Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 January tsamba 8
  • Tisamaiwale Kupempherera Akhristu Amene Akuzunzidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tisamaiwale Kupempherera Akhristu Amene Akuzunzidwa
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhani Zodalirika Komanso Zolimbitsa Chikhulupiriro
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Muzisangalala Mukamazunzidwa
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Ozunzidwa Komabe Achimwemwe
    Nsanja ya Olonda—2004
  • ‘Pemphereranani’
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 January tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tisamaiwale Kupempherera Akhristu Amene Akuzunzidwa

Baibulo linaneneratu kuti Satana adzatizunza n’cholinga choti asokoneze utumiki wathu. (Yoh. 15:20; Chiv. 12:17) Kodi tingathandize bwanji Akhristu anzathu amene akuzunzidwa m’mayiko ena? Tikhoza kumawapempherera. Paja “pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”—Yak. 5:16.

M’bale wina akuikidwa m’ndende atamangidwa ndi maunyolo; abale ndi alongo; m’bale wina akupemphera

Kodi tinganene chiyani m’mapemphero athu? Tikhoza kupempha Yehova kuti athandize abale ndi alongo athu kuti akhale olimba mtima. (Yes. 41:10-13) Tikhozanso kupemphera kuti akuluakulu a boma asachite chilichonse chosokoneza ntchito yathu yolalikira n’cholinga choti “tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere.”—1 Tim. 2:1, 2.

Pa nthawi imene Paulo ndi Petulo ankazunzidwa, Akhristu anzawo ankawatchula mayina powapempherera. (Mac. 12:5; Aroma 15:30, 31) Ngakhale kuti sitikudziwa mayina a anthu onse amene akuzunzidwa, tikhoza kutchula mpingo wawo, dziko lawo kapena dera lawo powapempherera.

  • Tikhoza kudziwa a Mboni za Yehova anzathu amene akuzunzidwa tikapita pa jw.org/ny. (Pitani pamene palembedwa kuti MALO A NKHANI > ZOKHUDZANA NDI MALAMULO.)

  • Nkhani ya pa jw.org yakuti “Mayiko Amene a Mboni za Yehova Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira” imasonyeza chiwerengero cha a Mboni amene ali m’ndende m’dziko lililonse. (Pitani pamene palembedwa kuti MALO A NKHANI > ZOKHUDZANA NDI MALAMULO.) Dinani padziko linalake kuti mudziwe zambiri zimene zikuchitika m’dzikolo komanso kuti muone mayina a anthu amene ali m’ndende.)

Lembani madera amene kuli Akhristu amene akuzunzidwa omwe mukufuna kumawapempherera

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena