratu kuti anthu ampatukowo ankamunamizira, moti akalongawo anaweruza kuti Yeremiya sakuyenera chilango cha imfa.—Werengani Yeremiya 26:11-16; Luka 21:12-15.
10 Mwina mukukumbukira kuti Pasuri, amene anali mkulu wa pakachisi, atamva uthenga wamphamvu umene mneneriyu ankamuuza, anamugwira n’kumuika m’matangadza. N’kutheka kuti Pasuri ankaganiza kuti Yeremiya akakhala m’matangadzamo akhaula ndipo asiya kulalikira. Choncho tsiku lotsatira Pasuri anamasula mneneriyu. Koma Yeremiya, amene ayenera kuti anali akumva ululu kwambiri chifukwa choikidwa m’matangadzamo, anauza Pasuri pamasom’pamaso chilango chimene Yehova adzam’patse. Apa n’zoonekeratu kuti Yeremiya sanasiye kulalikira ngakhale pamene ankazunzidwa koopsa. (Yer. 20:1-6) N’chifukwa chiyani sanasiye? Yeremiya akutiuza yekha kuti: “Yehova anali nane ngati msilikali wamphamvu ndi woopsa. N’chifukwa chake anthu amene akundizunza adzakhumudwa ndipo sadzapambana.” (Yer. 20:11) Yeremiya sanachite mantha ngakhale pamene ankatsutsidwa ndi anthu oopsa. Iye anali ndi zifukwa zamphamvu zodalira kwambiri Yehova, ndipo inunso mungakhale ndi zifukwa zoterozo.
11, 12. (a) Kodi Yeremiya anachita bwanji zinthu mwanzeru pamene Hananiya ankamutsutsa? (b) Kodi mungapindule bwanji ngati mutakhala ‘ougwira mtima pokumana ndi zoipa’?
11 Tiyenera kukumbukira kuti Yeremiya sankachita zinthu mongotengeka kapena monyanyira. Anthu akamamutsutsa, iye ankachita zinthu mwanzeru ndipo ankadziwa nthawi yoyenera kuchoka pamaso pa otsutsawo. Mwachitsanzo, ganizirani zimene Yeremiya anachita atakumana ndi Hananiya. Mneneri wonyengayu atatsutsa mawu aulosi a Yehova pamaso pa anthu, Yeremiya anamudzudzula, kenako anafotokoza mmene anthuwo angadziwire mneneri woona. Pa nthawiyi, Yeremiya anaika goli lathabwa m’khosi mwake posonyeza kuti Aisiraeli akuyenera kupitiriza kugonjera Ababulo. Koma Hananiya anakwiya kwambiri ndi zimenezi ndipo anathyola golilo. N’kutheka kuti Hananiya akanathanso kuchita zinthu zina zoopsa kuposa pamenepa. Choncho, kodi Yeremiya anatani? Timawerenga kuti: “Yeremiya anachokapo.” Zoonadi, Yeremiya anaona kuti ndi bwino kungochokapo. Pambuyo pake, atauzidwa ndi Yehova, Yeremiya anapitanso kumalowo ndipo anakauza Hananiya zimene Mulungu adzachite. Anamuuza kuti Mulungu adzachititsa kuti Ayuda atengedwe ukapolo ndi mfumu ya ku Babulo komanso kuti Hananiyayo amwalire.—Yer. 28:1-17.
12 Nkhani youziridwayi ikusonyezeratu kuti ngakhale kuti tiyenera kukhala olimba mtima tikamalalikira, tiyeneranso kuchita zinthu mwanzeru. Mwachitsanzo, ngati panyumba ina munthu akukana kukambirana naye mfundo za m’Malemba ndipo wakwiya, komanso akuoneka kuti akufuna kuyamba zachiwawa, tiyenera kungotsanzika mwaulemu n’kupita panyumba ina. Sitiyenera kukangana ndi wina aliyense pa nkhani yokhudza uthenga wabwino wa Ufumu. Ndipotu tikakhala ‘ougwira mtima pokumana ndi zoipa,’ tingathe kudzathandiza munthu ameneyo pa nthawi ina zinthu zitasintha.—Werengani 2 Timoteyo 2:23-25; Miy. 17:14.
N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira kwambiri Yehova tikamalalikira uthenga wabwino? N’chifukwa chiyani tikamachita zinthu molimba mtima tiyenera kuchitanso zinthu mwanzeru?
“USACHITE MANTHA”
13. N’chifukwa chiyani Yehova anauza Yeremiya kuti: “Usachite mantha,” nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira nkhani imeneyi?
13 Anthu omwe ankalambira Mulungu m’njira yoyenerera anakhudzidwa ndi zinthu zoopsa zomwe zinkachitika Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa mu 607 B.C.E. Choncho, mungamvetse chifukwa chake Mulungu anauza Yeremiya kuti: “Usachite mantha.” (Yer. 1:8; Maliro 3:57) Ndipo Yehova anauza Yeremiya kuti auzenso anthu ake mawu olimbikitsawa. (Werengani Yeremiya 46:27.) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? M’nthawi yoopsa ya mapeto ino, nthawi zina tingachite mantha. Pa nthawi ngati zimenezo, kodi tidzamvera Yehova, yemwe akutiuza kuti: “Usachite mantha”? Taona kale m’buku lino mmene Mulungu anathandizira Yeremiya pa nthawi yoopsa kwambiriyo. Tsopano tiyeni tionenso mwachidule zomwe zinachitika, kuti tione zimene tingaphunzirepo.
14, 15. (a) Kodi Yeremiya anakumana ndi zinthu zotani zoopsa? (b) Kodi Yehova anakwaniritsa bwanji lonjezo lake lakuti adzateteza Yeremiya?
14 Pamene Ababulo anapitiriza kuzungulira mzinda wa Yerusalemu, njala inavuta kwambiri mumzindawo ndipo pasanapite nthawi yaitali, anthu ambiri chakudya chinawathera. (Yer. 37:21) Kuwonjezera pa vuto lanjalali, Yeremiya anaponyedwa m’chitsime chakuya kwambiri chamatope okhaokha, ndipo akanafera momwemo. Akalonga a ku Yuda anapempha Mfumu Zedekiya, yomwe inali yamantha, kuti Yeremiya aponyedwe m’chitsimechi, ndipo mfumuyo inalolera. Pamene Yeremiya ankamira m’matopemo, ankangoona kuti basi, afera momwemo. Kodi zinthu zimenezi zikanachitikira inuyo, simukanachita mantha?—Yer. 38:4-6.
15 Ngakhale kuti Yeremiya anali munthu ngati ife tomwe, iye anakhulupirira zimene Yehova anamuuza, zoti sadzamusiya. (Werengani Yeremiya 15:20, 21.) Kodi Yehova anathandizadi mneneri wake yemwe anali ndi chikhulupiriro cholimbayu? Tikudziwa kuti anamuthandizadi. Mulungu anachititsa Ebedi-meleki kuti achite zinthu motsutsana ndi akalonga aja, n’kukapulumutsa Yeremiya. Atapeza chilolezo kwa mfumu, Ebedi-meleki anatulutsa mneneriyo m’chitsime chakuya chamatopecho, n’kumupulumutsa ku imfa.—Yer. 38:7-13.
16. Kodi Yehova anapulumutsa atumiki ake okhulupirika ku zinthu zoopsa ziti?
16 Ngakhale kuti Yeremiya anatulutsidwa m’chitsime chamatopecho, sikuti mavuto anali atatha. Pochonderera Mfumu Zedekiya kuti Yeremiya atulutsidwe m’chitsimecho, Ebedi-meleki anati: “Afera momwemo chifukwa cha njala, pakuti mkate watheratu mumzindawu.” (Yer. 38:9) Chakudya chinkasowa kwambiri mu Yerusalemu moti anthu anayamba kudya nyama ya anthu anzawo. Koma kachiwirinso Yehova anapulumutsa mneneri wakeyu. Ndiponso Yeremiya anatsimikizira Ebedi-meleki kuti Yehova adzamuteteza. (Yer. 39:16-18) Yeremiya anali asanaiwale mawu olimbikitsa amene Mulungu anamuuza akuti: “Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.” (Yer. 1:8) Anthu awiri okhulupirikawa sakanaphedwa ndi adani kapena kufa ndi njala chifukwa chakuti Mulungu Wamphamvuyonse ankawateteza. Ndipo iwo anapulumukadi pamene anthu ambiri anafa mumzinda wa Yerusalemu. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Yehova analonjeza kuti adzateteza atumiki akewo ndipo anakwaniritsa lonjezo lake.—Yer. 40:1-4.
17. N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti adzateteza atumiki ake?
17 Ulosi wa Yesu wokhudza mapeto a nthawi ino ukukwaniritsidwa mofulumira kwambiri, ndipo posachedwapa ufika pachimake. Yesu ananena kuti “padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika, ndipo adzathedwa nzeru . . . Mwakuti anthu adzakomoka chifukwa cha mantha ndi kuyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu.” (Luka 21:25, 26) Tiyenera kuyembekezera kuti tione mmene zizindikiro zimenezi zidzaonekere komanso mmene anthu ambiri adzachitire mantha. Komabe kaya padzachitika zotani, musakayikire zoti Yehova adzateteza anthu ake ndipo akufunitsitsa kuchita zimenezi. Koma zimene zidzachitikire anthu oipa zidzakhala zosiyana kwambiri ndi zimenezi. (Werengani Yeremiya 8:20; 14:9.) Ngakhale atumiki a Mulungu ataoneka kuti alibiretu chiyembekezo chilichonse, ngati kuti ali m’chitsime chamdima komanso chamatope okhaokha, Mulungu adzawapulumutsa. Mawu amene Mulungu anauza Ebedi-meleki adzagwiranso ntchito pa anthu ake. Iye anati: “‘Ine ndidzakupulumutsa ndithu, ndipo sudzaphedwa ndi lupanga, koma udzapulumutsa moyo wako chifukwa chakuti wandikhulupirira,’ watero Yehova.”—Yer. 39:18.
MAWU AMENE ANALEMBEDWA KUTI AKUTHANDIZENI
18. (a) Kodi ndi mawu ati amene anasintha moyo wa Yeremiya? (b) Kodi lamulo la Mulungu lopezeka pa Yeremiya 1:7 lili ndi tanthauzo lotani kwa inu?
18 Mulungu analamula Yeremiya kuti: “Upite kwa anthu onse amene ndidzakutumako. Ndipo ukanene zonse zimene ndidzakulamula kuti ukanene.” (Yer. 1:7) Yeremiya atamva lamulo lochokera kwa Mulungu limeneli, moyo wake unasinthiratu. Kuyambira pa nthawi imeneyo, maganizo ake onse anali pa ntchito yolengeza “mawu a Yehova.” Mawu akuti “mawu a Yehova,” akupezeka mobwerezabwereza m’buku la Yeremiya. M’chaputala chomaliza, Yeremiya anafotokoza kuti mzinda wa Yerusalemu unawonongedwa, ndipo Zedekiya, mfumu yake yomaliza, anagwidwa n’kupititsidwa ku ukapolo. Zoonadi, Yeremiya anapitiriza kuphunzitsa ndi kulimbikitsa anthu a ku Yuda kuti azimvera Yehova, kufikira pamene zinali zoonekeratu kuti ntchito yake yatha.
19, 20. (a) N’chifukwa chiyani mungatengere mmene Yeremiya anachitira utumiki wake? (b) Kodi ntchito yolalikira imathandiza bwanji munthu kukhala wosangalala? (c) Kodi kuphunzira buku la Yeremiya ndi la Maliro kwakuthandizani bwanji?
19 Ntchito imene Yeremiya anapatsidwa imafanana m’njira zambiri ndi utumiki wa Mboni za Yehova masiku ano. Mofanana ndi Yeremiya, inunso mukutumikira Mulungu woona pa nthawi imene iye watsala pang’ono kupereka chiweruzo. Maudindo ena amene muli nawo amafuna nthawi komanso mphamvu zanu, komabe ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi yofunika kwambiri kuposa ntchito iliyonse imene mungagwire pa nthawi ino. Mukamagwira ntchito imeneyi, mumalemekeza dzina lalikulu la Mulungu komanso mumasonyeza kuti mukuvomereza kuti iye yekha ndiye woyeneradi kukhala Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. (Werengani Maliro 5:19.) Komanso mukamathandiza ena kudziwa Mulungu woona ndiponso zimene iye amafuna kuti iwo azichita n’cholinga choti adzapeze moyo wosatha, mumasonyeza kuti mumakonda kwambiri anthu enawo.—Yer. 25:3-6.
20 Pofotokoza za ntchito imene Mulungu anam’patsa, Yeremiya anati: “Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu wa makamu.” (Yer. 15:16) Masiku ano, anthu onse amene amalengeza ndi mtima wonse uthenga wochokera kwa Mulungu woona, amasangalala ngati mmene Yeremiya ankachitira. Choncho inuyo muli ndi chifukwa chabwino chopitirizira kulengeza uthenga wa Yehova ngati mmene Yeremiya anachitira.
Kodi chitsanzo cha Yeremiya ndi cha Ebedi-meleki chingakuthandizeni bwanji kukhala olimba mtima? Kodi mukufuna kutsanzira khalidwe liti la Yeremiya mukamalalikira?